Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/98 tsamba 3-4
  • Khalani Wogwira Mtima mu Utumiki Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Wogwira Mtima mu Utumiki Wanu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Perekani Chisamaliro Chokhazikika ku Chiphunzitso Chanu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Mungapemphe Gawo Lanulanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Gwiritsani Ntchito Nthaŵi Yanu Moyenera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 11/98 tsamba 3-4

Khalani Wogwira Mtima mu Utumiki Wanu

1 Thambo likuda bii, ndipo phokoso loopsa likukulabe mpaka pogonthetsa m’khutu. Mtambo wonga utsi ukutsika. Nchiyani chimenecho kodi? Khamu la dzombe mamiliyoni ambiri likudzasakaziratu dziko! Mkhalidwe umene mneneri Yoweli anaufotokozawu ukukwaniritsidwa lero pantchito yolalikira imene atumiki odzozedwa a Mulungu akuchita limodzi ndi mabwenzi awo, khamu lalikulu.

2 Nsanja ya Olonda ya May 1, 1998, tsamba 11, ndime 19, inati: “Khamu la dzombe lamakono la Mulungu lachitira umboni mosamalitsa ‘m’mudzi’ wa Dziko Lachikristu. (Yow. 2:9) . . . Lidakakwerabe zopinga zonse ndi kuloŵa m’nyumba zambirimbiri, kufikira anthu m’makwalala, ndi kulankhula nawo pafoni, ndi kuonana nawo mwanjira iliyonse yotheka pamene likulengeza uthenga wa Yehova.” Kodi umenewu si mwayi waukulu kugwira nawo ntchito yomwe Mulungu walamula kuti ichitidweyi?

3 Komabe nzosiyana ndi dzombe lenileni, chifukwa ilo cholinga chake nchakungodya basi, pomwe ife monga atumiki a Yehova timada nkhaŵa ndi moyo wa anthu amene timawalalikira. Tikufuna kuthandiza ena kudziŵa choonadi chaulemerero chomwe chili m’Mawu a Mulungu kuti asonkhezereke kuchita zinthu zimene zidzawapulumutsa kosatha. (Yoh. 17:3; 1 Tim. 4:16) Nchifukwa chake tikufuna kukhala ogwira mtima pochita utumiki wathu. Kaya tikugwiritsira ntchito njira yotani polalikira, tiyenera kuona kuti tikulalikira mwanjira ndiponso panthaŵi imene tidzapeza zotulukapo zabwino kwambiri. Popeza kuti “maonekedwe a dziko ili apita,” [“akusintha,” NW], tingachite bwino kuwongolera njira zathu zolalikira ndi zakafikidwe kuti tizikhoza kuchita ntchito yathu mwanjira yobala zipatso kwambiri.—1 Akor. 7:31.

4 Ngakhale kuti timayesetsa kufikira anthu mwanjira zambiri, koma ntchito yakunyumba ndi nyumba ndiyo yopambana mu utumiki wathu. Kodi mukafika panyumba mumaona kuti nthaŵi zambiri simupezapo anthu? Ndiye zimakhumudwitsatu, chifukwa mubwerera nawo uthenga wa Ufumuwo musanawauze! Kodi poteropo mungapange bwanji?

5 Sinthani Nthaŵi Koma Moyenera: Mu Israyeli wa m’zaka za zana loyamba, asodzi ankasodza usiku. Chifukwa chiyani usiku? Ngakhale kuti imeneyo sinali nthaŵi yabwino kwambiri kwa iwowo, inali nthaŵi yabwino kwenikweni yogwira nsomba zambiri. Inali nthaŵi yotulutsa zambiri. Pothirira ndemanga kachitidwe kameneka, Nsanja ya Olonda ya June 15, 1992, inati: “Ifenso tiyenera kupenda gawo lathu kuti tisodze, titero kunena kwake, pamene anthu ambiri ali panyumba ndipo okhoza kulabadira.”

6 Pa Afilipi 4:5, mtumwi Paulo amatikumbutsa kuti ‘kufatsa kwathu kuzindikirike ndi anthu onse.’ Pomvera uphungu wouziridwa umenewu, tikufuna kuchita zinthu panthaŵi yake ndipo moyenera pochita ntchito yathu yolalikira mwachangu ndi mwachimwemwe. Sitikufuna ‘kuleka kuphunzitsa anthu pabwalo ndi kunyumba ndi nyumba,’ koma tikufuna kuchitadi utumiki wathu wakunyumba ndi nyumba panthaŵi yoyenera, imene tingapeze anthu ambiri. (Mac. 20:20) Monga ankachitira asodzi a m’zaka za zana loyamba mu Israyeli, tikufuna ‘kusodza’ panthaŵi zimene zizititheketsa kupeza anthu ambiri, osati panthaŵi zimene zili bwino kwa ife.

7 Ngati mumaona kuti m’gawo lanu pali nthaŵi zina zimene simupeza anthu pakhomo, kodi mungatani kuti nthaŵi imene ofalitsanu munapatula muigwiritse ntchito bwino kwambiri? Mabungwe ena a akulu akhala akukonza zoti gululo lichite utumiki mwanjira zina, monga umboni wamumsewu, kufola gawo labizinesi, kapena kuyenda maulendo obwereza, asanapite kukhomo ndi khomo kunyumba za anthu. Kusinthasintha zinthu ngati zimenezo kungathandize kuwonjezera zotulukapo za ntchito yakukhomo ndi khomo.

8 Khalani Wozindikira ndi Waluso: Tikamaonana ndi anthu kukhomo ndi khomo, amachita mosiyanasiyana akamva uthenga wathu. Eninyumba ena amamvetsera, ena ngamphwayi, ndipo angapo ngamakani kapena aukali. Ponena za awo amakaniwo, patsamba 7 m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba, akutikumbutsa kuti si kuti timafuna “‘kuwina mikangano’ ndi anthu amene samalemekeza chowonadi.” Ngati mwininyumba ali waukali, zingakhale bwino kwambiri kungotembenuka. Sitiyenera kukangana ndi anthu natiwakakamiza kulankhula nafe kapena kuti amvetsere zimene tikunena. Sitimakakamiza anthu kumvetsera uthenga wathu. Kuchita zimenezo si bwino ndipo zingavutitse Mboni zina ndi kudodometsa ntchito yonse.

9  Kuzindikira nkofunikanso poyesayesa kufola bwino gawo lathu. Popeza kuti anthu ambiri sitimawapeza panyumba panthaŵi yoyamba imene tafika, tiyeneranso kuyesetsa kukawafikira kuti tiwauze uthenga wachipulumutso. (Aroma 10:13) Akuti nthaŵi zina ofalitsa ena amafika panyumba imodzimodzi yomweyo kangapo tsiku limodzi poyesayesa kuti akapeze anthu alipo. Zimenezozo anansi awo amaziona. Ndiye zingawapale mkamwa nkuyamba kumanena kuti Mboni za Yehova ‘zimangofikafika’ pakhomo pawo. Kodi zimenezo tingazipeŵe bwanji?

10 Khalani wozindikira. Ngati mwalephera kumpeza munthu mutayesa kamodzi kapena kaŵiri panthaŵi zosiyana patsiku, mwina mungadzampeze panthaŵi ina imene mudzafolanso gawolo.

11 Chitani Zinthu Mwadongosolo ndi Mwaulemu: Titamalinganiza bwino zinthu tingapeŵe kupanga magulu aakulu ocheukitsa anthu amene amasonkhana m’gawo. Eninyumba ena angachite mantha ataona gulu lalikulu la ofalitsa likuyandikira panyumba yawo. Sitifuna kupangitsa anthu kuganiza kuti tabwera “kudzawaukira” m’nyumba zawo. Zokonzekera kukafola gawo zimakhala bwino kwambiri kuzichitira pamalo okumanira popita mu utumiki wakumunda. Magulu aang’ono a ofalitsa, monga banja, sawopseza kwenikweni eninyumba ndipo samafunikira kugaŵidwanso pofola gawolo.

12 Ambiri aona kuti zimawayendera bwino kwambiri pofikira anthu paliponse pamene angapezeke—pamisewu, pamalo oimika magalimoto, ndi m’mabwalo enanso. M’malo onga amenewonso, timafuna kuchitira umboni wabwino, osati mwa mawu athu okha komanso mwa kuchita kwathu zinthu bwino. Ofalitsa a mpingo uliwonse ayenera kutsimikizira kuti sakugwira ntchito m’gawo la mpingo wina kotero kuti asamasoŵetse mtendere anthu oyenda pamsewu kapena ogwira ntchito m’makampani, monga pomwetsera petulo potsegulidwa maola 24. Kuti tichite utumiki wathu mwadongosolo ndi molemekezeka, tisamagwire ntchito kunja kwa gawo limene tinapatsidwa, pokhapokha ngati woyang’anira utumiki wa mumpingo wina wakonza zimenezo kuti tikawathandize. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 10:13-15.)

13 Mipingo ina imene ili ndi madera ambiri omwe amachitiramo umboni kwa anthu onse, inakonza mapu a magawowo. Ndiyeno wofalitsa kapena gulu limapatsidwa khadi lagawo. Zimenezi zimathandizira kulifola bwino kwambiri gawolo ndi kutinso pasakhale ofalitsa ambiri ogwira ntchito pachigawo chimodzi nthaŵi imodzi, kuti tigwiritsire ntchito pulinsipulo la pa 1 Akorinto 14:40, lakuti: “Zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.”

14 Pa 1 Akorinto 9:26, mtumwi Paulo anati: “Ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga.” Potsanzira Paulo, tikufuna kutsimikiza kuchita utumiki mogwira mtima, ndi mobala zipatso. Pamene tikugwira mwachangu ntchito yochitira umboni monga “gulu la dzombe” la Yehova, monga Akristu, tiyeni tizikhala ochita zinthu moyenera ndi ozindikira popereka uthenga wachipulumutso kwa onse a m’dera lathu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena