Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/03 tsamba 1
  • Ulaliki Wagulu Umasangalatsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulaliki Wagulu Umasangalatsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mungachite Kuti Muzipindula ndi Kagulu Kanu ka Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Mungatani Kuti Msonkhano Wokonzekera Utumiki Uzikhala Wothandiza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 7/03 tsamba 1

Ulaliki Wagulu Umasangalatsa

1 Pamene Yesu amatumiza ophunzira ake 70 kupita kokalalikira, anawaphunzitsa zokanena, anawaika aŵiriaŵiri, ndipo anawapatsa gawo loti akalalikiremo. Zimenezi n’zimene zinapangitsa kuti asangalale ndi ntchito yawo. (Luka 10:1-17) N’chimodzimodzinso masiku ano. Ulaliki wagulu umathandiza kuphunzitsa, kukonzekeretsa, ndi kulimbikitsa anthu a Mulungu mu ntchito yolalikira.

2 Akulu Amatsogolera: Akulu ali ndi udindo waukulu wothandiza onse kuti azichita nawo ntchito yolalikira mokhazikika. Woyang’anira utumiki ndi amene amatsogolera pokonza zopita mu utumiki mkati mwa mlungu. Woyang’anira phunziro la buku aliyense ali ndi udindo wokonza zoti gulu lake lichite, makamaka pamapeto pa mlungu. Pa nthaŵi imene mpingo wonse wakumana kuti ukonzekere utumiki wakumunda, mwachitsanzo, pamapeto pa phunziro la Nsanja ya Olonda, woyang’anira phunziro la buku aliyense ayenera kusamalira anthu a m’gulu lake.

3 ‘Moyenera ndi Molongosoka’: Amene waikidwa kuti atsogolere msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda ayenera kuyamba pa nthaŵi yake ndipo aonetsetse kuti msonkhanowo ukhale wa mphindi 10 kapena 15. Ndibwino kuti azigaŵiratu anthu okalalikirawo m’timagulu ndi kuwapatsa gawo asanatseke ndi pemphero (pokhapokha ngati oyang’anira maphunziro a buku ndi amene achite zimenezi, monga momwe tanenera kale). Zimenezi zimathandiza kuti ofalitsa asamakaunjikane m’gawo, zimene zingachititse kuti anthu asalemekeze ntchito yathu. Zimenezi n’zogwirizananso ndi langizo la Paulo lakuti: “Zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.” (1 Akor. 14:40) Onse amene amafika pa misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda ayenera kuthandiza kuti msonkhanowo uyende bwino mwa kufika panthaŵi yake, kumvera zilizonse zimene wotsogolera gulu akunena, ndi kunyamuka msanga kupita ku gawo msonkhanowo ukangotha.

4 Timakhala Ogwirizana: Ulaliki wagulu ndi njira yabwino kwambiri yodziŵira bwino anthu ena mu mpingo wathu. Ngakhale kuti sikulakwa kupezeratu munthu woyenda naye muulaliki, tingapindulenso ngati tipezeka pa misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda tisanapezeretu woyenda naye. Akhoza kutiuza kuti tiyende ndi munthu amene sitikumudziŵa bwino, ndipo zimenezi zingatithandize “kukulitsa” chikondi chathu.—2 Akor. 6:11-13, NW.

5 Ulaliki wagulu umatilimbikitsa ndi kutithandiza kukhala ogwirizana monga ‘othandizana m’choonadi.’ (3 Yoh. 8) Tiyeni tizichita nawo ulaliki umenewu nthaŵi zonse!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena