Mungatani Kuti Msonkhano Wokonzekera Utumiki Uzikhala Wothandiza?
1. Kodi cholinga cha msonkhano wokonzekera utumiki n’chiyani?
1 Pa nthawi ina, Yesu anasonkhana ndi ophunzira ake 70 asananyamuke kupita kokalalikira. (Luka 10:1-11) Pa msonkhanowu, Yesu anawalimbikitsa powauza kuti sadzakhala okha. Anawauzanso kuti Yehova, yemwe ndi “Mwini zokolola,” awatsogolera. Yesu anapatsanso ophunzira akewa malangizo othandiza ndipo kenako anawagawa “awiriawiri.” Masiku anonso timachita msonkhano wokonzekera utumiki. Mofanana ndi nthawi ya Yesu cholinga cha msonkhanowu ndi kutilimbikitsa komanso kutithandiza kuti tizilalikira mwaluso.
2. Kodi msonkhano wokonzekera utumiki uzichitika nthawi yaitali bwanji?
2 Msonkhano wokonzekera utumiki umachitika maminitsi 10 kapena 15. Pa msonkhanowu timapatsidwa woyenda naye, kuuzidwa gawo lomwe tikukalalikira ndipo msonkhanowu umatha ndi pemphero. Koma kuyambira mwezi wa April, msonkhano wokonzekera utumiki uzichitika maminitsi 5 kapena 7. Komabe, ngati msonkhanowu ukuchitika pambuyo pa misonkhano ya mpingo, uyenera kukhala waufupi kuposa pamenepa. Zili choncho chifukwa abale ndi alongo amakhala ataphunzira kale zinthu zambiri. Zimenezi zingathandize kuti anthu azikhala ndi nthawi yambiri yolalikira. Zingathandizenso kuti apainiya kapena ofalitsa amene ayamba kale kulalikira asamasiye kwa nthawi yaitali chifukwa chokhala nawo pa msonkhanowu.
3. Kodi msonkhano wokonzekera utumiki uyenera kuchitika bwanji kuti ukhale wothandiza kwa onse?
3 Msonkhano wokonzekera utumiki uyenera kuchitika m’njira yoti uzikhala wothandiza kwa onse. M’mipingo yambiri, amaona kuti ndi bwino kuti magulu a utumiki wakumunda asamachitire limodzi msonkhanowu. M’malomwake amasonkhana m’magulu awo pamalo osiyanasiyana. Zimenezi zimathandiza kuti ofalitsa asamayende mtunda wautali popita komwe akukachitira msonkhanowu komanso popita kugawo lawo. Zimathandizanso kuti wochititsa msonkhanowu asavutike kugawa anthu. Ubwino winanso ndi woti woyang’anira kagulu amatha kudziwa bwinobwino wofalitsa aliyense wa m’gulu lake. Komabe bungwe la akulu lingasankhe kuti msonkhanowu uzichitika mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa mpingo wawo. Musanamalize msonkhanowu ndi pemphero, aliyense ayenera kukhala atadziwa gawo lomwe mukalalikire komanso munthu amene ayende naye.
4. N’chifukwa chiyani msonkhano wokonzekera utumiki uyenera kuonedwa kuti ndi wofunikanso?
4 Msonkhanowu Ndi Wofunika Ngati Misonkhano Ina Yonse ya Mpingo: Popeza cholinga cha msonkhano wokonzekera utumiki ndi kuthandiza anthu omwe akupita mu utumiki pa tsikulo, nthawi zambiri pa msonkhanowu pamakhala anthu ochepa osati mpingo wonse. Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti msonkhanowu ndi wosafunika kwenikweni poyerekeza ndi misonkhano ina. Mofanana ndi misonkhano yonse, msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda umatipatsa mwayi wolimbikitsana pa chikondi ndi ntchito zabwino. (Aheb. 10:24, 25) Choncho, yemwe akuchititsa msonkhanowu ayenera kukonzekera bwino kuti ukhale wolemekeza Yehova komanso kuti ukhale wothandiza kwa onse omwe akupita kolalikira pa tsikulo. Ngati n’zotheka, wofalitsa aliyense yemwe akupita kolalikira ayenera kupezeka pa msonkhanowu.
Msonkhano wokonzekera utumiki suyenera kuonedwa ngati wosafunika kwenikweni poyerekeza ndi misonkhano ina
5. (a) Kodi woyang’anira utumiki ayenera kukumbukira chiyani akamasankha wochititsa msonkhano wokonzekera utumiki? (b) Kodi mlongo angachititse bwanji msonkhano wokonzekera utumiki?
5 Kodi Wochititsa Msonkhanowu Angakonzekere Bwanji? Kuti munthu akambe bwino nkhani, ayenera kukonzekera bwino. Choncho, ayenera kupatsidwa nkhaniyo padakali nthawi. N’chimodzimodzinso ndi msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda. Yemwe adzachititse msonkhanowu ayenera kukonzekera kudakali nthawi. Magulu a utumiki wakumunda akakhala kuti sachitira limodzi msonkhanowu, oyang’anira magulu kapena othandizira awo, ndi amene amachititsa. Komabe ngati mpingo wonse udzachitire limodzi msonkhanowu, woyang’anira utumiki ayenera kusankha munthu woti adzachititse. Oyang’anira utumiki ena amalemberatu ndandanda ya ochititsa msonkhanowu n’kuwapatsiratu. Ndandanda ina amaiika pa bolodi ya chidziwitso. Woyang’anira utumiki ayenera kusankha bwino munthu wochititsa msonkhanowu. Ayenera kukumbukira kuti, msonkhanowu umakhala wopindulitsa ngati wochititsayo ali ndi luso lophunzitsa komanso amachita zinthu mwadongosolo. Ngati palibe mkulu, mtumiki wothandiza kapena m’bale woyenerera woti adzachititse msonkhanowo, woyang’anira utumiki angasankhe mlongo woyenerera kuti adzachititse.—Onani nkhani yakuti, “Zoyenera Kukumbukira Mlongo Akamachititsa Msonkhano Wokonzekera Utumiki,” patsamba 6.
6. N’chifukwa chiyani munthu yemwe wauzidwa kuti akachititse msonkhano wokonzekera utumiki ayenera kukonzekera bwino?
6 Tikapatsidwa nkhani m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kapena mu Msonkhano wa Utumiki, timaonetsetsa kuti taikonzekera bwino. Timadziwa kuti si bwino kudikira mpaka tsiku la nkhaniyo litakwana, n’kuyamba kuganizira tili m’njira zoti tikanene. N’chimodzimodzinso ngati mwauzidwa kuti mukachititse msonkhano wokonzekera utumiki. Muyenera kukonzekera pasanakhale m’malo mokakonzekerera komweko. Popeza nthawi ya msonkhanowu yachepetsedwa, kukonzekera n’kofunika kuti msonkhanowu uzikhala wothandiza komanso kuti uzitha pa nthawi yake. Muyeneranso kudziwiratu gawo limene mukalalikire.
7. Kodi ndi zinthu ziti zomwe wochititsa msonkhano wokonzekera utumiki angakambirane ndi ofalitsa?
7 Kodi Tingakambirane Chiyani? Popeza madera amasiyanasiyana, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru sanapereke ndandanda ya zinthu zomwe tiyenera kukambirana pa msonkhano wokonzekera utumiki. Bokosi lakuti, “Zimene Mungakambirane pa Msonkhano Wokonzekera Utumiki” lomwe lili patsamba 6, latchula zinthu zina zomwe mungakambirane. Kawirikawiri msonkhanowu umakhala wokambirana. Nthawi zina wochititsayo angakonze zoti pachitike chitsanzo kapena angaonetse vidiyo ya pa webusaiti yathu ya jw.org/ny, yokhudza utumiki. Wochititsa akamakonzekera, aziganizira mfundo zimene zingalimbikitse komanso kuthandiza ofalitsa amene akupita mu utumiki pa tsikulo.
Wochititsa akamakonzekera aziganizira mfundo zimene zingalimbikitse komanso kuthandiza ofalitsa amene akupita mu utumiki pa tsikulo
8. Kodi ndi zinthu ziti zomwe tingakambirane pa msonkhano wokonzekera utumiki Loweruka kapena Lamlungu?
8 Mwachitsanzo, Loweruka ofalitsa ambiri amakonda kugawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ambiri amene amalowa mu utumiki Loweruka angakhale oti salowa mu utumiki mkati mwa mlungu. Choncho, n’kutheka kuti amakhala ataiwala zimene anakonzekera pa Kulambira kwa Pabanja, zoti akanene mu utumiki. Motero, zingakhale bwino kuti amene akuchititsa msonkhano wokonzekera utumiki abwerezenso zitsanzo za ulaliki zomwe zimakhala patsamba lomaliza la Utumiki Wathu wa Ufumu. Ngati ili nthawi ya chikondwerero chinachake, mungakambirane zimene munganene mu utumiki zokhudza chikondwererocho. Mungakambiranenso zimene munganene poyamba kukambirana ndi anthu pogwiritsa ntchito nkhani yomwe yangochitika kumene m’deralo. Njira ina ndi kukambirana funso limene mungamufunse munthu yemwe walandira magazini, kuti mudzaone poyambira ulendo wotsatira. Ngati anthu ena alalikirapo pogwiritsa ntchito magazini omwe mukugawira m’mweziwo, wochititsa msonkhanowu angawapemphe kuti afotokoze zimene akumanena pogawira magaziniwo kapena zosangalatsa zimene akumana nazo. Lamlungu, wochititsa msonkhano wokonzekera utumiki angasankhenso kuchita chimodzimodzi ndi buku kapena kabuku kogawira mweziwo. Mabuku omwe timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu monga buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi kabuku kakuti, Uthenga Wabwino kapena Mverani Mulungu, timawagawira nthawi iliyonse. Choncho, wochititsa msonkhanowu angafotokoze mwachidule mmene tingagawirire mabukuwa.
9. Kodi ndi zinthu ziti zomwe tingakambirane kumapeto kwa mlungu ngati tikugawira kapepala kapadera komanso koitanira anthu kumsonkhano kapena ku Chikumbutso?
9 Ngati ndi kumapeto kwa mlungu ndipo mpingo ukugawira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso, kumsonkhano kapena kapepala kapadera, wochititsa msonkhano wokonzekera utumiki angafotokoze mmene tingagawirire kapepalako limodzi ndi magazini a mweziwo. Angafotokozenso zimene tingachite ngati takumana ndi munthu yemwe akufuna kudziwa zambiri. Akhozanso kufotokoza zinthu zomwe zinachitika zosonyeza kufunika kogawira timapepalati.
10, 11. N’chifukwa chiyani ofalitsa ayenera kukonzekera bwino msonkhano wokonzekera utumiki?
10 Kodi Ofalitsa Angakonzekere Bwanji? Ofalitsa nawonso angathandize kuti msonkhano wokonzekera utumiki ukhale wothandiza. Mwachitsanzo atakhala kuti anakonzekera msonkhanowu pa kulambira kwawo kwa pabanja, anganene mfundo zimene zingathandize ofalitsa ena. Ofalitsa ayeneranso kutengeratu magazini komanso mabuku omwe akufuna kukagawira, msonkhano wokonzekera utumiki usanayambe. Zimenezi zingathandize kuti msonkhanowu ukangotha, anyamuke nthawi yomweyo.
11 Ndi bwinonso kufika msonkhanowu usanayambe. N’zoona kuti timasokoneza ena tikafika mochedwa pa misonkhano yonse ya mpingo. Komabe zimasokoneza kwambiri ngati tafika mochedwa pa msonkhano wokonzekera utumiki. Zili choncho chifukwa m’bale yemwe akuchititsa msonkhanowu amaganizira mfundo zingapo akamagawa anthu kuti alowe mu utumiki. Mwachitsanzo, ngati waona kuti pali ofalitsa ochepa, angaganize zoti onsewo akalalikire m’gawo lomwe linayambidwa kale. Ngati pali anthu ena omwe ayenda pansi ulendo wautali pobwera ku msonkhanowu, ndipo gawo lomwe mukukalalikira ndi lakutali, wochititsayo angaone kuti ndi bwino kuwagawa anthu oterewa, ndi omwe ali ndi magalimoto. Ngati gawo lomwe mukukalalikira lili loopsa, wochititsayo angagawe abale ena kuti ayende ndi alongo kapena angakonze zoti kagulu ka abale kapitenso kugawo lomwelo. Ofalitsa omwe akudwala kapena okalamba angauzidwe kuti alalikire gawo lapafupi kapena kudera komwe kulibe zitunda. Wochititsa msonkhano wokonzekera utumiki akhozanso kukonza zoti ofalitsa atsopano agawidwe ndi ofalitsa aluso. Koma ngati tafika pa msonkhanowo mochedwa, zingapangitse kuti wochititsayo asinthenso zimene anakonza kale. N’zoona kuti nthawi zina timachedwa pa zifukwa zomveka. Komabe ngati tili ndi chizolowezi chochedwa, mwina n’chifukwa choti sitiyamikira msonkhanowo kapena sitichita zinthu mwadongosolo.
12. Kodi muyenera kuganizira chiyani musanapangane ndi munthu woti muyende naye?
12 Tikhoza kupangana ndi munthu woti tiyende naye, kapena wochititsa msonkhanowu akhoza kutigawira woti tiyende naye. Komabe si bwino kumangoyenda ndi munthu yemweyemweyo. (2 Akor. 6:11-13) Ndi bwinonso kuyenda ndi ofalitsa atsopano kuti tiwathandize kuti azilalikira mwaluso. (1 Akor. 10:24; 1 Tim. 4:13, 15) Muzimvetsera mwatcheru wochititsa msonkhano wokonzekera utumiki akamapereka malangizo, kuphatikizapo onena za gawo limene mukayambire kulalikira. Msonkhanowu ukatha, musasinthe zimene wochititsa msonkhano wanena ndipo muyenera kunyamuka nthawi yomweyo.
13. Kodi kukonzekera bwino msonkhano wokonzekera utumiki n’kothandiza bwanji?
13 Ophunzira 70 aja, amene Yesu anawatumiza kuti akalalikire, “anabwerera ali osangalala.” (Luka 10:17) N’zosakayikitsa kuti msonkhano wokonzekera utumiki umene Yesu anachita nawo asananyamuke, ndi umene unawathandiza. Masiku anonso, tonse tikamakonzekera bwino, msonkhano wokonzekera utumiki, msonkhanowu ungakhale wolimbikitsa komanso wothandiza kwambiri. Izi zingachititse kuti tithe kukwaniritsa ntchito yathu yochitira “umboni ku mitundu yonse.”—Mat. 24:14.