PHUNZIRO 28
Kukamba Nkhani Mmene Mumalankhulira ndi Anthu
KAŴIRIKAŴIRI anthu amakhala omasuka pokambirana ndi anzawo. Mawu awo amatuluka mwachibadwa. Anthu ena amalankhula kwambiri; ena ndi ofatsirapo. Mulimonsemo, kulankhula mwachibadwa kumakopa chidwi.
Komabe, pofikira munthu amene simum’dziŵa, n’kosayenera kulankhula naye momasuka kwambiri ngati kuti munazoloŵerana naye. Ndipo kumadera ambiri, kukambirana kulikonse ndi munthu wosam’dziŵa kumayamba mwaulemu kwambiri. Mutapereka ulemu woyenererawo, mumayamba kulankhula momasukirapo kenako mumakambirana momasuka.
Polankhula pa pulatifomu, muyeneranso kusamala. Kulankhula momasuka kwambiri kumachepetsa ulemu wa msonkhano wachikristu komanso ukumu wa zimene mukunena. M’zinenero zina, alipo mawu oyenera kutchula polankhula ndi munthu wachikulire, mphunzitsi, mkulu wa boma, kapena kholo. (Onani mawu ogwiritsidwa ntchito pa Machitidwe 7:2 ndi 13:16.) Palinso mawu ena owatchula polankhula ndi mkazi wanu kapena mwamuna wanu kapenanso mnzanu wokondana naye. Ngakhale kuti kalankhulidwe ka papulatifomu sikayenera kukhala komangika kwambiri, kazikhalabe kaulemu.
Komanso, zilipo zinthu zina zimene zingachititse kakambidwe ka munthu kukhala komangika kwambiri. Chimodzi mwa zinthuzo ndi kapangidwe ka masentensi, kapena kuti ziganizo. Pamakhala vuto ngati wokambayo akuyesa kulankhula masentensiwo ndendende mmene alembedwera. Mawu olembedwa kaŵirikaŵiri amatuluka mosiyana ndi ongolankhula. N’zoona kuti pokonzekera nkhani timaifufuza mwa kuŵerenga mawu olembedwa kale. Komanso timakhala ndi autilaini yolembedwa monga maziko a nkhani yathu. Koma ngati m’nkhani yanu mulankhula maganizo ndendende mmene alembedwera, kapena ngati mungoŵerenga pa autilaini yosindikizidwa, kakambidwe kanu sikangamveke mmene mumalankhulira masiku onse. Kuti kakambidwe kanu kamveke mmene mumalankhulira ndi anthu, lankhulani maganizo anu m’mawu anuanu ndipo peŵani masentensi ovuta.
Chofunika china ndi kusinthasintha liŵiro la kalankhulidwe. Wokamba nkhani akamalankhula momangika, kaŵirikaŵiri amatchula mawu molinganizika kwambiri ndipo liŵiro limakhala lofanana m’nkhani yonseyo. M’kukambirana kwa masiku onse, timasinthasintha liŵiro ndipo timapumira mosiyanitsasiyanitsa.
Komabe, pamene mulankhula pamaso pa gulu lalikulu, powonjezera pa kulankhula monga mwa masiku onse, muyeneranso kukweza mawu, kuwonjezera mphamvu ya mawu, kulankhula mwaumoyo kuti mukope chidwi cha omverawo.
Kuti mu utumiki wa kumunda mukalankhule mmene mumalankhulira mwachibadwa, muyenera kuyesetsa kumalankhula bwino masiku onse. Apa sitikutanthauza kuti muyenera kukhala wophunzira kwambiri ayi. Koma ndi chinthu chabwino kukhala ndi chizoloŵezi cholankhula bwino chimene chingapangitse ena kumvetsera mwaulemu zimene munena. Ndi mfundo zimenezo, onani ngati mufunikira kukonza mbali zina pa mfundo zotsatirazi m’kalankhulidwe kanu ka tsiku ndi tsiku.
Pewani mawu osokoneza kalankhulidwe kabwino kapena kotengera anthu amene moyo wawo umanyoza makhalidwe oopa Mulungu. Mogwirizana ndi uphungu wa pa Akolose 3:8, pewani mawu onyoza ndi otukwana. Mawu amene anthu amalankhula mwa masiku onse ali bwino kuwagwiritsa ntchito. Mawu oterowo ndi omasuka kwambiri, koma akhale mawu abwino ndi ololeka.
Pewani kubwerezabwereza mawu amodzimodzi pofotokoza mfundo zosiyanasiyana. Phunzirani kugwiritsa ntchito mawu omveketsa bwino zimene mukutanthauza.
Pewani kuphimba mfundo zabwino ndi mawu ambirimbiri. Khalani ndi chizoloŵezi cholankhula m’mawu osavuta mfundo imene mukufuna kuti akaikumbukire.
Lankhulani m’njira yosonyeza ena ulemu.