Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/06 tsamba 8
  • Kodi Mungasinthe Ndandanda Yanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungasinthe Ndandanda Yanu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Yesetsani Kumalalikira Madzulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Kodi Mwayesa Kuchitira Umboni Kwamadzulo?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Kufunafuna Anthu Oyenerera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi Mukakhala mu Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 4/06 tsamba 8

Kodi Mungasinthe Ndandanda Yanu?

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kusintha ndandanda yathu yolalikirira?

1 Popeza kuti ndife Akristu oona, tinavomera kuitanidwa kuti tikhale “asodzi a anthu.” (Mat. 4:19) Monga asodzi enieni a nsomba, mwachidziwikire tingapindule kwambiri muntchito yosodza anthu ngati tingamalalikire pamene anthuwo akupezeka pakhomo. Anthu ambiri amakhala pakhomo dzuwa likapendeka. Kawirikawiri amakhala akupumula. Kumidzi anthu amakhala ataweruka kumunda ndipo mwina sangadandaule kulandira alendo. Kodi mungasinthe ndandanda yanu kuti muzipita kukalalikira pa nthawi zimenezo?—1 Akor. 9:23.

2. Kodi ndi njira zina ziti zomwe tingathe kufikira anthu ambiri ndi uthenga wabwino?

2 Ulaliki Wamasana: Tingafikire anthu ambiri ndi uthenga wabwino ngati titakonzeratu zolalikira masana. (Miy. 21:5) Achinyamata angathe kulalikira ataweruka ku sukulu. Ndipo ena angathe kulalikira ataweruka ku ntchito. Magulu ena a phunziro la buku angakonze zokalalikira kwa ola limodzi asanayambe phunziro la buku mlungu uliwonse.

3. Kodi ndi njira zotani zomwe mungalalikirire m’gawo lanu dzuwa litapendeka?

3 Ngati tilalikira kunyumba ndi nyumba dzuwa litapendeka tingathe kulankhula ndi anthu amene sapezeka pakhomo nthawi zambiri. M’madera ambiri, anthu angathe kulalikira mu msewu ndiponso kuchitira umboni m’malo amene mumapezeka anthu ambiri masana. Ndipo anthu ambiri amaona kuti masana ndi nthawi yabwino yopita ku maulendo obwereza ndi kukayambitsa maphunziro a Baibulo.

4. Kodi n’chifukwa chiyani kusamala ndi kuganizira ena kuli kofunika pamene tikulalikira masana?

4 M’pofunika Kusamala: Sibwino kufika pakhomo la munthu pamene eni nyumbayo ali otanganidwa. (Afil. 2:4) Mukatha kulonjerana, nenani mwamsanga chimene mwabwerera. Ngati mwafika pa nthawi yoipa, monga nthawi imene banja likudya, auzeni kuti mudzabweranso nthawi ina. Ganizirani ena nthawi zonse.—Mat. 7:12.

5. Kodi tingapindule motani ngati tilalikira masana?

5 Kulalikira masana kumatipatsa mwayi wolalikira uthenga wabwino kwa anthu ambiri. Kungatipatsenso mwayi wopita muutumiki ndi apainiya othandiza ndiponso apainiya okhazikika. (Aroma 1:12) Kodi mungasinthe ndandanda yanu kuti muchite nawo utumiki umenewu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena