Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira March 10
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Chitani zitsanzo za mmene mungagawirire Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi Galamukani! ya March pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu. Gawirani magaziniwa limodzi ndi kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso.
Mph.20: “Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Obwera pa Chikumbutso?”a Pokambirana ndime 5, chitani chitsanzo chachidule cha mmene mungayambitsire phunziro la Baibulo ndi mlendo amene anabwera ku Chikumbutso.
Mph.15: “Aliyense Angapatse Yehova Chinachake.”b Ngati nthawi ingalole, pemphani omvetsera kuti afotokoze malemba osagwidwa mawu.
Mlungu Woyambira March 17
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani omvetsera kuti adzabweretse magazini a Nsanja ya Olonda ya April 1 ndi Galamukani! ya April ku Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wamawa ndiponso kuti akakonzekere kudzakambirana ulaliki woyenererana ndi gawo lawo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph.15: Bokosi la Mafunso. Ikambidwe ndi mkulu. Werengani ndi kukambirana nkhani yonse.
Mph.20: “Makolo, Phunzitsani Ana Anu Mowafika Pamtima—Gawo 2.”c Kambiranani ndime 1 mpaka 7. Ngati nthawi ingalole, pemphani omvetsera kuti afotokoze malemba osagwidwa mawu.
Mlungu Woyambira March 24
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti.
Mph.15: Konzekerani Kugawira Magazini Atsopano. Nkhani yokambirana ndi omvetsera. Mukafotokoza mwachidule zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya April 1 ndi Galamukani! ya April, pemphani omvetsera kuti atchule nkhani zimene zingakhale zogwira mtima kwa anthu a m’gawo lawo ndipo afotokoze zifukwa zake. Pemphani omvetsera kuti afotokoze mmene angachitire pogawira magaziniwo pogwiritsa ntchito nkhani zimene angasankhe. Kodi mungafunse funso lotani kuti muyambitse makambirano? Kodi ndi lemba liti m’nkhaniyo limene mungagwiritse ntchito? Chitani chitsanzo cha mmene mungagawirire Nsanja ya Olonda ya April 1 ndi Galamukani! ya April pogwiritsa ntchito ulaliki umene ungagwirizane ndi gawo lanu.
Mph.20: “Makolo, Phunzitsani Ana Anu Mowafika Pamtima—Gawo 2.”d Kambiranani ndime 8 mpaka 14. Ngati nthawi ingalole, pemphani omvetsera kuti afotokoze malemba osagwidwa mawu.
Mlungu Woyambira March 31
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a mwezi wa March.
Mph.20: “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.”e Ngati nthawi ingalole, pemphani omvetsera kuti afotokoze malemba osagwidwa mawu.
Mph.15: “Limbikitsanani Mukakhala mu Utumiki.”*
Mlungu Woyambira April 7
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Tchulani masiku ndi malo a Msonkhano Wachigawo wanu wa 2008 wakuti “Mzimu wa Mulungu Umatitsogolera.”
Mph.20: N’chifukwa Chiyani Mukuchedwa Kubatizidwa? Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2006 masamba 29 mpaka 30, ndime 14 mpaka 17. Phatikizanipo chitsanzo chachidule cha ofalitsa mmodzi kapena awiri amene anabatizidwa ali achinyamata. N’chiyani chinawachititsa kusankha kuchita zinthu zofunika zimenezi adakali aang’ono? Kodi ubatizo unawathandiza bwanji kuti akhale okhwima mwauzimu, ndipo unawateteza bwanji?
Mph.15: Kodi Munayesapo Kuyambitsa Phunziro M’njira Yolunjika? Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera yochokera mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002, tsamba 6. Gwiritsani ntchito zitsanzo za mu mphatikayo ndipo fotokozani mmene mungasinthire zitsanzozo kuti muyambitse phunziro la Baibulo m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kenako chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri. Limbikitsani omvetsera kuti mlungu wamawa adzayesere kuyambitsa phunziro la Baibulo m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pogwiritsa ntchito njira yolunjika.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
e Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.