Ntchito Yofunika Kwambiri Kuposa Zonse
1. Kodi tingadzipereke kuchita chiyani ngati timakonda kwambiri utumiki?
1 N’chifukwa chiyani nthawi zonse timalimbikitsidwa kuti tizithera nthawi yathu, mphamvu zathu ndiponso tizigwiritsa ntchito chuma chathu mu utumiki? N’chifukwa chakuti palibe ntchito ina yofunika kwambiri kuposa imeneyi. Kuganizira kufunika kwa ntchito imeneyi kumatilimbikitsa kukhala ndi mtima wogwira nawo ntchitoyi yomwe sidzachitikanso.—Mac. 20:24.
2. Kodi ntchito yathu yolalikira imathandiza bwanji kuyeretsa dzina lalikulu la Yehova?
2 Ntchitoyi Imayeretsa Dzina la Yehova: Ntchito yolalikira imatsindika mfundo yakuti Ufumu wa Yehova, womwe Khristu Yesu ndiye wolamulira wake, udzachotsa maboma onse a anthu ndiponso udzathetsa mavuto onse. (Mat. 6:9, 10) Imathandizanso kuti Yehova azilemekezedwa chifukwa ndi iye yekha amene adzathetse matenda ndi imfa. (Yes. 25:8; 33:24) Popeza timadziwika ndi dzina lake, anthu ena angamalemekeze Mulungu poona changu ndiponso khalidwe lathu labwino. (1 Pet. 2:12) N’zosangalatsa kwambiri kudziwikitsa dzina la Ambuye Mfumu Yehova padziko lonse lapansi.—Sal. 83:18.
3. Kodi anthu amene amamvetsera uthenga wa Ufumu amakhala ndi madalitso otani?
3 Imapulumutsa Moyo: Yehova “safuna kuti wina akawonongeke, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Komabe, popanda munthu wolalikira, kodi anthu angadziwe bwanji zimene Yehova amati n’zoyenera kapena zosayenera? (Yona 4:11; Aroma 10:13-15) Anthu akamvera uthenga wabwino n’kusiya makhalidwe oipa, moyo wawo umasintha. (Mika 4:1-4) Komanso amakhala ndi chiyembekezo chodzalandira moyo wosatha. Kugwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa mwachangu kumathandiza kuti ifeyo ndiponso anthu amene amatimvetsera tidzapulumuke. (1 Tim. 4:16) Tilitu ndi mwayi waukulu wogwira nawo ntchito yofunika kwambiri kuposa zonse imeneyi.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwira mwakhama ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira?
4 Posachedwapa chisautso chachikulu chithetsa mwadzidzidzi dziko lopanda chilungamo limene lilipoli. Anthu amene amalambira Yehova adzapulumuka. N’chifukwa chake ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira ndi yofunika kwambiri ndipo ndi yothandiza komanso yofunika kuigwira mwachangu kuposa ntchito zonse. Choncho, tiyeni tiziika ntchito imeneyi pamalo oyamba m’moyo wathu.—Mat. 6:33.