Bokosi la Mafunso
◼ Kodi pamisonkhano yokonzekera utumiki wakumunda azikambapo zotani?
Cholinga cha msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda ndicho kutithandiza kuika maganizo pa ntchito imene tikukagwira, ya utumiki. Choncho, wochititsa msonkhanowu azikonzekera bwino ndipo azikhala wokonzeka kunena mfundo yolimbikitsa, yachindunji, ndi yothandiza. Ngati lemba la tsiku limenelo likukhudza kwambiri ntchito yolalikira, mungaliŵerenge ndi kulikambirana mwachidule. Komabe, msonkhanowo uzikhala kwenikweni wokambirana ntchito ya utumiki kuti uthandize anthu amene akupita kuulaliki tsiku limenelo kukonzekera bwino kukwaniritsa utumiki.—2 Tim. 4:5.
Mungakambirane mfundo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu zofunika kuzigwiritsa ntchito pothandiza onse kudziŵa mabuku ofunika kugaŵira nthaŵiyo ndiponso zimene angachite pogaŵira. Tsiku la ulaliki wa magazini mungasonyeze chitsanzo cha ulaliki kuchokera pa “Zoyenera Kunena Pogaŵira Magazini.” Pa ndawala zina, mungatsindike mawu oyamba amodzi kapena aŵiri a m’buku la Kukambitsirana amene angagwire ntchito m’gawolo. Mungathe kukambirana kapena kusonyeza chitsanzo cha mbali ina ya utumiki, monga momwe tingagwiritsire ntchito Baibulo pakhomo la munthu, momwe tingachitire ndi anthu oimitsa kukambirana, momwe tingapemphere anthu kuphunzira nafe Baibulo, kapena momwe tingapitire kwa anthu amene anasonyeza chidwi.
Misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda isamatenge nthaŵi yopitirira mphindi 10 kapena 15, zimene zikuphatikizapo kugaŵa gululo, kutchula gawo, ndiponso kupemphera. Pamene mukubalalika, onse pagululo azikhala akudziŵa woyenda naye ndiponso kumene akalalikire, ndipo azinyamuka mwamsanga. Popeza msonkhanowu ndi wanthaŵi yochepa, n’kofunika kuti anthu onse azifika panthaŵi yake. Msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda uzikhala wachidule ngati umachitika pamapeto pamsonkhano wampingo, monga Phunziro la Nsanja ya Olonda. Sikofunika kukambirana lemba latsiku, popeza zinthu zabwino za m’Malemba takambirana kale.
Abale obatizidwa komanso oyeneretsedwa aziuzidwiratu tsiku limene adzachititse msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda. Akulu asankhe alongo obatizidwa omwe angachititse msonkhanowo tsiku limene palibe abale omwe angatsogolere. Mlongo amene achititse msonkhanowo angatsogolere gululo kukambirana lemba la tsikulo kapena mfundo zina zogwirizana ndi utumiki wakumunda atakhala pansi komanso asachulutse zonena. Ayenera kuvala duku.
Misonkhano yautumiki wakumunda ndi nthaŵi yabwino kwambiri, yotilimbikitsa ndi kutikonzekeretsa kutumikira. Wochititsa msonkhanowu akakonzekera bwino, onse amapindula kwambiri.