Gwiritsani Ntchito Nthaŵi Yanu Moyenera
1 Aliyense ali ndi nthaŵi yofanana mlungu uliwonse. Nthaŵi imene timathera m’kufalitsa uthenga wabwino ndiyo makamaka ili yofunika kwambiri chifukwa ndi nthaŵi imene tathera mu ntchito yopulumutsa miyoyo. (Aroma 1:16) Timasonyeza kuyamikira kwathu zimenezi mwa kukonzekera bwino utumiki umene wakonzedwa, kufika pa misonkhano ya utumiki nthaŵi yabwino, ndi kupita m’gawo mofulumira. Ndi bwino kulalikira m’malo mochedwa pamsonkhano wa utumiki. Popeza Yehova watiphunzitsa kuti “kalikonse kali ndi nthaŵi yake,” tiyenera kugwiritsa ntchito bwino nthaŵi imene taipatula kuti tikhala mu utumiki.—Mlal. 3:1.
2 Gwiritsani Ntchito Nthaŵi Yanu Mwanzeru:Timapeza madalitso ochuluka pamene titsatira mokhazikika ndandanda imene imatilola kuchita nawo utumiki wakumunda nthaŵi zonse. Kaŵirikaŵiri, zotsatirapo zabwino zimene timapeza mu utumiki ziyenera kugwirizana ndi nthaŵi imene tathera mu utumiki. Mwa kusintha zochita zathu pang’ono, kodi sitingathere nthaŵi yambiri mu utumiki wakumunda? Mwachitsanzo, tikatha kufalitsa magazini Loŵeruka, kodi sitingakhale ndi nthaŵi ina yoti tichite maulendo obwereza angapo? Ngati Lamlungu takhala mu utumiki wakumunda kwa kanthaŵi, kodi sitingathere nthaŵi inanso kupanga maulendo obwereza kapena kuchititsa maphunziro a Baibulo? Kodi kungatheke kuwonjezera umboni wa mumsewu pa ntchito yathu ya kunyumba ndi nyumba? M’njira zimenezi kapena m’njira zina, tikhoza kuwongolera utumiki wathu.
3 Pamene tili mu utumiki, tikhoza kutaya nthaŵi yofunika kwambiri ngati sitili osamala. N’zoona, pamene nyengo sili bwino, kupuma pang’ono kungatitsitsimule ndi kutithandiza kupitirizabe. Komabe, khalani wachikatikati, popeza kupuma kumeneku sikungakhale koyenera nthaŵi zonse.
4 M’zaka zaposachedwapa kwakhala kovuta kwambiri kupeza anthu panyumba. Kuti agwirizane ndi mkhalidwewu, ofalitsa ambiri amachita umboni wawo wa kunyumba ndi nyumba nthaŵi zosiyanasiyana. Bwanji osayesa kuchitira umboni madzulo kusanayambe kuda kapena kutangoyamba kuda?
5 Si bwino ofalitsa kumacheza pamene ali mu ntchito ya m’khwalala. M’malo mwake, imani motalikirana ndipo fikirani anthu kuti muyambe kukambirana nawo. Chotero mudzagwiritsa ntchito nthaŵi moyenera kwambiri ndipo mudzapeza chimwemwe chachikulu m’ntchitoyo.
6 Gwiritsani Ntchito Mipata Yochitira Umboni: Pamene mwininyumba anati sindikufuna, Mboni inafunsa ngati m’nyumbamo munali munthu wina amene angalankhule naye. Izi zinachititsa kukambirana ndi mwamuna wa nyumbayo, amene anakhala akudwala kwa zaka zambiri ndipo kwa nthaŵi yaitali ali pabedi. Chiyembekezo chotchulidwa m’Mawu a Mulungu chinamuyambitsanso kusangalala ndi moyo. Mosakhalitsa anachira nayamba kupezeka pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu, ndi kugaŵana chiyembekezo chake chatsopanocho ndi ena!
7 Mlongo wina wachitsikana anagwiritsa ntchito malingaliro oyamba kupita ku utumiki wakumunda nthaŵi ya Phunziro la Buku la Mpingo isanakwane. Pakhomo lake loyamba, anapeza kamtsikana ka zaka 13 kamene kanamvetsera mwachidwi ndipo kanatenga mabuku. Tsiku lotsatira atapita kusukulu, mlongo wachitsikanayu anakaona kamtsikana kaja. Mosakhalitsa, anakapempha kuti aziphunzira nako Baibulo, ndipo kamtsikanako kanavomera.
8 Nthaŵi Yanu Ikhale Yaphindu: Kutenga mbali mu utumiki wakumunda nthaŵi zonse kumatithandiza kuwonjezera maluso athu polalikira uthenga wabwino. Kodi mungawongolere luso lanu loyambitsa makambitsirano pakhomo mwa kugwiritsa ntchito mawu oyamba ogwira mtima kwambiri? Kodi mungakhale mphunzitsi waluso kwambiri pochititsa phunziro la Baibulo lapanyumba? Mwakutero, mungagwiritsedi ntchito nthaŵi yanu ya mu utumiki moyenera ndi kupanga utumiki wanu kukhala wopindulitsa kwambiri.—1 Tim. 4:16.
9 Popeza kuti “yafupika nthaŵi,” miyoyo yathu iyenera kukhala yodzaza ndi ntchito zachikristu. (1 Akor. 7:29) Pazinthu zathu zofunika kwambiri, nthaŵi ya ku ulaliki iyenera kukhala m’gulu la zinthu zoyambirira. Tiyeni tikhale ndi mbali yaikulu, komanso achangu mu utumiki. Nthaŵi ndi chinthu chofunika chimene Yehova watipatsa. Nthaŵi zonse igwiritseni ntchito mwanzeru ndi moyenera.
[Bokosi patsamba 8]
Onani Malingaliro Aŵa:
◼ Fikani pamsonkhano wa utumiki nthaŵi yabwino.
◼ Mosapambanitsa, gulu lopita ku ulaliki lizikhala lochepa.
◼ Peŵani kuchedwa poloŵa m’gawo.
◼ Loŵani m’gawo pamene anthu ambiri ali panyumba.
◼ Nthaŵi zina yendani nokha ngati mukuona kuti mudzakhalabe wotetezeka potero.
◼ Pangani maulendo obwereza pafupi ndi gawo lanu la kukhomo ndi khomo.
◼ Khalani otanganidwa mu utumiki pamene ena achedwa panyumba ina.
◼ Pamene kuli kotheka, malinga ndi mikhalidwe, lalikirani kwambiri kuposa ola limodzi.