Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/08 tsamba 2-7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 3/08 tsamba 2-7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Chitani maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pa nkhani yapadera, koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zambiri. Cholinga cha maulendo obwerezawa chikhale kuyambitsa phunziro la Baibulo ndi anthu amene sanayambebe kuphunzira. June: Gawirani buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Mipingo imene ilibe mabukuwa ingagawire buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha.

◼ M’bale amene woyang’anira wotsogolera wamusankha, awerengere maakaunti a mpingo a miyezi ya December, January, ndi February. Munthu mmodzi asawerengere maakaunti maulendo awiri otsatizana. Mukatha kuwerengerako, lengezani ku mpingo pamodzi ndi lipoti lotsatira la maakaunti.—Onani Malangizo Oyendetsera Maakaunti a Mpingo (S-27).

◼ Mutu wa msonkhano wachigawo wa 2008 ndi wakuti “Mzimu wa Mulungu Umatitsogolera.” Utumiki Wathu wa Ufumu wa July, udzafotokoza mwatsatanetsatane mfundo zothandiza kuti mukonzekere kudzapezeka pa chigawo chilichonse cha msonkhano wa masiku atatu umenewu. Musazengereze kupempha tchuthi kwa abwana anu kuti mudzapezekepo masiku onse atatu, ngati muli pa ntchito.

◼ Ofesi ya nthambi silembera wofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Ofalitsa azioda okha mabuku amene akufuna kudzera ku mpingo. Woyang’anira wotsogolera azilengeza mwezi uliwonse asanatumize ku nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale woyang’anira za mabuku. Chonde, kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera. (Mpingo uyenera kuitanitsa zimenezo kokha ngati pali anthu amene akuzifuna.) Muzitumiza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) mwachangu mwezi uliwonse ngakhale ngati mukufuna mabuku ochepa.

◼ Mtumiki wa magazini aone kuchuluka kwa magazini ophunzira a Nsanja ya Olonda ndi magazini ogawira komanso a Galamukani! amene akulandira. Ngati akulandira ochuluka kwambiri, mpingo uyenera kuchepetsa chiwerengerocho pogwiritsa ntchito Fomu ya Maoda a Magazini (M-202). Ngati akulandira ochepa kwambiri angathenso kuwonjezera chiwerengerocho. Dziwani kuti pangadutse miyezi ingapo kuti oda yanu yatsopanoyo iyambe kubwera.

◼ Mipingo iyambe kuitanitsa mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2007. Mabaundi voliyumu amenewa ali m’Chingelezi ndi m’Chifalansa. Kufikira pamene mavoliyumuwa adzakhalapo ndi kutumizidwa azidzaonekera monga “zoyembekezeredwa” pa mapepala otumizira mabuku. Mavoliyumu amenewa ndi zinthu zofunsira mwapadera.

◼ Mipingo izipereka kwa ofalitsa magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akangofika. Zimenezi zidzathandiza kuti ofalitsa athe kudziwiratu bwino nkhani zimene zili m’magaziniwo asanawagawire mu utumiki wa kumunda. Utumiki Wathu wa Ufumu uyeneranso kugawidwa kwa ofalitsa ukangofika.

◼ Mabuku Atsopano Amene Alipo:

“Come Be My Follower” (cf)—Chingelezi ndi Chifalansa

Watch Tower Publications Index 2006 (dx06)—Chinenero Chamanja cha ku America

(Zapitirizidwa patsamba 7)

Zilengezo (Zachokera patsamba 2)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena