Njira Zisanu Zopezera Phunziro la Baibulo
1. Ngati zimakuvutani kupeza munthu woti muziphunzira naye Baibulo m’gawo la mpingo wanu, kodi muyenera kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
1 Kodi zimakuvutani kupeza munthu woti muziphunzira naye Baibulo? Ngati zili choncho, pitirizani kuchita khama kufunafuna phunziro la Baibulo. Yehova amadalitsa anthu amene sagwa ulesi pofuna kukwaniritsa chifuniro chake. (Agal. 6:9) M’munsimu muli njira zisanu zimene zingakuthandizeni kupeza phunziro la Baibulo.
2. Kodi tingapemphe bwanji anthu mwachindunji kuti tiziphunzira nawo Baibulo?
2 Apempheni Mwachindunji: Anthu ambiri amadziwa kuti timagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, koma mwina sadziwa kuti timachititsanso maphunziro a Baibulo. Pamene mukulalikira kunyumba ndi nyumba, bwanji osapempha anthu mwachindunji kuti muziphunzira nawo Baibulo? Mungafunsenso anthu achidwi amene mumawagawira magazini mwezi ndi mwezi ngati angakonde kuti muziphunzira nawo Baibulo. Ngati akana, pitirizani kuwagawira magazini ndiponso kuwalimbikitsa kukonda zinthu zauzimu. M’bale wina anakhala akugawira magazini banja lina kwa zaka zingapo. Tsiku lina atawagawira magazini atsopano, ananyamuka kuti azipita koma kenako anawafunsa kuti: “Kodi mungakonde kuti ndiziphunzira nanu Baibulo?” M’baleyu anadabwa banjali litavomera kuphunzira Baibulo ndipo panopa banjali linabatizidwa.
3. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti aliyense amene amafika pamisonkhano akuphunzira Baibulo ndi wina wake?
3 Anthu Amene Amafika Pamisonkhano: Musamaganize kuti anthu achidwi amene amafika pamisonkhano ya mpingo ali kale ndi munthu amene amaphunzira naye Baibulo. M’bale wina anafotokoza kuti: “Pafupifupi hafu ya anthu amene ndimaphunzira nawo Baibulo ndinawapeza pocheza ndi anthu amene amafika pamisonkhano.” Mlongo wina anapempha mzimayi wina kuti aziphunzira naye Baibulo. Mayiyu ankachita manyazi kucheza ndi anthu, koma ana ake aakazi anali obatizidwa. Iye anakhala akusonkhana ndi mpingo pafupifupi zaka 15 ndipo nthawi zonse ankafika pa Nyumba ya Ufumu misonkhano ikuyamba ndipo ankanyamuka misonkhano ikangotha. Mayiyu anavomera kuphunzira Baibulo ndipo patapita nthawi anabatizidwa. Mlongoyo analemba kuti: “Ndikudandaula kuti panadutsa zaka 15 ndisanapemphe mayiyu kuti ndiziphunzira naye Baibulo.”
4. Kodi kufunsa ena kungatithandize bwanji kuti tipeze phunziro?
4 Muzifunsa Ena: Mlongo wina amayesetsa kulowa mu utumiki ndi anthu osiyanasiyana pamene akukachititsa maphunziro awo a Baibulo. Pambuyo popempha mwini wake wa phunzirolo, mlongoyu amafunsa wophunzirayo ngati akudziwa anthu ena amene angafune kuphunzira Baibulo. Inunso mukamagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kwa munthu amene mwakhala mukucheza naye, mungafunse kuti: “Kodi mukudziwa aliyense amene angakonde kulandira bukuli?” Chifukwa cha zovuta zina, nthawi zina ofalitsa kapena apainiya sangakwanitse kuchititsa phunziro la Baibulo ndi munthu amene akumana naye m’gawo la mpingo wawo. Choncho, muziuza anthu ena kuti muli ndi mpata woti mukhoza kumachititsa phunziro la Baibulo.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha kuti tiziphunzira Baibulo ndi anthu amene amuna kapena akazi awo ndi Mboni?
5 Amuna Kapena Akazi Osakhulupirira: Kodi mu mpingo wanu muli ofalitsa amene amuna kapena akazi awo si Mboni? Anthu ena amene si Mboni amakana kukambirana mfundo za m’Baibulo ndi amuna kapena akazi awo amene ndi Akhristu, koma akhoza kulola kuphunzira ndi munthu wina. Koma tisanayambe kuphunzira nawo, tingachite bwino kukambirana ndi mwamuna kapena mkazi wachikhristuyo n’cholinga choti tidziwe njira yabwino yowafikira pamtima.
6. Kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji ngati mukufuna kupeza phunziro la Baibulo?
6 Pemphero: Musakayikire kuti pemphero lingakuthandizeni. (Yak. 5:16) Yehova akutilonjeza kuti adzamva mapemphero athu ngati ali ogwirizana ndi chifuniro chake. (1 Yoh. 5:14) Mwachitsanzo, m’bale wina amene ankakhala wotanganidwa kwambiri anayamba kupemphera kuti apeze phunziro la Baibulo. Mkazi wake ankakayikira ngati m’baleyo angapeze nthawi yochititsa phunziro ndiponso kuthandiza wophunzira makamaka ngati wophunzirayo atakhala ndi mavuto ambiri. Choncho, mlongoyu anatchula nkhawa zakezi popemphera kuti Yehova athandize mwamuna wake kupeza phunziro. Mapemphero awo anayankhidwa patapita pafupifupi milungu iwiri. Izi zinachitika pamene mpainiya wina anapeza munthu amene ankafuna kuphunzira Baibulo ndipo anauza m’baleyu kuti aziphunzira naye. Mkazi wa m’baleyu analemba kuti: “Aliyense amene akuganiza kuti sangakwanitse kuchititsa phunziro la Baibulo ndikumulimbikitsa kuti: Muzitchula mwachindunji nkhani imeneyi m’mapemphero anu ndipo musasiye kuipempherera. Ifeyo tapeza madalitso ambiri kuposa mmene tinkaganizira.” Ngati mutachita khama, inunso mukhoza kupeza munthu woti muziphunzira naye Baibulo n’kupeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chothandiza munthu kuti aziyenda pamsewu wopita “ku moyo.”—Mat. 7:13, 14.