Ndandanda ya Mlungu wa March 29
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 29
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 5 ndime 1-6 ndi mabokosi a patsamba 52 ndi 55
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 14-15
Na. 1: 1 Samueli 14:24-35
Na. 2: Njira Zimene Tingayandikirire kwa Yehova (Yak. 4:8)
Na. 3: Kodi Anzeru a Kummawa, Kapena Kuti Amagi, Amene Nyenyezi Inawatsogolera kwa Yesu Anali Ndani? (rs tsa. 240 ndime 2-4)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo. Lengezani tsiku lotsatira loyambitsa maphunziro a Baibulo. Funsani wofalitsa amene anakwanitsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo panthawi imeneyi ndipo akuwachititsabe. Ndi nkhani ziti zimene iye waona kuti zikugwira mtima anthu a m’gawolo ndipo zikuthandiza kuyambitsa maphunziro? Kodi iye saiwala mfundo iti pochita maulendo obwereza? M’pempheni kuti achite chitsanzo pankhani imodzi mwa nkhani zimene iye waona kuti zikuthandiza kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Ikambidwe ndi mkulu woyenera.
Mph. 10: “Muzithandizana mu Utumiki.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.