Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 March tsamba 14-19
  • Muzilalikira Mwakhama Ngati Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzilalikira Mwakhama Ngati Yesu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ANKAGANIZIRA ZIMENE YEHOVA AMAFUNA
  • ANKACHITA CHIDWI NDI MAULOSI A M’BAIBULO
  • ANKADALIRA YEHOVA KUTI AZIMUTHANDIZA
  • ANKAKHULUPIRIRA KUTI ANTHU ENA ADZAMVETSERA
  • Zimene Tingachite Kuti Tizisangalala Kwambiri Tikamalalikira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Chikondi Chizikulimbikitsani Kuti Mupitirize Kulalikira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 March tsamba 14-19

NKHANI YOPHUNZIRA 11

NYIMBO NA. 57 Tizilalikira Anthu a Mitundu Yonse

Muzilalikira Mwakhama Ngati Yesu

‘Ambuye . . . anawatumiza awiriawiri kuti atsogole kupita mumzinda ndi malo alionse kumene iye ankafunika kudzapitako.’​—LUKA 10:1.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi, tikambirana njira 4 zosonyeza mmene tingatsanzirire Yesu pogwira mwakhama ntchito yolalikira.

1. Kodi ndi chinthu chimodzi chiti chomwe chimasiyanitsa atumiki a Yehova ndi anthu ena?

CHINTHU chimodzi chomwe chimasiyanitsa atumiki a Yehova ndi anthu ena omwe amati ndi Akhristu, ndi khamaa limene amachita pa ntchito yolalikira. (Tito 2:14) Nthawi zina mungamaone kuti ntchito yolalikira sikukusangalatsani. Mwina mungamamve ngati mmene amamvera mkulu wina yemwe ndi wakhama. Iye anati: “Nthawi zina ndimangoona kuti sindikufuna kulalikira.”

2. Kodi ndi zinthu ziti zomwe nthawi zina zingachititse kuti tisamasangalale ndi ntchito yolalikira?

2 Mwina mungamasangalale kuchita mautumiki ena kusiyana ndi kugwira ntchito yolalikira. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa tikamagwira nawo ntchito yomanga ndi kukonza nyumba za gulu, kugwira nawo ntchito yopereka thandizo pakachitika ngozi komanso kulimbikitsa abale, tingamaone mwamsanga zotsatirapo zake. Timaona mtendere ndi chikondi tikamagwira ntchito ndi abale athu ndipo timadziwa kuti akuyamikira zimene tikuchita. Pomwe nthawi zina tingakhale tikulalikira gawo lomwelomwelo kwa zaka zambiri koma osapeza anthu achidwi. Kapenanso tingamakumane ndi anthu omwe amakana uthenga wathu. Timadziwanso kuti pamene mapeto akuyandikira anthu ambiri azitsutsa uthenga wathu. (Mat. 10:22) Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipitirize kukonda ntchito yolalikira komanso kumaigwira mwakhama?

3. Kodi lemba la Luka 13:6-9, likusonyeza bwanji khama limene Yesu anachita?

3 Kuganizira chitsanzo cha Yesu kungatithandize kuti tizichita khama pa ntchito yolalikira. Ali padziko lapansi iye sanasiyepo kugwira mwakhama ntchitoyi. Ndipotu anapitiriza kuchita khama mpaka kumapeto kwa utumiki wake. (Werengani Luka 13:6-9.) Yesu anali ngati wosamalira munda wa mpesa amene ankasamalira mtengo wa mkuyu kwa zaka zitatu koma sunkabala zipatso. Yesu analalikira kwa Ayuda kwa zaka pafupifupi zitatu ndipo ambiri mwa iwo sankamvetsera uthenga wake. Komabe Yesu sanasiye kuwalalikira. Iye anachita mofanana ndi wosamalira munda uja yemwe sanasiye kusamalira mtengowo, akumayembekezera kuti udzabereka. Yesu anawonjezera kuchita khama pofuna kuwathandiza Ayudawo kuti akhulupirire uthenga wabwino.

4. Kodi ndi zinthu 4 ziti zomwe tingaphunzire kwa Yesu?

4 Munkhaniyi tikambirana mmene Yesu anasonyezera khama makamaka pa miyezi 6 yomalizira ya utumiki wake. Kukambirana zimene anaphunzitsa komanso kuchita, kungatithandize kuti nafenso tipitirize kuchita khama masiku ano. Tiona mmene tingamutsanzirire m’mbali 4 izi: (1) Iye ankaganizira kwambiri zochita chifuniro cha Yehova, (2) ankachita chidwi ndi maulosi, (3) ankadalira Yehova kuti azimuthandiza, ndipo (4) ankakhulupirira kuti anthu ena amumvetsera.

ANKAGANIZIRA ZIMENE YEHOVA AMAFUNA

5. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti kuchita chifuniro cha Mulungu n’kofunika?

5 Yesu ankalalikira mwakhama “uthenga wabwino wa Ufumu” chifukwa ankadziwa kuti ndi zimene Mulungu ankafuna kuti iye achite. (Luka 4:43) Yesu ankaona kuti ntchito yolalikira inali yofunika kwambiri pa moyo wake. Ngakhale chakumapeto kwa utumiki wake, iye ankayenda “mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi” kuphunzitsa anthu. (Luka 13:22) Anaphunzitsanso ophunzira ambiri kuti azigwira nawo ntchito yolalikira.​—Luka 10:1.

6. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kulalikira ndi ntchito zina zomwe zimachitika m’gululi? (Onaninso chithunzi.)

6 Masiku anonso kulalikira uthenga wabwino ndi ntchito yaikulu imene Yehova ndi Yesu amafuna kuti tizigwira. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Pali kugwirizana pakati pa ntchito yolalikira ndi mautumiki ena m’gulu la Mulungu. Mwachitsanzo, timamanga nyumba za gulu kapena kutumikira pa Beteli pothandiza pa ntchito yolalikira. Timagwira nawo ntchito yopereka thandizo kwa abale ndi alongo pakachitika ngozi pofuna kuwathandiza kuti ayambirenso kuchita zinthu zokhudza kulambira zomwe zikuphatikizapo kugwira ntchito yolalikira. Tikazindikira kufunika kwa ntchito yolalikira komanso kukumbukira kuti ndi ntchito yaikulu imene Yehova amafuna kuti tizigwira, tidzalimbikitsidwa kugwira nawo ntchitoyi nthawi zonse. Mkulu wina wa ku Hungary dzina lake János, ananena kuti: “Ndimadzikumbutsa kuti palibe ntchito ina iliyonse m’gululi yomwe ingalowe m’malo mwa ntchito yolalikira komanso kuti ntchitoyi ndi yofunika kwambiri.”

Zithunzi: 1. M’bale akugwira ntchito pamalo a zomangamanga. 2. M’bale wina akuthandiza ntchito za pa Beteli ali kunyumba kwake. 3. Pambuyo pake abale aja akulalikira limodzi.

Masiku ano kulalikira uthenga wabwino ndi ntchito yaikulu imene Yehova ndi Yesu amafuna kuti tizigwira (Onani ndime 6)


7. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizipitiriza kulalikira? (1 Timoteyo 2:3, 4)

7 Tingapitirize kuchita khama pa utumiki wathu tikamaona anthu ngati mmene Yehova amawaonera. Iye amafuna kuti anthu ambiri amve uthenga wabwino n’kukhala atumiki ake. (Werengani 1 Timoteyo 2:3, 4.) Choncho amatiphunzitsa mmene tingagwirire bwino ntchito yopulumutsa moyoyi. Mwachitsanzo, kabuku kakuti Muzikonda anthu​—Muziwaphunzitsa kamatipatsa malangizo abwino omwe angatithandize kuti tizikambirana ndi anthu n’cholinga chowathandiza kuti akhale ophunzira a Yesu. Ngakhale anthu asamvetsere uthenga wathu panopo, mwina angadzakhale ndi mwayi wophunzira za Yehova mkati mwa chisautso chachikulu mapeto asanafike. Mwina angadzakumbukire zimene tingawauze panopa n’kuyamba kufuna kutumikira Yehova. Koma zimenezo zingatheke ngati titapitiriza kulalikira.

ANKACHITA CHIDWI NDI MAULOSI A M’BAIBULO

8. Kodi kudziwa maulosi kunathandiza bwanji Yesu kudziwa mmene angagwiritsire bwino nthawi yake?

8 Yesu ankadziwa mmene maulosi a m’Baibulo adzakwaniritsidwire. (Dan. 9:26, 27) Iye ankadziwa kuti adzangochita utumiki wake kwa zaka zitatu ndi hafu. (Luka 18:31-34) Ankadziwanso zimene maulosi ananena zokhudza mmene adzafere komanso nthawi yake. Zimenezi zinamuthandiza kuti agwiritse ntchito bwino nthawi yake. Choncho ankalalikira mwakhama n’cholinga choti amalize ntchito imene anapatsidwa.

9. Kodi maulosi a m’Baibulo amatilimbikitsa bwanji kuti tizilalikira mwakhama?

9 Kumvetsa maulosi a m’Baibulo kungatithandize kuti tizilalikira mwakhama. Timadziwa kuti zochitika komanso khalidwe la anthu masiku ano ndi zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika m’masiku otsiriza. Timadziwanso kuti kukankhanakankhana komwe kulipo pakati pa ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America komanso dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nawo, kukukwaniritsa ulosi wonena za mfumu yakumpoto ndi mfumu yakumwera “m’nthawi yamapeto.” (Dan. 11:40) Timamvetsanso kuti ulamuliro wa Britain ndi America umaimiridwa ndi mapazi a chifaniziro chotchulidwa pa Danieli 2:43-45. Sitikayikira kuti monga mmene ulosiwo umafotokozera, posachedwapa Ufumu wa Mulungu uwononga maboma a anthu. Maulosi onsewa amatithandiza kudziwa nthawi yomwe tili ndipo amatilimbikitsa kuti tizilalikira mwakhama.

10. Kodi maulosi a m’Baibulo angatilimbikitse m’njira zina ziti kuti tizilalikira mwakhama?

10 Maulosi a m’Baibulo alinso ndi uthenga umene timafunitsitsa kuuza anthu ena. Mlongo wina wa ku Dominican Republic, dzina lake Carrie, ananena kuti: “Malonjezo osangalatsa a Yehova onena za tsogolo labwino amandilimbikitsa kuti ndiziuza ena uthenga wabwino.” Iye anawonjezeranso kuti: “Ndikamaona mavuto omwe anthu amakumana nawo masiku ano ndimazindikira kuti malonjezowa sakukhudza ine ndekha, koma akukhudzanso iwowo.” Maulosi a m’Baibulo amatilimbikitsa kuti tizipitirizabe kugwira ntchito yolalikira chifukwa timadziwa kuti Yehova ndi amene amatithandiza. Leila, yemwe amakhala ku Hungary ananena kuti: “Lemba la Yesaya 11:6-9 limandilimbikitsa kuti ndizilalikira uthenga wabwino ngakhale kwa anthu amene akuoneka ngati sangamvetsere. Ndimadziwa kuti aliyense angathe kusintha ngati atathandizidwa ndi Yehova.” M’bale wina wa ku Zambia, dzina lake Christopher, ananena kuti: “Mogwirizana ndi lemba la Maliko 13:10, uthenga wabwino ukulalikidwa padziko lonse ndipo ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kukwaniritsa nawo ulosi wa palembali.” Kodi ndi maulosi a m’Baibulo ati amene amakulimbikitsani inuyo kuti mupitirize kulalikira?

ANKADALIRA YEHOVA KUTI AZIMUTHANDIZA

11. N’chifukwa chiyani Yesu ankafunika kudalira Yehova kuti apitirize kulalikira mwakhama? (Luka 12:49, 53)

11 Yesu ankadalira Yehova kuti azimuthandiza kuti apitirize kulalikira mwakhama. Ngakhale kuti Yesu anali waluso, ankadziwa kuti uthenga wabwino wa Ufumu udzakwiyitsa anthu komanso kuwachititsa kuti azimutsutsa kwambiri. (Werengani Luka 12:49, 53.) Choncho chifukwa chakuti ankagwira ntchito yolalikira, atsogoleri achipembedzo ankadana naye ndipo mobwerezabwereza ankafuna kumupha. (Yoh. 8:59; 10:31, 39) Komabe iye ankapitiriza kulalikira chifukwa ankadziwa kuti Yehova anali naye. Yesu anati: “Iye sanandisiye ndekha chifukwa ndimachita zinthu zimene zimamusangalatsa nthawi zonse.”​—Yoh. 8:16, 29.

12. Kodi Yesu anakonzekeretsa bwanji ophunzira ake kuti azipitirizabe kulalikira ngakhale pamene akutsutsidwa?

12 Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti azidalira Yehova kuti aziwathandiza. Mobwerezabwereza, iye anawatsimikizira kuti Yehova adzawathandiza ngakhale pamene akuzunzidwa. (Mat. 10:18-20; Luka 12:11, 12) Choncho anawalimbikitsa kuti azikhala osamala. (Mat. 10:16; Luka 10:3) Anawalangiza kuti asamakakamize anthu omwe sankafuna kumvetsera. (Luka 10:10, 11) Anawauzanso kuti azithawa akamazunzidwa. (Mat. 10:23) Ngakhale kuti Yesu anali wakhama komanso ankadalira Yehova, sankachita dala zinthu zimene zingaike moyo wake pangozi.​—Yoh. 11:53, 54.

13. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatithandiza?

13 Masiku ano timafunikiranso kuti Yehova azitithandiza kuti tizilalikira mwakhama ngakhale tikutsutsidwa. (Chiv. 12:17) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatithandiza? Taganizirani pemphero la Yesu lomwe limapezeka mu Yohane chaputala 17. Yesu anapempha Yehova kuti aziyang’anira atumwi ake, ndipo Yehova anayankha pempheroli. Buku la Machitidwe limafotokoza mmene Yehova anathandizira atumwi kuti azilalikira mwakhama ngakhale pamene ankazunzidwa. M’pemphero lake, Yesu anapemphanso Yehova kuti aziyang’anira anthu omwe angakhulupirire uthenga womwe atumwi ankalalikira. Anthu amenewa akuphatikizapo inuyo. Yehova sanasiye kuyankha pemphero la Yesu. Iye adzakuthandizani inuyo ngati mmene anathandizira atumwi.​—Yoh. 17:11, 15, 20.

14. Kodi timadziwa bwanji kuti tingathe kupitirizabe kulalikira mwakhama? (Onaninso chithunzi.)

14 Pamene mapeto akuyandikira, nthawi zina zizikhala zovuta kulalikira uthenga wabwino mwakhama. Ngakhale zili choncho, tingapeze thandizo lomwe timafunikira. (Luka 21:12-15) Mofanana ndi Yesu ndi ophunzira ake, timalola anthu kusankha okha ngati akufuna kumvetsera kapena ayi ndipo timapewa kukangana nawo. Ngakhale m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa abale athu amapitirizabe kulalikira uthenga wabwino chifukwa amadalira Yehova osati mphamvu zawo. Mofanana ndi mmene Yehova anaperekera mphamvu kwa atumiki ake m’nthawi ya atumwi, masiku anonso amatipatsa mphamvu kuti ntchito yolalikira ichitike mokwanira mogwirizana ndi zimene iye akufuna. (2 Tim. 4:17) Choncho simuyenera kukayikira kuti mukamadalira Yehova mudzapitirizabe kulalikira mwakhama.

Ngakhale pamene ntchito yathu yaletsedwa, ofalitsa akhama amayesetsa kupeza njira zoti azilalikirabe (Onani ndime 14)b


ANKAKHULUPIRIRA KUTI ANTHU ENA ADZAMVETSERA

15. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankakhulupirira kuti anthu angamvetsere uthenga wake?

