Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu September: Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Mipingo imene ili ndi Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kapena Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe m’sitoko ingagaŵire mabuku ameneŵa. October: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda kapena ya Galamukani! kapena ya magazini onse aŵiri. November: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Kuyesayesa kwapadera kudzachitidwa kubwerera kulikonse kumene tinagaŵira zofalitsa, ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. December: New World Translation ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena winawake woikidwa ndi iye ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Lengezani ku mpingo mutachita zimenezi.
◼ Ofalitsa okonzekera kutumikira monga apainiya othandiza m’October ayenera kupereka msanga pempho lawo. Zimenezi zidzalola akulu kupanga makonzedwe ofunikira a magazini, mabuku, ndi gawo.
◼ Akulu akukumbutsidwa kutsatira malangizo operekedwa pamasamba 21-3 a Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, onena za wochotsedwa aliyense kapena munthu wodzilekanitsa amene angakonde kubwezeretsedwa.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Mabaundi voliyumu a Watchtower a 1951-57 ndi 1960-95—Chingelezi
Mabaundi voliyumu a Awake! a 1984, 85, 87, ndi 1991-95—Chingelezi
◼ Zofalitsa Zomwe Mulibe m’Sitoko Kwakanthaŵi:
Magazine File Case
◼ Zofalitsa Zomwe Mulibe m’Sitoko Kwachikhalire:
Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe—Chicheŵa, Chingelezi
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi—Chicheŵa, Chingelezi