Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/10 tsamba 2-3
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 3/10 tsamba 2-3

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Okondedwa Anzathu a Mboni za Yehova:

Ndife anthu a mwayi kwambiri kudziwika ndi dzina la Yehova, yemwe ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. Dzina limeneli ndi losatha komanso sitingaliyerekezere ndi dzina lina lililonse. Yehova ndi amene watipatsa dzina limeneli ndipo takhala tikudziwika ndi dzina lapaderali makamaka kuyambira m’chaka cha 1931. (Yes. 43:10) Timanyadira kwambiri kudziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova.

Mdyerekezi akuyesetsa kuti afafanize dzina la Mulungu ndipo maboma a anthu, omwe mtsogoleri wawo ndi Satana, amanyoza dzina la Yehova. Nayenso Babulo Wamkulu, yemwe ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga, amadana ndi dzina la Mulungu ndipo walichotsa m’Mabaibulo ambiri. Koma mosiyana ndi zimenezi, Yesu ankalemekeza dzina la Atate wake ndipo m’pemphero lake lachitsanzo limene anaphunzitsa otsatira ake, iye anatchula dzinali koyambirira. Iye anati: “Muzipemphera motere: ‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’” (Mat. 6:9) Kenako iye anapemphera kwa Atate wake mochokera pansi pamtima kuti: “Dzina lanu ndalidziwitsa kwa anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine.” (Yoh. 17:6) Potsatira chitsanzo cha Yesu, tatsimikiza kuposa kale kuti tidzalimbikira kulengeza dzina la Yehova padziko lonse.

Lemba la chaka chatha lakuti: “Kuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino,” linatilimbikitsa kukwaniritsa utumiki wathu. (Mac. 20:24) N’zosakaikitsa kuti Yehova wadalitsa kwambiri khama lathu m’chaka cha utumiki chapitachi. Ntchito yaikulu yochitira umboni yachitika padziko lonse ndipo zimenezi zachititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe. M’chakachi, chiwerengero chatsopano cha ofalitsa chinafika 7,313,173 ndipo onsewa anagwira nawo ntchito yolalikira kwa anthu onse komanso kuphunzitsa anthu a mitima yabwino, omwe akufunafuna njira zothetsera mavuto amene akukumana nawo tsiku ndi tsiku. Anthu okwana 18,168,323 anapezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Khristu ndipo zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambiri akhoza kuyamba kuitanira padzina la Yehova dongosolo loipali lisanawonongedwe.

Yehova akalola, tipitirizabe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mwakhama kwambiri ndipo tiyesetsa kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti tilalikire anthu a m’gawo lathu. (Mat. 24:14; Maliko 13:10) Kaya tikulalikira khomo ndi khomo, mumsewu, polemba makalata kapena kulalikira patelefoni kapenanso tikulalikira mwamwayi, tiyeni tiyesetse kudziwitsa anthu ambiri dzina la Yehova ndiponso cholinga chake.

Sitikuika kuti posachedwapa Yehova achita zinthu zomwe ziyeretse dzina lake. (Ezek. 36:23) Nthawi yatsala pang’ono kwambiri yoti anthu onse omwe akunyoza dzina la Yehova awonongedwe. Lidzakhala tsiku losangalatsa kwambiri kwa atumiki okhulupirika onse a Yehova omwe akuuza ena dzina la Yehova ndiponso omwe akhala kumbali ya ulamuliro wake wachilengedwe chonse.

Chikondi cha Yehova pa anthu ake chinaonekera kwambiri pamisonkhano yachigawo komanso yamayiko ya 2009 yakuti: “Khalani Maso.” Misonkhanoyi ndi yosaiwalika pa mbiri ya atumiki a Yehova ndipo inatilimbikitsa kuti tizikumbukira kufunika kokhala maso pomwe tikuyembekeza tsiku la Yehova.—Maliko 13:37; 1 Ates. 5:1, 2, 4.

Kunena zoona, Yehova amatikonda kwambiri ndipo amafuna kuti tizikhala osangalala. Iye amatigonetsa kubusa lamsipu ndipo amatitsogolera kumadzi odikha.—Sal. 23:1, 2; 100:2, 5.

Yehova apitirize kukudalitsani pamene mukupitiriza kuchita utumiki mwakhama kwambiri m’miyezi ikubwerayi.

Landirani moni wathu wachikondi chachikhristu,

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena