Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi Mukakhala mu Utumiki
M’chaka chautumiki cha 2014 tinathera maola 1,945,487,604 tikulalikira. Zimenezi zikusonyeza kuti timafunitsitsa kugwira ntchito yomwe Yehova watipatsa. (Sal. 110:3; 1 Akor. 15:58) Koma popeza “nthawi yotsalayi yafupika,” kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi tikakhala mu utumiki?—1 Akor. 7:29.
Kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi tikakhala mu utumiki, tiyenera kukhala okonzeka kusintha nthawi imene timalowa mu utumiki. Mwachitsanzo, ngati nthawi zina mukamalalikira pogwiritsa ntchito njira inayake mumatha nthawi yambiri osalankhula ndi munthu, mwina mungafunike kusintha zina ndi zina kuti muzilankhula ndi anthu ambiri. N’zoona kuti zinthu zimasiyana malinga ndi dera. Komabe mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu m’malo ‘momangomenya mphepo.’—1 Akor. 9:26.
Mukamalalikira Kunyumba ndi Nyumba: Ofalitsa ambiri amakonda kulalikira kunyumba ndi nyumba m’mawa. Komabe, anthu ambiri amagwira ntchito tsiku lonse ndipo amapezeka pakhomo madzulo. Ndiye bwanji osayesa kumalalikira madzulo pamene anthu ambiri amapezeka pakhomo? Komanso masana anthu amakhala ali pikitipikiti. Choncho ulaliki wamumsewu kapena wa m’malo a malonda ungakhale wothandiza pa nthawiyi kuposa ulaliki wa kunyumba ndi nyumba.
Mukamalalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri: Matebulo ndi timashelefu tamatayala tiyenera kuikidwa m’malo omwe mumadutsa anthu ambiri m’gawo la mpingo wanu. (Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 2013 tsamba 5.) Ngati pamalo omwe mpingo unakonza kuti aziika tebulo kapena kashelefu kamatayala sipakupezekanso anthu ambiri, Komiti ya Utumiki ya Mpingo ingakonze zoti ofalitsa omwe amachita utumikuwu asunthe n’kukakhala pamalo omwe pamapezeka anthu ambiri.
Mukamachita Maulendo Obwereza Kapena Kuchititsa Maphunziro: Ngati simupeza anthu mukamalalikira pa nthawi inayake, mungachite bwino kukonza zoti pa nthawi imeneyoyo muzipita kumaulendo obwereza kapena kumaphunziro a Baibulo. Mwachitsanzo, ngati anthu ambiri a m’dera lanu amapezeka pakhomo Loweruka m’mawa, mungachite bwino kusintha nthawi yanu kuti muzilalikira kunyumba ndi nyumba m’mawawo, n’kumachititsa maphunziro a Baibulo chakumadzulo. Ngati mwakonza zoti mupite kumaulendo obwereza, m’malo moti nonse mupite gawo limodzi, mungachite bwino kugawana m’magulu angapo n’kupita magawo osiyanasiyana.
Ngakhale kuti timawerengera nthawi yonse yomwe takhala mu utumiki, timasangalala kwambiri ngati takwanitsa kulankhula ndi anthu ambiri pa nthawi yomwe tinali mu utumikiyo. Choncho, ngati mukugwiritsa ntchito njira inayake yolalikira pa nthawi ina koma simukupeza anthu, mungachite bwino kugwiritsa ntchito njira ina. Muzipemphanso Yehova, yemwe ndi “Mwini zokolola” kuti akuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu mukakhala mu utumiki.—Mat. 9:38.