Kupeza Okondwerera Kupyolera mu Umboni wa m’Khwalala Wogwira Mtima
1 Yesu analangiza ophunzira ake kufunafuna awo oyenera kumva mbiri yabwino ya Ufumu. (Mat. 10:11) Komabe, m’madera ambiri lerolino, kukukhala kovutirapo kulankhula ndi anthu panyumba pawo. Chotero, kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuti oyenerawo amene angaphonyedwe afikiridwe?
2 Umboni wa m’khwalala ungakhale njira yogwira mtima yopezera anthu ophonyedwa m’ntchito yakunyumba ndi nyumba. Tingachite umboni wa m’khwalala pasiteshoni ya basi, pafupi ndi nyumba zokhala zotetezeredwa kwambiri, m’mapaki a onse, ndi m’malo ena kumene anthu amachitira zinthu zawo zamasiku onse.
3 Pamene umboni wa m’khwalala utchulidwa, ena amachita mantha. Angakhale ozengereza kukhala ndi phande m’ntchito imeneyo chifukwa chakuti amakhala amanyazi kapena amayembekezera kutsutsidwa ndi anthu amene amaipidwa ndi uthenga wa Ufumu. Kaŵirikaŵiri nkhaŵa zimenezi zimakhala zopanda maziko. Awo amene ali ozoloŵera ntchito imeneyi amasimba kuti ili yosavuta mofanana ndi umboni wakunyumba ndi nyumba. Kwenikweni, iwo apeza kuti anthu ochuluka ngozoloŵera kukambitsirana ndi ena m’khwalala pazifukwa zosiyanasiyana, ndipo ena angakonde kwambiri kukambitsirana kapena kumvetsera koposa ndi mmene akanakhalira ngati tikanagogoda pachitseko pawo. Chotero ngati ‘tilimbika mkamwa,’ tingakondwere kwambiri ndi zotsatirapo zake.—1 Ates. 2:2.
4 Kodi ndimotani mmene ntchito ya m’khwalala ingachitidwire mogwira mtima koposa? Kukonzekera bwino lomwe nkofunika. Ŵerengani magazini nthaŵi ikaliko, ndipo sankhani mfundo imodzi kapena ziŵiri zokambitsirana zimene muganiza kuti zidzakondweretsa anthu amene mudzakumana nawo. Ulaliki wa timphindi 30 n’ngwoyenerera. Popeza kuti cholinga ndicho kulankhula ndi ena mwachindunji, sankhani malo kumene anthu ochulukirapo amadutsa nthaŵi zonse. Ngakhale kuti kukhala ndi wofalitsa wina pafupi kuli bwino, kaŵirikaŵiri kugwira ntchito payekhapayekha kumakhala bwino koposa. Ofalitsa amene aimirira pamalo amodzi angakhale ndi chikhoterero cha kutaya nthaŵi akumacheza ndi kusasamala za anthu amene angafune kumvetsera uthenga wa Ufumu.
5 Kuimirira pamalo amodzi ndi kungosonyeza magaziniwo sikuli kogwira mtima monga mmene kulili kuchitapo kanthu mwa kuyamba kuyandikira kwa anthuwo. Yesani kuyang’anizana nawo. Khalani wansangala, waubwenzi, ndi wonena zinthu mwachindunji pamene mukuyesa kuyambitsa kukambitsirana. Nthaŵi zina, mungafunikire kuyenda mapazi oŵerengeka ndi munthuyo pamene mukulankhula naye. Ngati akondwera, gaŵirani magaziniwo. Ngati magazini akanidwa, mungagaŵire trakiti.
6 Kaŵirikaŵiri ndi bwino kukonza ulaliki wachidule wodzutsa funso kapena wopereka ndemanga imene idzadzutsa chikondwerero. Ngati pakhala chikondwerero, lembani dzina la munthuyo, keyala, ndipo mwinamwake ngakhale nambala yake yalamya kotero kuti mungalondole chikondwererocho. Munganene kuti: “Ngati mungafune kuphunzira zambiri, ndingakonde kukuchezerani kunyumba kwanu kapena kupanga makonzedwe akuti Mboni ina itero.”
7 Mkulu wina amene anali kuchita umboni wa m’khwalala anafikira mkazi wina napeza kuti mkaziyo sanakhalepo ndi nthaŵi ya kulankhula ndi Mboni panyumba pake. Analandira buku navomereza kuti mlongo wina akamchezere kunyumba kwake panthaŵi yabwino. Oyenera ambiri angapezedwedi ndi kuthandizidwa ngati tili ogwira mtima mu umboni wa m’khwalala.—Mac. 17:17.