Lemba la Tsiku Silizigwiritsidwanso Ntchito pa Msonkhano Wokonzekera Utumiki Wakumunda
M’mbuyomu, pamsonkhano wokonzekera utumiki wakumunda tinkakambirana lemba tsiku ngati likukamba za utumiki. Tsopano pali kusintha. Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku sikazigwiritsidwanso ntchito ngati maziko a zokambirana zokonzekera utumiki. Monga mmene zinalili poyamba, amene akutsogolera zokambiranazo angagwiritse ntchito Baibulo, Utumiki Wathu wa Ufumu, buku la Sukulu ya Utumiki, buku la Kukambitsirana ndi buku lililonse lokamba za utumiki. Amene apatsidwa mbali imeneyi ayenera kukonzekera mfundo zimene zingathandize amene akulowa mu utumiki tsiku limenelo. Ndipo monga takhala tikuchitira m’mbuyomu, msonkhanowu uyenera kutenga mphindi 10 kapena 15 ndipo uzikhala wofupikirapo ngati ukuchitika pambuyo pa misonkhano ya mpingo.