Kudziŵikitsa Dzina la Mulungu
1. Kodi kuphunzira dzina la Mulungu kungakhudze bwanji anthu?
1 Kodi munatani mutaphunzira dzina la Mulungu? Anthu ambiri amachita zimene anachita mayi wina amene anati: “Nditaona dzina la Mulungu m’Baibulo nthaŵi yoyamba, ndinalira. Ndinasangalala kwambiri nditazindikira kuti ndadziŵadi dzina lenileni la Mulungu ndiponso kuti ndikhoza kuligwiritsa ntchito.” Kuphunzira dzina la Mulungu kunali kofunika kwambiri kwa mayiyu kuti am’dziŵe Yehova monga munthu ndiponso kuti apange naye ubwenzi.
2. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti tiziphunzitsa ena za Yehova?
2 N’chifukwa Chiyani Tifunika Kulidziŵikitsa? Kudziŵa dzina la Mulungu kumaphatikizapo kudziŵa makhalidwe ake, zolinga zake ndi zochita zake. Kumayendera limodzinso ndi chipulumutso. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye [“Yehova,” NW] adzapulumuka.” Ndiyeno Paulo anafunsa kuti: “Iwo adzaitana bwanji pa iye,” ngati sanaphunzire kaye za Yehova ndi kumukhulupirira? N’chifukwa chake, n’kofunika kwambiri kwa Akristu kudziŵitsa ena dzina la Mulungu ndi zonse zimene dzinalo limaimira. (Aroma 10:13, 14) Komabe, pali chifukwa china chachikulu kwambiri chodziŵikitsira dzina la Mulungu.
3. Kodi timalalikira pa chifukwa chachikulu chiti?
3 Cha mu 1920, anthu a Mulungu anazindikira m’Malemba nkhani yokhudza anthu onse yotsimikizira kuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira ndiponso yoyeretsa dzina lake. Yehova asanawononge anthu oipa kuti achotse chitonzo chimene chili pa dzina lake, choonadi cha iye chiyenera ‘kudziŵika m’dziko lonse.’ (Yes. 12:4, 5; Ezek. 38:23) Choncho, chifukwa chachikulu chimene timalalikirira ndicho kutamanda Yehova pamaso pa anthu ndi kuyeretsa dzina lake kwa anthu onse. (Aheb. 13:15) Kukonda Mulungu ndi anzathu kudzatilimbikitsa kuchita mokwanira ntchito imene Mulungu watipatsayi.
4. Kodi Mboni za Yehova zimadziŵika bwanji ndi dzina la Mulungu?
4 “Anthu a Dzina Lake”: Mu 1931 tinalandira dzina lakuti Mboni za Yehova. (Yes. 43:10) Kuyambira nthaŵi imeneyo, anthu a Mulungu adziŵikitsa dzina la Mulungu ndipo buku la Proclaimers, patsamba 124, limati: “Padziko lonse lapansi, aliyense amene amagwiritsa ntchito momasuka dzina lakuti Yehova amadziwikiratu kuti ndi mmodzi wa Mboni za Yehova.” Kodi inu mumadziŵika choncho? Kuyamikira ubwino wa Yehova kuyenera kutilimbikitsa ‘kulemekeza dzina lake,’ kulankhula za iye nthaŵi iliyonse yoyenera.—Sal. 20:7; 145:1, 2, 7.
5. Kodi kudziŵika ndi dzina la Mulungu kumakhudza bwanji khalidwe lathu?
5 Monga “anthu a dzina lake,” tiyenera kutsatira miyezo yake. (Mac. 15:14; 2 Tim. 2:19) Nthaŵi zambiri chimene anthu amayambira kuona kwa Mboni za Yehova ndi khalidwe lawo labwino. (1 Pet. 2:12) Sitikufuna kuipitsa dzina lake mwa kunyalanyaza mfundo za Mulungu kapena kuona kulambira kwake kukhala kosafunika kwenikweni pamoyo wathu. (Lev. 22:31, 32; Mal. 1:6-8, 12-14) M’malo mwake, moyo wathu uzisonyezatu kuti timayamikira mwayi wodziŵika ndi dzina la Mulungu.
6. Kodi ndi mwayi wotani umene tili nawo masiku ano ndiponso umene tidzakhala nawo nthaŵi zonse?
6 Masiku ano, timaona kukwaniritsidwa kwa zimene Yehova ananena kuti: “Kuyambira kotulukira dzuŵa kufikira koloŵera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu.” (Mal. 1:11) Tiyeni tipitirize kudziŵikitsa choonadi cha Yehova ndi ‘kulemekeza dzina lake loyera ku nthaŵi za nthaŵi.’—Sal. 145:21.