Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/12 tsamba 5-6
  • Zimene Mungachite Kuti Muzipindula ndi Kagulu Kanu ka Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Muzipindula ndi Kagulu Kanu ka Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Mungatani Kuti Msonkhano Wokonzekera Utumiki Uzikhala Wothandiza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Ulaliki Wagulu Umasangalatsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Mmene Phunziro la Buku la Mpingo Limatithandizira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 10/12 tsamba 5-6

Zimene Mungachite Kuti Muzipindula ndi Kagulu Kanu ka Utumiki

1. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinkachitika ku Phunziro la Buku la Mpingo zomwe zikuchitikabe m’magulu a utumiki wakumunda?

1 Kodi pali zinthu zimene mumazilakalaka kwambiri zomwe zinkachitika ku Phunziro la Buku la Mpingo? Mwachitsanzo, pa phunziroli pankakhala anthu ochepa ndipo anthuwo ankadziwana bwino. Zimenezi zinkachititsa kuti anthu azigwirizana komanso kulimbikitsana mwauzimu. (Miy. 18:24) Woyang’anira phunziro la buku ankatha kudziwa bwino mmene zinthu zilili pa moyo wa wina aliyense komanso mmene angamulimbikitsire. (Miy. 27:23; 1 Pet. 5:2, 3) Zinthu zimenezi zikuchitikabe m’magulu athu a utumiki wakumunda.

2. Kodi ifeyo tingachite chiyani kuti anthu a m’kagulu kathu ka utumiki azikondana ndiponso kulimbikitsana mwauzimu?

2 Muziyamba Ndi Inuyo Kuchitapo Kanthu: Anthu amene amakhala m’kagulu ka utumiki wakumunda amakhala ochepa mofanana ndi amene ankakhala m’kagulu ka phunziro la buku. Tikamalowa mu utumiki “pamodzi” ndi ena, timayamba kukondana nawo kwambiri. (Afil. 1:27) Kodi inuyo, mwalowapo mu utumiki ndi anthu angati m’gulu lanu? Kodi mungayesetse kumalowa mu utumiki ndi anthu osiyanasiyana? (2 Akor. 6:13) Kuwonjezera pamenepa, nthawi zina tikhoza kumaitana anthu ena a m’kagulu kathu kuti adzakhale nawo tikamachita Kulambira kwa Pabanja kapena kudzadya nawo chakudya. M’mipingo ina, timagulu ta atumiki wakumunda timasinthana pochereza mlendo amene wabwera kudzakamba nkhani mumpingowo. Pamlungu umene kaguluko kakufunika kuchereza mlendoyo, abale ndi alongo a m’kaguluko amasonkhana kuti adyere limodzi chakudya komanso kulimbikitsana, ngakhale mlendoyo atalephera kupezekapo.

3. Kodi kukagulu ka utumiki kumapezeka mipata yotani yoti mungalimbikitsidwe?

3 Ngakhale kuti masiku ano mpingo umasonkhana kawiri kokha pa mlungu, zimenezi si zikutanthauza kuti tsopano pali mipata yochepa yoti mungalimbikitsidwe mwauzimu. Pa kagulu kalikonse ka utumiki, pali m’bale woyang’anira kaguluko amene amalimbikitsa wofalitsa aliyense payekha komanso kumuthandiza pa ntchito yolalikira. Ngati woyang’anira kagulu kanu sanakupemphenipo kuti muyende naye mu utumiki, inuyo mungachite bwino kumupempha kuti muyende naye. Komanso, woyang’anira utumiki amalowa mu utumiki ndi timagulu tosiyanasiyana kamodzi mwezi uliwonse. M’mipingo ing’onoing’ono yomwe ili ndi timagulu tochepa, woyang’anira utumiki angakonze zoti aziyendera kagulu kalikonse kawiri pa chaka. Kodi mumayesetsa kulowa mu utumiki pa nthawi imene woyang’anira utumiki akuchezera kagulu kanu?

4. (a) Kodi misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda imachitika bwanji? (b) N’chifukwa chiyani tingachite bwino kuganizira zoti msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda uzichitikira panyumba yathu?

4 Nthawi zambiri zimakhala bwino kuti kagulu kalikonse kazikumana pakokha pokonzekera utumiki wakumunda Loweruka ndi Lamlungu. Ngati kagulu katakhala ndi malo angapo okonzekerera utumiki pa nthawi imene amalowa mu utumiki nthawi zonse, zingakhale bwino kwambiri. Zimenezi zingathandize kuti ofalitsa asamayende mtunda wautali kupita kumalo okonzekerera komanso kugawo lokalalikira. Ngati kaguluko kamakumana pakokha pokonzekera utumiki wakumunda, zimathandizanso woyang’anira kaguluko kuti azitha kuyang’anira bwino anthu a m’kagulu kake. Komabe, nthawi zina zinthu zina zingachititse kuti timagulu tiwiri kapena toposerapo tiphatikizane. Ngati mpingo wonse umakumana pamodzi pokonzekera utumiki Loweruka loyamba la mwezi uliwonse kapena pambuyo pa Phunziro la Nsanja ya Olonda, nthawi zambiri zimakhala bwino kuti woyang’anira kagulu aliyense apatsidwe kanthawi pang’ono kuti agawe ofalitsa a m’kagulu kake, pemphero lomaliza lisanaperekedwe.—Onani bokosi lakuti, “Kodi Msonkhano Wokonzekera Utumiki Ungamachitikire Panyumba Yanu?”

5. Ngakhale kuti Phunziro la Buku la Mpingo linatha, kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

5 Ngakhale kuti Phunziro la Buku la Mpingo linatha, Yehova akupitirizabe kutipatsa zinthu zonse zimene tikufunikira kuti tichite chifuniro chake. (Aheb. 13:20, 21) Popeza Yehova ndi amene amatisamalira, sitisowa kanthu. (Sal. 23:1) Pali madalitso ambiri amene tingapeze kukagulu kathu ka utumiki wakumunda. Chotero ngati ifeyo ‘titabzala mowolowa manja, tidzakololanso zochuluka.’—2 Akor. 9:6.

[Bokosi patsamba 6]

Kodi Msonkhano Wokonzekera Utumiki Ungamachitikire Panyumba Yanu?

Mipingo ina imaphatikiza timagulu ta utumiki kuti ikonzekere utumiki Loweruka ndi Lamlungu chifukwa chosowa malo amene angakonzekerere. Popeza misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda ndi mbali ya zochitika za mpingo, kugwiritsa ntchito nyumba yanu kuchitiramo misonkhanoyi ndi chinthu cha mtengo wapatali. Kodi n’zotheka kuti msonkhanowu uzichitikira kunyumba kwanu? Musachite manyazi chifukwa choganiza kuti nyumba yanu si yooneka bwino. Akulu adzaganizira za malo amene kuli nyumba yanuyo ndi zinthu zina zofanana ndi zimene ankaona akafuna kusankha malo ochitira phunziro la buku. Chotero dziwitsani woyang’anira kagulu ka utumiki kanu ngati mungafune kuti Msonkhano Wokonzekera Utumiki uzichitikira panyumba yanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena