Misonkhano Yautumiki ya July
Mlungu Woyambira July 1
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Longosolani lipoti la utumiki wakumunda la April la dziko lathu lino ndi la mpingo.
Mph. 15: “Kukwaniritsa Choŵinda Chathu Tsiku ndi Tsiku.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanimo ndemanga za mu Insight, Voliyumu 2, tsamba 1162, ndime 6-7, mukumasonyeza chifukwa chake choŵinda chili thayo lalikulu.
Mph. 18: “Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima.” (Ndime 1-3) Gwiritsirani ntchito ndime yoyamba kufotokozera mutu wa nkhani. Onani mabrosha amene ali m’stoko pakali pano mumpingo amene mungawagaŵire bwino m’gawo lanu. Ndiyeno fotokozani ndime 2-3 zokha, ndi kusonyeza chitsanzo cha mmene ulendo woyamba ndi ulendo wobwereza ungachitidwire ndi brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Sonyezani mmene ofalitsa angalinganizire ulaliki wa iwo eni pa brosha lina limene lingakhale loyenerana ndi gawolo.
Nyimbo Na. 112 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 8
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima.” (Ndime 4-5) Fotokozani ndime 4-5 zokha ndi mfundo zina za brosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Ndiyeno sonyezani chitsanzo cha maulaliki osonyezedwa a ulendo woyamba ndi ulendo wobwereza.
Mph. 20: “Tapatsidwa Zambiri—Zambiri Zikufunidwa kwa Ife.” Mafunso ndi mayankho. Limbikitsani aliyense kuganiza zolembetsa kukhala mpainiya wothandiza.
Nyimbo Na. 16 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 15
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 20: “Kodi Mwayesa Kuchitira Umboni Kwamadzulo?” Nkhani yokambitsirana ndi omvetsera ndi kufunsa ena. Simbani zimene zaonedwa kwanuko pogwira ntchito m’gawolo madzulo. Phatikizanimo zokumana nazo zosonyeza zipatso zabwino za umboni wamadzulo. Fotokozani za mndandanda wa mlungu ndi mlungu wakumaloko wa misonkhano yokonzekera utumiki.
Mph. 15: “Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima.” (Ndime 6-8) Gwiritsirani ntchito ndime yotsiriza ya nkhaniyi kulimbikitsira onse kupanga maulendo obwereza mwamsanga pa aja amene anagaŵiridwa mabrosha. Sonyezani chitsanzo, mogwiritsira ntchito ndime 6-7, cha mmene munthu angagaŵirire brosha la Chifuno cha Moyo pa ulendo woyamba ndi mmene angayambitsire phunziro m’mutu woyamba wa buku la Chidziŵitso pa ulendo wobwereza. Kumbutsani ofalitsa kuti angathe kudzipangira maulaliki a iwo eni pa mabrosha ena, akumatsatira chitsanzo cha maulaliki oikidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Nyimbo Na. 64 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 22
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Fotokozani mwachidule za makope a magazini atsopano, mukumasonyeza mfundo zokondweretsa zimene zingagwiritsiridwe ntchito polalikira pakhomo. Ndiponso kambitsiranani nkhani yakuti “Pitirizani Kukula m’Chidziŵitso Cholongosoka,” ndipo gogomezerani kufunika kwa kufika pa Phunziro la Buku la Mpingo nthaŵi zonse.
Mph. 15: “Msonkhano Wachigawo wa ‘Amithenga a Mtendere Waumulungu’ wa 1996.” Kufoledwa kwa ndime 1-15 kwa mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 10-11, 14.
Mph. 20: “Mmene Tingapangire Ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso.” Nkhani yofola ndime 12-16 za mphatika ya June 1996. Phatikizanipo zitsanzo ziŵiri za phunziro la Baibulo limene likuchitika. Choyamba chisonyeze mmene tingaphunzitsire wophunzira kukonzekera phunziro mwa kusonyeza kapena kuchonga mfundo zazikulu ndi mawu amene akuyankha mwachindunji mafunso osindikizidwa. Chachiŵiri chisonyeze zimene munganene kuti mulimbikitse wophunzira Baibulo kufika pa Msonkhano Wapoyera ndi pa Phunziro la Nsanja ya Olonda.
Nyimbo Na. 116 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 29
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Fotokozani nkhani yakuti “Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.” Phatikizanipo Bokosi la Mafunso.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa ‘Amithenga a Mtendere Waumulungu’ wa 1996.” Kufoledwa kwa ndime 16-21 kwa mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 16-17. Pendani “Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo.”
Mph. 15: Zosoŵa Zapamalopo. Kapena mkulu akambe nkhani yakuti “Chitonthozo ndi Chilimbikitso—Ngale za Mbali Zambiri,” ya mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996, masamba 21-3.
Nyimbo Na. 165 ndi pemphero lomaliza.