Ndandanda ya Mlungu wa March 22
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 22
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv Zakumapeto, kuyambira pamutu wa patsamba 209 mpaka 212
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 10-13
Na. 1: 1 Samueli 10:17-27
Na. 2: Kodi Khirisimasi Ndi Chikondwerero Chogwirizana ndi Baibulo? (rs tsa. 239 ndime 2 mpaka tsa. 240 ndime 1)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akhristu Sayenera Kukhulupirira Mfundo Yoti Zamoyo Zinachita Kusanduka?
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Phatikizanipo zilengezo zilizonse zomaliza zokhudza Chikumbutso.
Mph. 15: Kukonzekera Kugawira Magazini Yapadera ya Nsanja ya Olonda ya April 1. Fotokozani mfundo za m’magaziniyi. Funsani omvera kuti anene funso ndiponso lemba limene akonzekera kugwiritsa ntchito pogawira magaziniyi. Chitani zitsanzo ziwiri.
Mph. 15: Thandizani Anthu Achidwi Kuti Adzapezeke pa Chikumbutso. Ikambidwe ndi mkulu. Kumbutsani ofalitsa kuti ali ndi udindo wothandiza anthu omwe akuphunzira Baibulo, ofalitsa amene anasiya kulalikira, ndiponso anthu ena kuti adzapezeke pamwambowu. (Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2008, patsamba 8.) Chitani chitsanzo chachidule. Kumbutsani omvera kuti azitsatira pulogalamu ya Kuwerenga Baibulo kwa panyengo ya Chikumbutso.