Kodi Mungayankhe?
Kodi munayamba mwaganizapo za mmene mungathetsere vuto la kulankhulana mu ukwati wanu kapena mmene mungathandizire ana anu KUKANA anamgoneka? Kodi mungalithandize bwanji bwenzi limene lili lopsinjika mtima? Kodi mungafotokoze bwino umboni umene tili nawo wakuti Mulungu aliko ndi chimene walolera kuipa? Kodi chilombo chofiiritsa cha m’Chivumbulutso chaputala 17 chimaimiranji? Kapena, kodi nthaŵi zina zimakuvutani kupeza chidziŵitso cha nkhani yanu m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki? Tili ndi mavoliyumu ambiri a The Watchtower a zaka zapitazo, 1951-57, 1960-95, ndi Awake! 1984, 85, 87, 1991-95. Chotero kungakhale kothandiza kuwombola mavoliyumu ameneŵa kaamba ka laibulale yanu ngati mulibe. Adzakuthandizani kwambiri pankhani zimenezi. Mtengo wa voliyumu imodzi ndi K72.00 chabe ndipo angaodedwe pakashi kupyolera mumpingo.