Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/96 tsamba 1
  • Kodi Mwayesa Kuchitira Umboni Kwamadzulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwayesa Kuchitira Umboni Kwamadzulo?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungasinthe Ndandanda Yanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Yesetsani Kumalalikira Madzulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Kufunafuna Anthu Oyenerera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Lalikirani Uthenga Wabwino Paliponse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 7/96 tsamba 1

Kodi Mwayesa Kuchitira Umboni Kwamadzulo?

1 Ife tonse timakondwera pokhala obala zipatso mu ntchito yathu. Komanso, pamene sititha kuona zipatso zabwino, ntchitoyo imakhala yotopetsa ndi yosakhutiritsa. Ntchito yopereka tanthauzo imafupa munthu mwachindunji, ndipo ndiyo dalitso. (Yerekezerani ndi Mlaliki 3:10-13.) Mfundo imeneyi ingagwire ntchito pa ntchito yathu yolalikira. Timadziŵa kuchokera m’zokumana nazo kuti pamene tipita kukhomo ndi khomo ndipo tili okhoza kukambitsirana ndi anthu za Baibulo, timabwerera kwathu tili otsitsimulidwa mwauzimu. Timamva kuti tachitadi kanthu kena.

2 M’madera ena anthu akhala ovuta kuwapeza panyumba pawo mkati mwa maola ena a masana. Malipoti akusonyeza kuti malo ena anthu samapezeka panyumba pamene tifika kuchiyambiyambi kwa tsiku. Mipingo yambiri yalimbana ndi vutoli mwa kupanga makonzedwe a kuchitira umboni kwamadzulo, ndipo achita zimenezi ndi chipambano chabwino. Ofalitsa akusimba kuti pamene apitako tsikulo madzulo, anthu ambiri amakhala ali panyumba, ndipo anthu ambiri amakhala omasuka kwambiri ndi ofunitsitsa kumvetsera uthenga wa Ufumu. Kodi mwayesa kuchitira umboni kwamadzulo m’gawo lanu?—Yerekezerani ndi Marko 1:32-34.

3 Akulu Linganizani Umboni Wamadzulo: M’madera ena misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda dzuŵa litatsala pang’ono kuloŵa kapena kuchiyambiyambi kwa madzulo yachirikizidwa bwino. Ofalitsa achichepere amene amaŵeruka kusukulu masana ndi akulu amene amaŵeruka kuntchito madzulo ayenera kulingaliridwa. Ofalitsa ena amene ali osakhoza kutuluka mu utumiki wakumunda pakutha kwa mlungu amapeza kuti umboni wamadzulo mkati mwa mlungu uli njira yothandiza kwa iwo kuti azikhala ndi phande nthaŵi zonse mu ntchito yolalikira.

4 Pali zochitika zosiyanasiyana zimene mungachite mkati mwa kuchitira umboni kwamadzulo. Mungathe kuchitira umboni kunyumba ndi nyumba ndi magazini kapena kugaŵira buku logaŵira la mweziwo. Madzulo ndi nthaŵi yabwino kwambiri yofikira anthu amene sanali panyumba pamene ofalitsa anafikapo tsikulo kapena pakutha kwa mlungu. Pangakhalenso gawo labwino lochitiramo umboni wa m’khwalala, zikumakulolezani kuonana ndi anthu amene akumka kwawo kuchokera ku ntchito. Ambiri amapeza kuti madzulo ndiyo nthaŵi yabwino koposa ya kupanga maulendo obwereza kwa aja amene anasonyeza chikondwerero.

5 Khalani Ochenjera ndi Anzeru: Kuyenda m’chisisira kapena mumdima kungakhale kwangozi m’madera ena. Kuli kwanzeru kuyenda aŵiriaŵiri kapena m’timagulu mumsewu wamagetsi oyaka bwino ndi kufikira nyumba kapena midadada kokha ngati pali chitsimikiziro chakuti muli otetezereka. Pamene mugogoda pakhomo, imani pamene akhoza kukuonani, ndipo dzidziŵikitseni bwinobwino. Khalani waluntha. Pamene muona kuti mwafika panthaŵi yosayenera, monga ngati pamene banja likudya chakudya, auzeni kuti mudzafika nthaŵi ina. Kaŵirikaŵiri ndi bwino koposa kuchita umboni wanu kumaola oyambirira a madzulo okha, m’malo mwa kufikira anthu usiku kwambiri, pamene eni nyumba angafune kupita kukagona.

6 Pamene tipereka “utumiki wopatulika usana ndi usiku,” Yehova adzadalitsadi zoyesayesa zathu.—Chiv. 7:15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena