Ulaliki wa Mumsewu Wopindulitsa
1. Kodi ndi njira imodzi iti imene tingatsanzirire Yesu?
1 Pamene Yesu anali padziko lapansi, sanazengereze kulankhula ndi anthu amene anakumana nawo mumsewu ndi m’malo ena. (Luka 9:57-61; Yoh. 4:7) Iye ankafuna kuuza anthu ambiri uthenga wofunika umene anali nawo. Masiku ano, ulaliki wa mumsewu ndi njira yabwino kwambiri yothandizira anthu kupeza nzeru za Mulungu. (Miy. 1:20) Koma kuti ulalikiwu ukhale wopindulitsa, tiziyamba ndi ife kufikira anthu komanso tizikhala ozindikira.
2. Kodi tingatani kuti tiyambe kulankhula ndi anthu polalikira mumsewu?
2 Muziyamba Ndinu Kufikira Anthu: Nthawi zambiri zimakhala bwino kufikira anthu m’malo mongoima kapena kukhala pansi pamalo enaake n’kumadikira kuti anthu odutsa abwere kwa inu. Mukamalankhula ndi munthu, muzimwetulira, muzimuyang’ana nkhope komanso musamachite zinthu mopupuluma. Ngati mukulalikira ndi ofalitsa ena, ndi bwino kuti wofalitsa mmodzi aziimitsa munthu kuti alankhule naye. Mukapeza munthu wachidwi, muzikonza zoti mudzakumane nayenso. Pomaliza kukambirana, m’funseni kuti mungadzakumanenso bwanji ngati n’zotheka. Abale ena amachita ulaliki wa mumsewu pamalo amodzimodzi. Zimenezi zimawathandiza kuti akumanenso ndi anthu amene analankhula nawo kale ndi kupitiriza kuwathandiza kuti chidwi chawo chisathe.
3. Kodi kuzindikira kungatithandize bwanji pochita ulaliki wa mumsewu?
3 Khalani Ozindikira: Mukamachita ulaliki wa mumsewu, muzisankha bwino malo oti muimepo ndiponso munthu woti mulankhule naye. Sikuti muyenera kulankhula ndi munthu wina aliyense ayi. Muziona kaye mmene zinthu zilili. Mwachitsanzo, ngati munthu akuoneka kuti akuthamangira kwinakwake, ndi bwino kungomusiya kuti adutse. Mukamalalikira kutsogolo kwa nyumba yochitiramo malonda, samalani kuti musakhumudwitse eniake malondawo. Nthawi zambiri ndi bwino kulankhula ndi anthu amene akutuluka m’nyumbayo osati amene akufuna kulowa. Pofikira anthu, musamawadzidzimutse kapena kuwachititsa mantha. Komanso muzisamala pogawira anthu mabuku ndi magazini. Ngati munthu sanasonyeze chidwi chenicheni, mungam’patse kapepala m’malo mwa magazini.
4. N’chifukwa chiyani ulaliki wa mumsewu uli njira yopindulitsa ndiponso yosangalatsa yolalikirira?
4 Ulaliki wa mumsewu ndi njira yothandiza kufesa mbewu zambiri za choonadi pa nthawi yochepa. (Mlal. 11:6) Anthu ena amene tingakumane nawo sitingawapeze pakhomo polalikira kunyumba ndi nyumba. Kodi simungayambe kuchita ulaliki wa mumsewu? Ulalikiwu ndi njira yosangalatsa ndiponso yopindulitsa yochitira utumiki wakumunda.