Nyimbo 64
Chikhulupiliro Chonga Chija cha Abrahamu
1. Ngwodala wozindikira
Mawu a Mulungu;
Poti Mulungu adziŵa
Poyamba mapeto.
Kutitonthoza ifeyo,
Mwa anthu akale
Anachita maulosi,
Omveka tsopano.
2. Tawonani Abrahamu,
Ndi Isake naye,
Ali m’Phiri la Moriya;
Ali kuyesedwa.
Yehova anamupempha
Kupatsa mwana’ke
Kuti chifuno cha M’lungu
Chikwaniritsidwe.
3. Abrahamu anatero,
Nakhala chitsanzo
Kuti M’lungu adzatuma
Dipo Mwana wake.
Kodi mukufuna moyo?
Khalani womvera,
Khalani wokhulupira
Monga Abrahamu.