Pindulani Mokwanira ndi Misonkhano Yokonzekera Utumiki wa Kumunda
1. Kodi misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda ingatithandize bwanji?
1 Misonkhano yogwira mtima yokonzekera utumiki wa kumunda imatilimbikitsa ndiponso imatipatsa malangizo othandiza tisanapite mu utumiki. Imatithandiza kuti tizilalikira monga gulu n’cholinga choti tizilimbikitsana komanso kuphunzitsana. (Miy. 27:17; Mlal. 4:9, 10) Kodi tingatani kuti tizipindula mokwanira ndi misonkhano imeneyi?
2. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene wochititsa msonkhano angaziganizire?
2 Wochititsa: Nthawi zambiri sipakhala nkhani yolembedweratu yoti izikambidwa pa misonkhano imeneyi. Choncho, kukonzekera bwino n’kofunika ngati muli wochititsa msonkhano umenewu. Si bwino kuti nthawi zonse muzikambirana lemba la tsiku, ngakhale kuti nthawi zina mungasankhe kulikambirana ngati mfundo zake zikugwirizana ndi utumiki wa kumunda. Ganizirani zimene zingawathandizedi anthu amene akukalalikira tsiku limenelo. Mwachitsanzo, mungalongosole kapena kuchita chitsanzo cha mmene ulaliki ungachitikire. Mungasankhenso kukambirana mfundo zina za m’buku la Kukambitsirana, Sukulu ya Utumiki, kapena mfundo zaposachedwapa za mu Msonkhano wa Utumiki. Pa nthawi zina, mukhoza kukambirana mmene mungachitire mutakumana ndi vuto m’gawo lanu. Kapena, mungakambirane mmene mungakulitsire chidwi ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo, makamaka ngati anthu ambiri akupita ku maulendo obwereza. Kaya musankha kukambirana mfundo zotani, zikambeni mwaumoyo ndi molimbikitsa.
3. Kodi msonkhanowu uzikhala wautali bwanji, ndipo ndi zinthu ziti zimene ziyenera kuchitika pa msonkhanowo?
3 Yambani msonkhanowo pa nthawi yake, ngakhale mukudziwa kuti anthu ena afika mochedwa. Chitani mwanzeru pogawa anthu opita mu utumiki, ndipo auzeni gawo loti apite ngati pangafunike kutero. Msonkhanowu usapitirire mphindi 10 kapena 15, ndipo uzikhala wofupikirapo ngati ukuchitika mutangomaliza kumene msonkhano wampingo. Msonkhanowo usanathe, aliyense adziwe yemwe akuyenda naye ndiponso komwe akalalikire. Msonkhanowu uzitha ndi pemphero.
4. Kodi n’chiyani chomwe chingathandize anthu onse kuti apindule mokwanira ndi msonkhano wokonzekera utumiki wa kumunda?
4 Mukhoza Kuthandiza: Monga mmene timachitira pa misonkhano ya mpingo, timasonyeza kuti timalemekeza Yehova ndiponso kuganizira ena mwa kufika panthawi yake. Muzilankhulapo pa makambiranowo. Mungalole wochititsa msonkhano kuti akupatseni munthu woyenda naye, kapena mungakonzeretu zoyenda ndi winawake msonkhanowo usanayambe. Ngati mungakonde kupeza nokha woyenda naye, yesetsani ‘kukulitsidwa’ mwa kulalikira ndi ofalitsa osiyanasiyana, m’malo mongoyenda ndi anzanu okhaokha nthawi zonse. (2 Akor. 6:11-13) Msonkhano ukangotha, pewani kusintha makonzedwe amene apangidwa, ndipo nyamukani nthawi yomweyo kupita ku gawo lanu.
5. Kodi cholinga cha misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda n’chiyani?
5 Cholinga cha misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda n’chofanana ndi cha misonkhano yampingo. Misonkhano imeneyi imakonzedwa n’cholinga choti “tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.” (Aheb. 10:24, 25) Ngati titamayesetsa kupindula ndi misonkhano imeneyi, tidzathandizidwa kukwaniritsa utumiki wathu, umene ulidi ‘ntchito yabwino’!