Muzithandizana mu Utumiki
1. Kodi kuyenda ndi mnzathu tikamagwira ntchito yolalikira kuli ndi ubwino wotani?
1 Panthawi ina, Yesu anatumiza ophunzira ake 70, kuti akagwire ntchito yolalikira ndipo ‘anawatumiza awiriawiri.’ (Luka 10:1) N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinathandiza kuti ophunzirawo azithandizana ndiponso azilimbikitsana akamagwira ntchito yolalikirayo. Nanga ifeyo tikayenda ndi wofalitsa wina mu utumiki, kodi tingatani kuti tizithandizana?
2. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mukumvetsera pamene mnzanu akulalikira, ndipo n’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezo?
2 Muzimvetsera: Muzimvetsera mwachidwi mnzanu yemwe mwayenda nayeyo akamalalikira. (Yak. 1:19) Akamawerenga lemba, inunso muziwerenga m’Baibulo lanu. Muziyang’ananso munthu yemwe akulankhula, kaya ndi mnzanuyo kapena munthu yemwe mukumulalikirayo. Mwininyumba akaona kuti inuyo mukumvetsera mwachidwi, nayenso angayambe kumvetsera mwachidwi.
3. Kodi ndi nthawi iti imene mnzathu angatipemphe kuti tiyankhulepo?
3 Muzizindikira Nthawi Yoyenera Kulankhula: Ngati tayenda ndi mnzathu mu utumiki ndipo iyeyo akulalikira munthu wina, tingasonyeze kuti tikumulemekeza ngati tingam’patse mpata woti iyeyo akambirane ndi munthuyo. (Aroma 12:10) Tiyenera kupewa kumudula mawu. Ngati waiwala mfundo inayake kapena mwininyumba wafunsa funso ndipo mnzathuyo watipempha kuti timuthandize, tiyenera kuyesetsa kuyankha mfundo zogwirizana ndi nkhani imene akulalikira, osati kuyambitsa nkhani ina yosagwirizana n’komwe. (Miy. 16:23; Mlal. 3:1, 7) Ngati tapatsidwa mpata wolankhula, tizionetsetsa kuti zoyankhula zathu zikugwirizana ndi ulaliki wa mnzathuyo.—1 Akor. 14:8.
4. N’chiyani chimene chingatithandize kuti tizikhala achimwemwe komanso zinthu zizitiyendera bwino mu utumiki?
4 Ophunzira 70 aja atamaliza kulalikira, “anabwerera ali achimwemwe.” (Luka 10:17) Ifenso zinthu zingatiyendere bwino mu utumiki ndiponso tingakhale ndi chimwemwe ngati tingamamvetsere ndiponso kuzindikira nthawi yoyenera kuyankhulapo mnzathu akamayankhula ndi mwininyumba.