15 Yesu sankakayikira kuti anthu ena adzamvetsera uthenga wabwino. Zimenezi zinamuthandiza kuti azisangalala ndi utumiki wake. Mwachitsanzo, chakumapeto kwa chaka cha 30 C.E., Yesu anaona kuti anthu ambiri anali okonzeka kumvetsera uthenga wabwino ndipo anawayerekezera ndi munda umene mbewu zake zakhwima. (Yoh. 4:35) Patangopita chaka chimodzi iye anauza ophunzira ake kuti: “Pali zinthu zambiri zofunika kukolola.” (Mat. 9:37, 38) Pasanapite nthawi yaitali anabwerezanso kuti: “Pali zinthu zambiri zofunika kukolola . . . pemphani Mwiniwake wa munda kuti atumize antchito kukakolola.” (Luka 10:2) Yesu sanasiye kukhulupirira kuti anthu amvetsera uthenga wabwino ndipo ankasangalala iwo akachita zimenezo.​—Luka 10:21.

16. Kodi mafanizo a Yesu anasonyeza bwanji kuti anthu ena adzamvetsera uthenga wabwino? (Luka 13:18-21) (Onaninso chithunzi.)

16 Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azionabe uthenga umene ankalalikira kukhala wofunika. Zimenezi zikanawalimbikitsa kuti apitirize kuchita khama. Mwachitsanzo, tiyeni tione mafanizo awiri omwe anawafotokoza. (Werengani Luka 13:18-21.) Yesu anagwiritsa ntchito kanjere ka mpiru pofuna kuphunzitsa kuti uthenga wa Ufumu udzafalikira modabwitsa ndipo palibe chidzalepheretse zimenezo. Komanso anagwiritsa ntchito chofufumitsa posonyeza mmene uthenga wa Ufumu udzafalikirire ndi kuthandiza anthu kuti asinthe, ngakhale kuti kusinthako sikungaonekere mwamsanga. Apa Yesu anathandiza ophunzira ake kudziwa kuti uthenga umene ankalalikira udzathandiza anthu ambiri.

Alongo awiri achita ulaliki wa pashelefu kumalo opezeka anthu ambiri. Anthu ambiri akungodutsa osaimapo.

Mofanana ndi Yesu timakhulupirira kuti anthu ena adzamvetsera uthenga wabwino (Onani ndime 16)


17. Kodi tili ndi zifukwa ziti zotichititsa kupitiriza kugwira ntchito yolalikira?

17 Timalimbikitsidwa kugwira mwakhama ntchito yolalikira tikamaona mmene ikuthandizira anthu padziko lonse. Chaka chilichonse anthu mamiliyoni amabwera ku Chikumbutso komanso amayamba kuphunzira Baibulo. Anthu enanso masauzande ambiri amabatizidwa n’kuyamba kugwira nafe ntchito yolalikira. Sitikudziwa kuti ndi anthu ochuluka bwanji omwe angamvetsere uthenga wathu, koma tikudziwa kuti Yehova akupitiriza kusonkhanitsa khamu lalikulu lomwe lidzapulumuke pa chisautso chachikulu. (Chiv. 7:9, 14) Mwiniwake wa munda akuonabe kuti padakali zokolola zambiri, choncho tili ndi zifukwa zabwino zotichititsa kupitiriza kulalikira.

18. Kodi timafuna kuti anthu ena akationa azizindikira chiyani?

18 Nthawi zonse ophunzira a Yesu ankadziwika chifukwa cha khama lawo polalikira. Anthu ataona kulimba mtima kwa atumwi polalikira, “anazindikira kuti ankayenda ndi Yesu.” (Mac. 4:13) Ifenso anthu akamaona kulimba mtima kwathu polalikira azizindikira kuti tikutsanzira Yesu.

KODI TINGATANI KUTI TIPITIRIZE KULALIKIRA MWAKHAMA POTSANZIRA MMENE YESU . . .

  • ankaonera ntchito yolalikira?

  • ankadalirira Yehova?

  • ankaonera anthu?

NYIMBO NA. 58 Kufufuza Anthu Okonda Mtendere

a TANTHAUZO LA MAWU ENA: Munkhaniyi, mawu akuti “khama” akuimira kufunitsitsa komanso changu chimene Akhristu amasonyeza polambira Yehova.

b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akulalikira mosamala kwa munthu wina pamalo ogulitsira mafuta a galimoto.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena