Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda
1. N’chifukwa chiyani timafunika kukhala ndi dongosolo labwino lolowera mu utumiki wakumunda?
1 Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino pankhani yolalikira Ufumu mwadongosolo ndiponso mogwira mtima. Masiku anonso, anthu amene ali ndi udindo woyang’anira ntchito yolalikira Ufumu padziko lonse amafunitsitsa kuti ntchitoyi izichitika ngati mmene inkachitikira panthawiyo. Mogwirizana ndi zimenezi, mipingo padziko lonse imakhala ndi misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda monga njira yokonzekeretsera magulu a ofalitsa Ufumu.—Mat. 24:45-47; 25:21; Luka 10:1-7.
2. Kodi misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda iyenera kuchitika motani?
2 Dongosolo Labwino: Misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda imakonzedwa ndi cholinga cholimbikitsa ndiponso kupereka malangizo othandiza kwa anthu amene akufuna kulowa mu utumiki wakumunda. Mungakambirane lemba la tsiku mwachidule ngati mfundo zake zili zogwirizana ndi utumiki wakumunda. Nthawi zina, mungakambirane mfundo zopezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu, m’buku la Kukambitsirana kapena la Sukulu ya Utumiki pokonzekeretsa anthu amene abwera kudzalowa mu utumiki tsiku limenelo. Mungachitenso chitsanzo chachidule chosonyeza zimene munganene pogawira buku kapena magazini a mweziwo. Pemphero lisanaperekedwe, aliyense ayenera kudziwa amene ayende naye komanso gawo limene akalalikire tsiku limenelo. Msonkhano umenewu suyenera kuposa mphindi 15 ndipo ukatha, aliyense ayenera kunyamuka kupita ku gawo lolalikira.
3. Kodi ndani ali ndi udindo wolinganiza misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda?
3 Kodi Imakonzedwa Bwanji? Popeza woyang’anira utumiki ndi amene amatsogolera ntchito yolalikira, ndi udindo wake kulinganiza misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda. Oyang’anira timagulu kapena owathandiza ali ndi udindo woyenda limodzi ndi gulu lawo la utumiki wakumunda kumapeto kwa mlungu. Akulu ena kapena atumiki othandiza angathe kuyendera limodzi ndi timagulu ta utumiki wakumunda mkati mwa mlungu. Oyang’anira timagulu ayenera kugwira ntchito limodzi ndi woyang’anira utumiki n’cholinga chakuti akhale ndi gawo lokwanira loti kagulu kawo kazilalikirako nyumba ndi nyumba kumapeto a mlungu. Woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti pali m’bale wotsogolera timagulu mu utumiki wakumunda mkati mwa mlungu.
4-6. (a) Kodi cholinga cha misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda n’chiyani tikaganizira za gawo la mpingo? (b) Kodi n’chiyani chimene tiyenera kuganizira tikafuna kusankha nthawi ndi malo ochitira misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda?
4 Malo Amene Mungachitire Misonkhanoyi Komanso Nthawi Yake: M’malo moti mpingo wonse usonkhane pamalo amodzi, zingakhale bwino ngati misonkhano imeneyi ingamachitikire m’malo osiyanasiyana m’gawolo, mwina m’nyumba za abale, n’cholinga choti muzilalikira mokwanira gawo lonse la mpingo. Mungathenso kuchitira misonkhano imeneyi pa Nyumba ya Ufumu. Lamlungu, mipingo yambiri imachita misonkhano yokonzera utumiki wakumunda pa Nyumba ya Ufumu ikangomaliza nkhani ya onse ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda. Muyenera kuonetsetsa kuti abale asamayende mtunda wautali asanafike ku gawo. Choncho, nthawi ndi nthawi muyenera kuganiziranso malo amene abale amakumana pokonzekera misonkhanoyi ndi cholinga choti muone ngati malowo akuthandiza mpingo kulalikira gawo lanu lonse mokwanira.
5 Mungathe kusankha nthawi yochitira misonkhanoyi komanso kuti muzichita kangati pamlungu malinga ndi mmene gawo lanu lilili. Mafunso otsatirawa angakuthandizeni kudziwa malo komanso nthawi yabwino yochitira misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda.
6 Kodi ndi mbali iti ya gawo lanu imene mufunikira kulalikira kwambiri? Kodi nthawi yabwino yochitira ulaliki wa ku nyumba ndi nyumba ndi iti? Kodi zingakhale bwino kusankha nthawi ya kumadzulo kuti muzilalikira nyumba ndi nyumba ndi kupanga maulendo obwereza? Dongosolo lonse lolowera mu utumiki wakumunda liyenera kuikidwa pa bolodi la chidziwitso la mpingo. Ofalitsa Ufumu onse ayenera kukhala ofunitsitsa kulalikira gawo lawo lonse kuti nafenso tidzathe kunena monga mmene mtumwi Paulo ananenera kuti: ‘Tsopano kulibenso gawo limene sindinafikeko.’—Aroma 15:23.
7. Kodi amene wasankhidwa kuti achititse msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda ali ndi udindo wotani?
7 Kuchititsa Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda: M’bale amene akuchititsa msonkhanowu ayenera kukonzekera bwino posonyeza kuti akulemekeza dongosolo la Mulungu limeneli. Misonkhano imeneyi iyenera kuyamba panthawi yake ndipo izikhala yothandiza komanso yachidule. Izitenga mphindi 10 mpaka 15. Msonkhanowu usanayambe, yemwe akuchititsa ayenera kudziwiratu gawo limene kaguluko kayenera kulalikirako. Ngakhale kuti msonkhanowu ukatha simufunikira kuyembekezera obwera mochedwa, mungachite bwino kusiya uthenga wowathandiza kudziwa gawo limene gululo likulalikira. Msonkhanowu ukangotha, aliyense ayenera kunyamuka kupita kugawo limene akalalikire. Msonkhano wokonzedwa bwino ndiponso wokhala ndi malangizo othandiza udzachititsa kuti ofalitsa onse amene abwera adziwe bwino mmene achitire utumiki wa tsikulo.—Miy. 11:14.
8. Kodi ofalitsa angatsatire motani dongosolo limene lakonzedwa ndi amene akutsogolera kagulu ka utumiki wakumunda?
8 Kupezeka pa Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda: Tifunika kutsatira dongosolo limene lakonzedwa. (Aheb. 13:17) Ngati n’kotheka, amene akutsogolera kaguluko angathandize aliyense amene akufuna wina woyenda naye. Ndi bwino kuti ofalitsa ozolowera kulalikira azipezeka pa misonkhano imeneyi n’cholinga choti azithandiza ofalitsa atsopano amene sanazolowere kulalikira. Abale ndi alongo amene amakhala okonzeka kuyenda ndi ofalitsa osiyanasiyana, angathe kuthandiza anthu ambiri. (Miy. 27:17; Aroma 15:1, 2) Tonse tiyenera kuyesetsa kufika pamisonkhano imeneyi panthawi yake. Kulemekeza dongosolo la Mulungu limeneli ndiponso kuganizira antchito anzathu kungatithandize kugwirizana ndi malangizo amenewa.—2 Akor. 6:3, 4; Afil. 2:4.
9. Kodi ndi zinthu zofunika ziti zimene apainiya angachite kuti athandize dongosolo limeneli?
9 Apainiya Angathandize: Apainiya akamapezeka pa misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda amathandiza ndi kulimbikitsa ena onse. N’zoona kuti apainiya amakhala ndi zochita zambiri. Kuwonjezera pa kuchititsa maphunziro a Baibulo ndiponso kuchita maulendo obwereza, iwo angafunikenso kusamalira banja mwinanso kugwira ntchito yolembedwa. Choncho, apainiya asamakakamizike kupezeka pa msonkhano uliwonse wokonzekera utumiki wakumunda umene mpingo wakonza, makamaka ngati misonkhanoyi imachitika tsiku ndi tsiku. Komabe, n’zotheka kuti apainiya azipezeka pa misonkhano ingapo mlungu uliwonse. Misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda imathandiza kuphunzitsa ofalitsa mumpingo. Ndipo apainiya amathandiza kwambiri ena chifukwa amalidziwa bwino Baibulo ndiponso akhala akugwira ntchitoyi nthawi yaitali. Iwo amadziwa zambiri zoyenera kuchita mu utumiki wakumunda chifukwa amalalikira pafupipafupi. Choncho angathe kugawana ndi ena zimene akudziwazo. Iwo ndi chitsanzo choyenera kutengera chifukwa nthawi zambiri amapezeka mu utumiki wakumunda ndiponso pamisonkhano yokonzekera utumiki wakumunda. Ndipo timawayamikira kwambiri chifukwa chotenga mbali pamisonkhano imeneyi.
10. Kodi n’chifukwa chiyani ofalitsa Ufumu onse ayenera kuchirikiza dongosolo limeneli ndi mtima wonse?
10 Mofanana ndi mmene zinalili ndi Yesu komanso ophunzira ake, mbali yaikulu ya ntchito yathu yolalikira Ufumu imachitidwa mwa kulalikira ku nyumba ndi nyumba. Cholinga cha misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda ndicho kulimbikitsana ndiponso kuti tonse tizitha kugwira ntchito imeneyi mokwanira. Ofalitsa uthenga wabwino onse ayenera kuchirikiza dongosolo la Mulungu limeneli mmene angathere. (Mac. 5:42; 20:20) Tiyeni tonse tithandize dongosolo limeneli ndi mtima wonse. Tikamachita zimenezi pamene tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, Yehova adzatidalitsa ndipo tidzasangalatsa Mtsogoleri wathu, Yesu Khristu.—Mat. 25:34-40; 28:19, 20.