Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/08 tsamba 3-5
  • Makolo, Phunzitsani Ana Anu Mowafika Pamtima—Gawo 2

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo, Phunzitsani Ana Anu Mowafika Pamtima—Gawo 2
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 3/08 tsamba 3-5

Makolo, Phunzitsani Ana Anu Mowafika Pamtima—Gawo 2

1. Kodi chilango n’chiyani, ndipo n’chofunika chifukwa chiyani?

1 Kodi n’chiyani chingachotse utsiru mumtima mwa mwana? Lemba la Miyambo 22:15 limati, “nthyole yom’langira” ndi imene ingachotse utsiruwo. Mawu akuti Chilango amatanthauza kuphunzitsa kumene kumawongolera mwana. Popereka chilango, makolo ayenera kukhala omvetsa komanso asamasinthesinthe chilangocho. Izi zingathandize kuti makolo asapanikize ana awo ndi malamulo kapena ‘kuwapsetsa mtima.’ (Aef. 6:4) Mwana wanu akayamba kukondana kwambiri ndi anthu omwe si amuna kapena akazi anzake, muyenera kum’patsa chilango. Kulola mnyamata ndi mtsikana amene sanafike msinkhu wokwatira kumacheza okha, kungabweretse mavuto.

2. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene zimathetsa nzeru makolo ambiri? (b) Kodi achimwene ake a Msulami anatani pamene mchemwali wawo anafuna kukayenda awiriwiri ndi bwenzi lake?

2 Ngakhale zili choncho, makolo ambiri amafunsa kuti, ‘Kodi kholo lingatani ngati anawo akufuna kumacheza awiriwiri?’ Achimwene ake a Msulami atadziwa kuti mchemwali wawo ndi mbusa yemwe anali bwenzi lake, akufuna kupita kukayenda awiriwiri kumapiri, makolo awo anawalangiza kuti aletse ulendowo. Anapatsa m’tsikanayo ntchito kuti asakhale ndi mpata ndiponso kuti atalikirane ndi mnyamatayo. Ngakhale kuti anali kum’khulupirira mchemwali wawoyo, iwo anadziwa kuopsa kwa mayesero. Kodi zimenezi zinawononga moyo wa m’tsikanayo? Ayi, koma zinathandiza mnyamata ndi mtsikanayo kudzisunga mpaka nthawi imene anakwatirana.—Nyimbo 1:6; 2:8-15.

3. Kodi makolo ena achita zotani pofuna kutetezera mitima ya ana awo?

3 Masiku anonso makolo afunika kupereka chilango champhamvu kwa ana awo komanso kuwapatsa zochita. Pankhani imeneyi, makolo ayenera kugwiritsa ntchito kuzindikira ndiponso nzeru za Mulungu. (Miy. 24:3) Zimakhala zovuta kwambiri kuti makolo athetse chibwenzi cha mwana wawo ngati mwanayo wayamba kale kukondana ndi chibwenzicho. Makolo achikhristu asanavomereze mwana wawo kukhala pachibwenzi (m’madera amene zimenezi n’zololedwa) ayenera kuganizira msinkhu wa mwana wawo, kukhwima maganizo kwake, kupita kwake patsogolo mwauzimu, munthu amene akufuna kukhala naye pachibwenziyo ndiponso zimene akufuna kudzachita. Mayi wina yemwe mwana wake wamkazi wa zaka 19 anachotsedwa mu mpingo chifukwa cha chiwerewere atamufunsa zimene akanachita ngati atayambiranso kulera mwana wakeyo, anayankha kuti: “Sindikanayerekeza kumulola kuchita chibwenzi adakali wamng’ono. Sindikanangoganiza kuti ndi wokhwima maganizo moti akhoza kuthana ndi mavuto amene anakumana nawo.”

4, 5. (a) Kodi ndi nzeru kuti anthu amene akufuna kukwatirana akane ngati makolo awapatsa munthu woti ayende nawo? (b) Kodi mnyamata wina anaphunzira chiyani atagwa m’mavuto?

4 Makolo ena akambiranapo ndi mnyamata ndi mtsikana amene akufuna kukhala pachibwenzi ndi kuwafotokozera chifukwa chimene makolowo sakufunira chibwenzicho. Zingathandize kwambiri kukambirana nkhaniyo ndi makolo a mwana winayo. Kholo lina la Chikhristu lomwe lili ndi ana anayi linati: “Makolo ambiri amaganiza kuti chikondi chapakati pa ana ndi ‘chosangalatsa’ ndipo amalimbikitsa anawo kuti azikondana. Amalolanso anyamata ndi atsikana kukayenda popanda munthu wamkulu wowayang’anira. Zotsatira zake zimakhala zibwenzi, chiwerewere ndi kukwatira kapena kukwatiwa msanga kwa anawo. Timalimbikitsa ana athu kuti azikonda kuchita masewera olimbitsa thupi ngati kukwera njinga. Angasewere okha, limodzi ndi banja, kapena ndi akazi kapena amuna anzawo.”

5 Ngakhale ngati mwamuna ndi mkazi omwe ali pachibwenzi ndi a msinkhu woyenerera, ndibwino kukonza zoti pakhale munthu woyenda nawo. Akhristu ena achinyamata amene anali pachibwenzi ndipo anali atatsala pang’ono kukwatirana, anachita “chonyansa” chifukwa choyenda okha. (Agal. 5:19) Pokumbukira, mnyamatayo anati: “Nthawi zonse tinkayenda ndi munthu wina. Koma tinagwa m’mavuto chifukwa choyenda tokha nthawi zingapo.” Achinyamata ena anathokoza makolo awo chifukwa chowapatsa malamulo okhwima ndiponso kuonetsetsa zosangalatsa zimene iwo ankachita. Chifukwa chothandizidwa, achinyamatawo anazisungabe mpaka analowa m’banja ndipo amasangalala kuti sanachite choipa. Ngati zolinga za mwana wanu zili zabwino, sangakane uphungu wochokera kwa Mulungu chifukwa ndi “njira ya moyo.”—Miy. 6:23.

6. (a) Kodi n’chiyani chingateteze mwana wanu kuti asachite chiwerewere, ndipo n’chiyani chingamuthandize kuchita zimenezo? (b) Kodi ndi mafunso otani amene makolo angadzifunse pa zimene amachita?

6 Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi chitetezo chachikulu kuti mwana wanu asachite chiwerewere. Ngakhale kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndi udindo wa mwanayo, kholo lingam’thandize. Choyamba, mwana wanu angatengere chitsanzo chanu cha kudzipereka. Anthu amene anakhala Akhristu m’nthawi ya atumwi ku Tesalonika anaona kuti Paulo ndi anzake ‘anali anthu otani’ ndipo ‘anakhala owatsanzira,’ kenako anakhala ndi “chitsimikizo champhamvu” monga mmene iwowo analili. (1 Ates. 1:4-6) Kodi ana anu amaona kuti ndinu “anthu otani?” Kodi amaona kuti muli ndi “chitsimikizo champhamvu” ndiponso kuti mukudzipereka kwa Mulungu ndi moyo wanu wonse? Kodi amaona kuti mumanyansidwa kwambiri ndi chiwerewere mwa kupewa zosangalatsa zimene zimalimbikitsa khalidwe la chiwerewere? Kodi anawo amaona kuti muli ndi chikondi pa zimene mumachita ndi mkazi kapena mwamuna wanu ndiponso anthu ena? Kodi amamva mukulankhula za Yehova m’njira yosonyeza kuti ndi weniweni kwa inu? Chitsanzo chanu chingalimbikitse ana anu kudzipereka ndi mtima wonse posunga malamulo a Yehova. Mwana wanu adzaona kuti kuchita zimenezi, n’kofunika kwambiri.

7. Kodi n’chiyani chingawononge ntchito yanu yophunzitsa mwana?

7 Mukafufuza mosamalitsa anthu amene ana anu amacheza nawo ndiponso kuwasankhira anzawo amene ali ndi “chitsimikizo champhamvu” pa zinthu zauzimu, khama lophunzitsa mwana wanu lidzapindula. Palibe chinthu chilichonse chimene chingawononge msanga khalidwe la ana anu kuposa mabwenzi oipa, ngakhale ngati mabwenzi oterewa ali mumpingo wachikhristu. Mabwenzi otere angawononge khalidwe labwino la mwana wanu ndi kum’chititsa kuona kuti ndinu achikalekale.—Miy. 13:20; Yuda 3, 4, 12, 16, 19.

8. (a) Mogwirizana ndi 1 Yohane 2:14, n’chiyani chimalimbikitsa mwauzimu ndipo ndi udindo wotani umene makolo ali nawo? (b) Kodi mukuganizira mfundo zothandiza zotani, kuti phunziro la Baibulo lizichitika nthawi zonse ndiponso kuti lizikhala losangalatsa?

8 Monga makolo, muyenera kukhutira kuti Mawu a Mulungu Baibulo, ndi amphamvu. Mtumwi Yohane ananena kuti “anyamata” olimba mwauzimu a mumpingo umene anaulembera kalata ‘anagonjetsa woipayo’ chifukwa ‘mawu a Mulungu anakhaladi mwa iwo.’ (1 Yoh. 2:14) Kuwonjezera pa kukhala ndi banja logwirizana komanso kukhala ndi chitsanzo chabwino, makolo oopa Mulungu ayenera kuphunzira Mawu a Mulungu limodzi ndi banja lawo nthawi zonse, kuti mawuwo akhazikike mumtima mwa mwana. Banja lina linakhumudwa kuona awiri mwa ana awo achinyamata atatu atapanduka. Bambo awo amene anawalera m’Chikhristu kuyambira ali aang’ono, anati: “Ndikanakhala ndi mwayi woleranso anawa, ndikanakhala ndi phunziro la Baibulo nthawi zonse. Tinkaphunzira mwa apo ndi apo. Ndikudziwa kuti phunziro la nthawi zonse likanatithandiza kukhala ndi banja logwirizana ndi kulimbikitsa kwambiri ana athu mwauzimu.” Makolo akamakonzekera bwino, akamapewa kuumirira pa zimene iwo akufuna, kupewa kupanga zinthu mwamwambo chabe, ndipo akamachititsa phunziro logwirizana ndi zosowa za ana awo, anawo adzayembekezera phunzirolo mwachidwi ndipo lidzachititsa banja kukhala logwirizana mwauzimu. N’zodziwikiratu kuti sizingakhale zophweka chifukwa makolo amakhala otanganidwa. Chofunika kwambiri sikutalika kwa phunzirolo koma kuti nthawi imene muli limodziyo, izikhala yosangalatsa kwambiri. Chinanso n’chakuti makolo afunika kuphunzitsa ana awo kukhala ndi chizolowezi chabwino chophunzira paokha.—Deut. 6:4-9.

9. Kodi mungaphunzitse bwanji mwana wanu kupemphera bwino?

9 Pemphero lochokera pansi pamtima limalimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu. Thandizani mwana wanu kuona kufunika kwa pemphero ndiponso mmene ‘angatsanulire mtima wake’ kwa Yehova. (Sal. 62:8) Lolani kuti mwana wanu azimvetsera mapemphero anu. Kambiranani naye zimene angatchule m’mapemphero ake. Mukamamuuza mmene Yehova wayankhira mapemphero anu ndi kumulimbikitsa kuona mmene Yehova angayankhirenso mapemphero ake, mwana wanu adzazindikira kuti pemphero ndi lamphamvu.

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani mwana ayenera kuphunzitsidwa kuti aziopa Yehova? (b) Kodi ndani amene makolo ayenera kupita naye muutumiki nthawi zonse, ndipo n’chifukwa chiyani?

10 Mfumu Davide analemba kuti: ‘Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye.’ (Sal. 25:14) Choncho, kuti mwana wanu akhaledi pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu, ayenera kuopa zinthu zimene angakumane nazo chifukwa chokwiyitsa “Mulungu wamoyo.” (Aheb. 10:31; Miy. 8:13) N’zoona kuti mwana ayenera kukonda Yehova ndi kumuyamikira kwambiri chifukwa cha chifundo ndi ubwino wake, koma ayenera kulemekeza kwambiri makonzedwe a Yehova olanga kapena kulola munthu kuti ‘akolole chimene wafesa.’ (Agal. 6:7) Akakhala ndi “mantha” oyenerera kuyambira pa ubwana wake, zidzamuthandiza kukhala ndi chikumbumtima chabwino. M’malo mongoganiza kuti, ‘zonse zili bwino bola ngati sanandigwire,’ iye adzamva ngati mmene anamvera Yosefe yemwe anakana kumunyengerera kuti achite chiwerewere ndipo anati: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?”—Gen. 39:7-9.

11 Mudzathandiza mwana wanu kukonda anthu ngati mmene Yehova amachitira, popita naye muutumiki wachikhristu. Mwanayo akamakhala ndi mtima woyamikira, adzaona mmene ‘angalemeretsere ambiri’ powaphunzitsa “uthenga wabwino” umene ungawathandize kuti asinthe moyo wawo. Utumiki umenewu ndi njira yabwinonso yokhalira pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.—2 Akor. 6:10

12, 13. (a) Kodi n’chifukwa chiyani makolo amafunikira ‘mphamvu yoposa yachibadwa’? (b) Kodi thandizo limeneli limachokera kuti? (c) Kodi bambo wina anachita chiyani ataganiza kuti mwana wake ‘akupanduka,’ ndipo kenako anazindikira chiyani?

12 Bambo wina wachikhristu anali ndi mantha chifukwa mwana wake wamkazi wa zaka 16, yemwe anali wofatsa kwambiri, amavutitsidwa ndi anyamata kusukulu. Iye anati: “Sizophweka kulera ana a chinyamata. Nthawi zambiri ndimapemphera pandekha komanso kupemphera naye limodzi, koma ndili ndi nkhawabe.” Indedi, bambowa anaona kufunika kwa thandizo la Mulungu limene lingapatse iwo komanso mwana wawoyo “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akor. 4:7.

13 Nthawi zina makolo angakhumudwe akaona kuti khama lawo silikupindula. Koma musataye mtima. Chifukwa cha khalidwe la mwana wawo lotayirira, bambo wina wachikhristu anavomereza kuti panthawi ina anamva ngati mwana wawo yemwe anamulera m’chikhristu kuyambira ali wamng’ono, “wapanduka”. Bambowa anati: “Ndinagwada pansi ndi kupemphera mpaka kugwetsa misozi, ndipo ndinapempha Yehova kuti andithandize. Yehova anayankha mapempherowo ndipo pang’ono ndi pang’ono mnyamatayo anasintha. Ndinayandikira kwambiri kwa Yehova nditaona mmene anathandizira banja langa.” Ndibwino kupempha thandizo kwa Yehova ndi kumudalira. Pempherani limodzi ndi ana anu ndipo muziwapempherera. Mukatero mudzaona kuti Yehova adzathandiza banja lanu.—1 Ates. 5:17.

14. (a) Kodi ndani amene ayenera kuphunzitsa mwana malamulo a Mulungu? (b) Kodi makolonu mumamva bwanji ana anu akamasonyeza mtima ‘wanzeru’?

14 Zindikirani kuti potsirizira pake mwana wanu afunikira kusunga malamulo a Yehova pamtima pake. (Yerekezerani ndi Miyambo 3:1-4.) Komabe, inu makolo chitani zonse zomwe mungathe kuti muphunzitse mwana wanu momufika pamtima. Zimakhala zonyaditsa kwambiri kuona mwana akukhalabe mokhulupirika m’choonadi. Mumakhala ndi ‘mtima wokondwera’ ana anu akamasonyeza kuti ndi “anzeru.” (Miy. 23:15) Mudzafanana ndi mtumwi Yohane amene ponena za ana ake auzimu anati: “Palibe chondisangalatsa koposa zinthu zimenezi, kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.”—3 Yoh. 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena