PHUNZIRO 33
Khalani Wosamala Komanso Wolimba
KUSAMALA ndi luso lochita zinthu ndi anthu ena popanda kuwakhumudwitsa wambawamba. Kumaphatikizapo kudziŵa mmene munganenere zinthu ndi pamene muyenera kuzinena. Zimenezo sizikutanthauza kulephera kunena zoona kapena kupotoza zenizeni ayi. Kusamala sikutanthauzanso kuopa munthu.—Miy. 29:25.
Zipatso za mzimu zimathandiza kwambiri pokhala wosamala. Choncho, munthu amene ali ndi chikondi safuna kukwiyitsa ena; amafuna kuwathandiza. Munthu wachifundo ndi wofatsa amachita zinthu modekha. Munthu wamtendere amafunafuna njira zothandiza kumvana ndi ena. Munthu woleza mtima amakhalabe wodekha ngakhale pakati pa anthu aukali.—Agal. 5:22, 23.
Komabe, alipo anthu ena amene adzanyansidwabe ndi uthenga wa m’Baibulo, mulimonse mmene mungaufotokozere. Kwa Ayuda ambiri a m’zaka 100 zoyambirira, Yesu Kristu anakhala “mwala wakukhumudwa nawo, ndi thanthwe lopunthwitsa,” chifukwa cha kuipa kwa mitima yawo. (1 Pet. 2:7, 8) Ponena za ntchito yake yolengeza Ufumu, Yesu anati: “Ndinadzera kuponya moto padziko lapansi.” (Luka 12:49) Ndipo uthenga wa Ufumu wa Yehova, umene umafuna kuti anthu azindikire ulamuliro wa Mlengi wawo, ikali nkhani yaikulu imene imakhudza anthu onse. Anthu ambiri amakhumudwa ndi uthenga wakuti posachedwa Ufumu wa Mulungu udzachotsa ulamuliro woipa umene ulipowu. Koma ife pomvera Mulungu, sitileka kulalikira. Pamene tikutero, sitiiŵala langizo la m’Baibulo lakuti: “Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”—Aroma 12:18.
Kusamala Polalikira. Ilipo mipata yambiri pamene timalankhula ndi anthu za chikhulupiriro chathu. N’zoona kuti timateronso mu utumiki wa kumunda, komabe timayesa kupezanso mipata ina pamene tili ndi achibale athu, anzathu a kuntchito, ndi anzathu a kusukulu. M’mikhalidwe yonseyi, kusamala n’kofunikira.
Ngati tilalikira uthenga wa Ufumu m’njira yopangitsa ena kuona ngati tikuwapatsa uphungu, angaipidwe nazo. Chifukwa chakuti sanatipemphe chithandizo ndipo mwina sakuchifuna, angakwiye nafe ngati tionetsa kuti tikuyesa kuwawongolera. Kodi tingatani kuti tisapereke ganizo limenelo? Tiyenera kuphunzira luso locheza ndi anthu mwaubwenzi.
Yesani kuyamba makambirano anu ndi nkhani imene winayo adzakondwera nayo. Ngati munthuyo ndi wachibale, mnzanu wa kuntchito, kapena wa kusukulu, mungadziŵe zimene zingam’sangalatse. Ngakhale atakhala munthu woti n’koyamba kukumana naye, mungayambitse nkhani imene yamveka panyuzi kapena imene ili m’kamwam’kamwa. Nkhani zotero kaŵirikaŵiri zimasonyeza zimene zili m’maganizo mwa anthu ochuluka. Pamene mukulalikira nyumba ndi nyumba, khalani maso. Zokongoletsa pakhomo, zoseŵeretsa ana, zinthu zokhudzana ndi kupembedza, komanso mawu kapena zithunzi zomata pagalimoto yoimika pakhomo zingasonyeze nkhani imene ingasangalatse mwininyumba. Mwininyumba akatuluka, mvetserani zimene ati alankhule. Zimene ati anenezo zingagwirizane kapena zingasiyane ndi zimene mwam’ganizira. Koma zingakuthandizeni kudziŵa zimene muyenera kunena kuti mum’lalikire.
Pamene kukambirana kuli m’kati, tchulani mfundo za m’Baibulo ndi za m’mabuku ophunzirira Baibulo zokhudzana ndi nkhaniyo. Koma kulankhulako kusakhale kwa inu nokha. (Mlal. 3:7) Perekani mpata kwa mwininyumba kuti azilankhulapo ngati akufuna. Mvetserani mosamala maganizo ake. Angakuthandizeni kudziŵa mofunika kusamala.
Musananene kanthu, ganizirani kaye kuti kodi zimene munenezo zidzamveka bwanji kwa munthuyo. Miyambo 12:8, NW, imatamanda “m’kamwa mwanzeru.” Mawu ake achihebri pamenepa amatanthauzanso kuzindikira ndi kuchenjera. Choncho, nzeru imaphatikizapo kusamala polankhula chifukwa choganizira bwino nkhaniyo kuti uchite mwanzeru. Miyambo 12:18 imachenjeza kuti tipeŵe ‘kunena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.’ N’zotheka kukweza choonadi cha m’Baibulo popanda kukhumudwitsa wina.
Kungodziŵa kusankha bwino mawu kungakuthandizeni kupeŵa zopinga kukambirana. Ngati kutchula liwu lakuti “Baibulo” kungachititse munthu kusafuna kukambirana, mungatchule kuti “mawu opatulika” kapena “buku limene tsopano lafalitsidwa m’zinenero zoposa 2,000.” Ngati mukufuna kutchula Baibulo, mungafunse munthuyo mmene akuliganizira ndiyeno samalani zimene wanenazo pamene mukukambirana.
Kukhala wosamala kumafuna kudziŵa nthaŵi yoyenera kunena zinthu. (Miy. 25:11) Simungavomereze zonse zimene munthuyo anganene, koma n’kosafunikira kuyesa kuwongolera chilichonse chotsutsana ndi malemba chimene anganene. Musayese kuuza mwininyumbayo zonse nthaŵi imodzi. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.”—Yoh. 16:12.
Ngati n’kotheka, ayamikireni moona mtima amene mukulankhula nawo. Ngakhale pamene mwininyumba ali wotsutsa, mukhoza kum’yamikirabe pa mfundo inayake imene watchula. N’zimene mtumwi Paulo anachita polankhula kwa anzeru ku Areopagi ku Atene. Anzeruwo “anatengana naye.” Kodi iye anatha bwanji kufotokoza mfundo yake popanda kuwakhumudwitsa? Poyamba anali ataona maguwa ambiri amene anapangira milungu yawo. M’malo mowatsutsa Aatenewo pa kulambira mafano kwawo, mosamala anawathokoza pokhala ndi mtima wofunitsitsa kupembedza. Iye anati: ‘M’zinthu zonse ndaona kuti muli akupembedzetsa.’ Njira imeneyi inam’tsegulira mpata kuti apereke uthenga wake wonena za Mulungu woona. Zotsatira zake, ena mwa iwo anakhala okhulupirira.—Mac. 17:18, 22, 34.
Ena akamatsutsa kapena kukana, inuyo musakwiye ayi. Khazikani mtima pansi. Onani zimenezo ngati mwayi woonerapo kalingaliridwe ka munthuyo. Mungachite bwino ngakhale kumuyamikira chifukwa chopereka maganizo ake. Koma bwanji ngati monyanyuka anena kuti: “Inenso ndili ndi mpingo wanga”? Mosamala mungafunse kuti: “Kodi mwakhala wopembedza kukula kwanu konse?” Ndiye akayankha, wonjezani kuti: “Kodi muganiza nthaŵi ina anthu onse adzagwirizana ndi kukhala mpingo umodzi?” Mafunso ameneŵa angatsegule mpata wokambirana zambiri.
Kukhala ndi maganizo oyenera a mmene timadzionera kungatithandize kukhala osamala. Tili otsimikiza zolimba kuti njira za Yehova n’zolungama ndipo Mawu ake ndi oona. Timalankhula zinthu zimenezi ndi chitsimikizo. Koma tisadziyese olungama mopambanitsa. (Mlal. 7:15, 16) Tili oyamikira podziŵa choonadi ndi kusangalala ndi madalitso a Yehova. Komabe, timadziŵa kuti kutiyanja kumene iye watiyanja nako, si chifukwa cha chilungamo chathu ayi, koma kukoma mtima kwake kopambana ndi chikhulupiriro chathu mwa Kristu. (Aef. 2:8, 9) Timazindikira kufunika ‘kodziyesa tokha kuona ngati tili m’chikhulupiriro, kuti tidzitsimikizire tokha.’ (2 Akor. 13:5) Choncho polankhula ndi anthu za kuyendera miyezo ya Mulungu, ifenso timayesetsa modzichepetsa kutsatira uphungu wa Baibulo. Si kwa ife kuweruza anthu anzathu. Yehova “anapereka kuweruza konse kwa Mwana,” ndipo tonsefe tikaonekera ku mpando wake woweruzira kuti tikayankhe pa ntchito zathu.—Yoh. 5:22; 2 Akor. 5:10.
Kwa a Pabanja Pathu ndi Akristu Anzathu. Si mu utumiki wa kumunda mokha mmene tiyenera kusamala kalankhulidwe kathu. Popeza kuti kukhala wosamala ndi umboni wa chipatso cha mzimu wa Mulungu, tiyeneranso kukhala wosamala panyumba pochita zinthu ndi a pabanja. Chikondi chidzatilimbikitsa kusamala za maganizo a ena. Mwamuna wa mfumukazi Estere sanali wokhulupirira Yehova, koma mfumukaziyo inam’lemekeza iye ndipo inkakhala yosamala kwambiri pomuuza nkhani zokhudza atumiki a Yehova. (Estere, macha. 3-8) Nthaŵi zina, kukhala wosamala pochita ndi achibale amene si Mboni kungafune kuti tiwalole azindikire choonadi mwa kungoona khalidwe lathu, m’malo mwa kumawafotokozera zimene timakhulupirira.—1 Pet. 3:1, 2.
Mofananamo, powadziŵa bwino abale ndi alongo a mu mpingo, si ndiye kuti tingalankhule nawo mosasamala kapena kuwachita chipongwe. Tisakhale ndi maganizo akuti ndi okhwima mwauzimu sangakhumudwe. Kapena tisadzikhululukire mwa kunena kuti: “Kungoti sandidziŵa bwino, ndi mmene ineyo ndimalankhulira.” Ngati tiona kuti kalankhulidwe kathu kamakhumudwitsa ena, tiyenera kusintha basi. “Chikondano chenicheni” chimene tili nacho kwa wina ndi mnzake chitilimbikitse ‘kuchitira . . . chokoma . . . a pabanja la chikhulupiriro.’—1 Pet. 4:8, 15; Agal. 6:10.
Polankhula kwa Omvera. Aja amene amalankhula pa pulatifomu afunikiranso kukhala osamala. Mwa omvera mumakhala anthu osiyanasiyana. Alinso a misinkhu yosiyanasiyana mwauzimu. Mwina ena ndi koyamba kufika pa Nyumba ya Ufumu. Ena angakhale ndi vuto linalake losautsa limene wokamba nkhaniyo sakudziŵa. Kodi wokamba nkhaniyo angapeŵe motani kukhumudwitsa omverawo?
Mogwirizana ndi uphungu wa mtumwi Paulo kwa Tito, cholinga chanu chikhale ‘kusachitira mwano munthu aliyense, . . . kukhala wofatsa kwa anthu onse.’ (Tito 3:2) Musatengere anthu a dziko okonda kugwiritsa ntchito mawu onyoza anthu osiyana nawo fuko, chinenero, kapena dziko. (Chiv. 7:9, 10) Mosabisa mawu, fotokozani zimene Yehova amafuna, ndipo sonyezani mmene kulili kwanzeru kutsatira zimenezo; koma peŵani mawu osuliza aja amene sanafikebe poyenda m’njira ya Yehova mokwanira. M’malo mwake, limbikitsani onse kuti azindikire chifuniro cha Mulungu ndi kuchita zimene zimam’sangalatsa. Kometserani uphungu ndi mawu achikondi ndi oyamikira moona mtima. Mmene mukulankhulira ndi kamvekedwe ka mawu anu, zisonyeze chikondi chaubale chimene tonse tiyenera kukhala nacho kwa wina ndi mnzake.—1 Ates. 4:1-12; 1 Pet. 3:8.