Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tiyenera kukumbukira chiyani poŵerenga ndime pamisonkhano?
Nthaŵi yochuluka ya Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi Phunziro la Buku la Mpingo imagwiritsiridwa ntchito poŵerenga ndime. Zimenezi zikutanthauza kuti mbale wogaŵiridwa kuŵerenga amasenza thayo lalikulu monga mphunzitsi. Ayenera kuŵerenga mwanjira yopereka ‘tanthauzo’ la nkhaniyo kuti omvetserawo asangoimvetsa chabe komanso kuti asonkhezeredwe kuchitapo kanthu. (Neh. 8:8) Chifukwa chake, woŵerenga afunikira kukonzekera bwino gawo lake. (1 Tim. 4:13; onani phunziro 6 la Bukhu Lolangiza la Sukulu.) Nazi zofunika pa kuŵerenga kwabwino kwa poyera.
Gogomezerani Ganizo Moyenera: Dziŵani pasadakhale mawu ofunikira kugogomezera kuti lingaliro lake lolondola limveke.
Tchulani Mawu Molondola: Matchulidwe oyenera ndi kumveketsa mawu bwino nkofunika kuti omvetsera azindikire mawu amene ali m’chofalitsa. Pezani mmene abale ena okhoza amawatchulira.
Lankhulani Momveka ndi Mwaumoyo: Kulankhula mwaumoyo kumadzutsa chidwi, kumakhudza mtima, ndi kusonkhezera womvetsera.
Khalani Waubwenzi ndi Kumveka Monga Ngati Mukulankhula: Kulankhula mwachibadwa kumakhalapo ngati mukuŵerenga mwamyaa. Mwa kukonzekera ndi kuyeseza, woŵerenga amakhala womasuka, ndipo kuŵerenga kwake kumakhala kokopa osati kogwetsa ulesi ndi kotopetsa.—Hab. 2:2, NW.
Ŵerengani Nkhaniyo Monga Momwe Yasindikizidwira: Mawu amtsinde limodzi ndi chidziŵitso m’mabulaketi nthaŵi zambiri zimaŵerengedwa momveka ngati zikumveketsa mawu osindikizidwawo. Kusiyapo kokha ngati ndi malifalensi ongosonyeza magwero a nkhaniyo. Mawu amtsinde ayenera kuŵerengedwa pamene asonyezedwa m’ndime, mwa kunena kuti: “Mawu amtsinde akuti . . . ” Mutawaŵerenga, ingopitirizani mbali yotsala ya ndimeyo.
Pamene kuŵerenga kwapoyera kuchitidwa bwino, ndiko njira yofunika kwambiri imene ‘tingaphunzitsire ena kusunga zinthu zonse zimene analamula’ Mphunzitsi Wamkulu.—Mat. 28:20.