PHUNZIRO 14
Kulankhula Mwachibadwa
KULANKHULA mwachibadwa ndiko kungachititse anthu kukhulupirira zimene mukunena. Mutazindikira kuti munthu amene anakuuzani zakutizakuti anangovala nkhope yopeka, kodi mungakhulupirirebe zimene iye anakuuzani? Kapena mungakhulupirire mawu ake kokha chifukwa nkhope yopekayo inali yokongola kuposa yake yachibadwa? N’zokayikitsa ngati mungatero. Choncho, m’malo molankhula mwa mtundu winawake, lankhulani mmene mumalankhulira.
Pamene tikuti kulankhula mwachibadwa sitikutanthauza kulankhula mosasamala. Tisalankhule molakwitsa galamala, motchula mawu molakwika, ndi movumatira mawu. Tipeŵenso kalankhulidwe kachinyamata. Nthaŵi zonse tionetse ulemu woyenerera, m’kalankhulidwe komanso m’khalidwe lathu. Munthu amene amalankhula mwachibadwa, salankhula mwaulemu wopambanitsa komanso sakhala ndi cholinga chofuna kupanga dzina.
Mu Utumiki wa Kumunda. Pamene mufika panyumba kapena pofuna kulalikira munthu pamalo opezekapo anthu osiyanasiyana, kodi mumamva mantha ena ake? Anthu ambiri amatero asanayambe kulankhula, koma kwa ena manthawo amapitirira. Kumangika thupi kungachititse mawu kusatuluka momasuka kapena angamatuluke onjenjemera. Mantha amaonekanso mwa kusakhazikika kwa manja ndi mutu.
Wofalitsa angakhale ndi vuto limeneli pazifukwa zingapo. Mwina akulingalira za mmene enawo akumuonera kapena akukayikakayika ngati ulaliki wake ukhala wopambana. Zonsezi sizachilendo, koma vuto limakhalapo ngati munthu alingalira zimenezi mopambanitsa. Kodi chingathandize n’chiyani ngati mumachita mantha poloŵa mu utumiki? Kukonzekera mwakhama ndi pemphero lochokera pansi pa mtima. (Mac. 4:29) Taganizani za chifundo chachikulu cha Yehova popereka kwa anthu mwayi wokhala ndi thanzi langwiro ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Taganizani za anthu ofunikira kumva uthenga wabwino amene mukuyesetsa kuwathandiza.
Koma musaiŵale kuti anthu ali ndi ufulu wosankha zimene afuna, choncho akhoza kulandira uthengawo kapena kuukana. Zinalinso chomwecho pamene Yesu anali kulalikira mu Israyeli wakale. Ntchito yanu ndi kulalikira basi. (Mat. 24:14) Ngakhale anthu asakuloleni kulankhula, kuwafikira kokhako kumachitira umboni. Mumakhala mutapambana pamenepo chifukwa mwalola Yehova kuti akugwiritseni ntchito kukwaniritsa chifuniro chake. Koma mukakhala ndi mpata wolankhula, kodi muyenera kulankhula motani? Ngati muphunzira kuika maganizo anu pa zosoŵa za ena, kalankhulidwe kanu kadzakhala kokoma ndiponso kachibadwa.
Pochitira umboni, ngati muchita zinthu ndi kulankhula mwa masiku onse, omvera anu adzakhala omasuka. Amatcheranso khutu ku mfundo za m’Malemba zimene mukuwafotokozera. M’malo mokamba nkhani kwa iwo, kambiranani nawo. Sonyezani mzimu waubwenzi. Sonyezani chidwi chanu pa iwo, ndipo yamikirani zolankhulapo zawo. Inde, kumene chinenero kapena chikhalidwe chimafuna machitidwe ena ake osonyeza ulemu polankhula ndi anthu osawadziŵa, tsatirani zimenezo. Koma nthaŵi zonse khalani wokonzeka kumwetulira mwaubwenzi.
Papulatifomu. Pamene mulankhula pamaso pa gulu, kulankhula mwachibadwa ndi monga mokambirana ndiyo njira yabwino koposa. Koma ngati gululo n’lalikulu, m’pofunika kuwonjezera mphamvu ya mawu. Ngati muyesa kuloŵeza pamtima nkhani yanu kapena ngati manotsi anu ndi ochuluka kwambiri, ndiye kuti mwina nkhaŵa yanu yaikulu ndi yofuna kutchula zinthu ndendende mmene munakonzekerera. Kutchula mawu moyenerera n’kofunika, koma ngati musamala kwambiri zimenezo, mumalankhula momangika ndi mosakhala mwachibadwa. Kulankhula mwachibadwa kumatayika. Muyenera kuganiziratu mosamala zimene mukanene, ndipo polankhula samalani kwambiri malingaliro, osati kulankhula ndendende mmene munakonzekerera.
N’chimodzimodzinso pamene akukufunsani pamsonkhano. Khalani wokonzekera bwino, koma musaŵerenge mayankho kapena kuwaloŵeza pamtima. Yankhani mmene mumalankhulira nthaŵi zonse kotero kuti mayankho anu amveke okoma mwachibadwa.
Ngakhale maluso osiririka akulankhula, ngati achitidwa monyanyira, omvera amaipidwa nawo. Mwachitsanzo, muyenera kulankhula bwino ndi kutchula bwino mawu, koma osati mopambanitsa moti mawu anu n’kumveka mwa mtundu winawake wosakhala wachibadwa. Ngati manja otsindika ndi ofotokoza muwapanga bwino, nkhani yanu imakhala yaumoyo. Koma kulimbitsa manja kapena kuwaponya monyanyira kumachotsa maganizo a anthu pa zimene mukunena. Lankhulani ndi mawu omveka bwino, koma musamakweze kwambiri. Ndi bwino nthaŵi zina kutenthetsa nkhani yanu, koma peŵani kufuula. Kusinthasintha mawu, kulankhula mwaumoyo, ndi kukhudzika mtima, ziyenera kuchitidwa m’njira yosapangitsa omvera kungoganiza za inu, kapena kuchititsa manyazi omvera.
Anthu ena mwachibadwa amalankhula bwino kwambiri ngati kuti achita kukonzekera, ngakhale pamene sakukamba nkhani. Ena ali ndi malankhulidwe achisawawa. Chofunika ndicho kulankhula mosamala masiku onse ndi kudzisungira ulemu wachikristu. Ndiyeno mukakhala papulatifomu, mudzatha kulankhula mwachibadwa ndi mosavuta.
Poŵerenga Pamaso pa Anthu. Kuŵerenga mwachibadwa pamaso pa anthu kumalira kulimbikira. Kuti zimenezo zikatheke, zindikirani malingaliro ofunika kwambiri m’nkhani imene mukaiŵerenge, ndipo onani mmene akuwafotokozera. Asungeni m’maganizo kuti musakangoŵerenga mawu okha. Fufuzani katchulidwe koyenera ka mawu osawazoloŵera. Yesezani kuŵerenga mokweza kuti muzoloŵere kusinthasintha mawu ndi kulumikiza mawu moyenerera m’njira yomveketsa bwino malingaliro. Chitani zimenezo mobwerezabwereza kufikira mutakhoza kuŵerenga mwa myaa. Mvetsani bwino nkhaniyo kwakuti poŵerenga muzimveka ngati kukambirana kwaumoyo. Ndiko kulankhula mwachibadwa kumeneko.
Zoona, zimene nthaŵi zambiri timaŵerengera anthu zimakhala zochokera m’zofalitsa zozikidwa pa Baibulo. Kuwonjezera pa mbali zoŵerenga mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, timaŵerenganso malemba mu utumiki wa kumunda ndi pokamba nkhani papulatifomu. Abale amaŵerenga nkhani zophunzira pa Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi pa Phunziro la Buku la Mpingo. Abale ena oyenerera amapatsidwa nkhani zoŵerenga pamisonkhano yaikulu. Kaya mukuŵerenga Baibulo kapena chofalitsa china, ŵerengani mawu ogwidwa okhala m’makoteshoni maka ndi mzimu wake wa mawuwo. Poŵerenga mbali zogwira mawu anthu ena, ziŵerengeni mwaumoyo. Ngati akugwira mawu a anthu osiyanasiyana, siyanitsani mawu anu poŵerenga mawu a munthu aliyense. Chenjezo: Musamafuule kwambiri, koma ŵerengani mwaumoyo ndi mwachibadwa.
Kaŵerengedwe kachibadwa kamakhala m’njira yokambirana. Sikamveka mwa mtundu wachilendo; kamakhala kokhutiritsa.