Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 7
Kupereka Pemphero pa Phunziro
1. (a) N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuyamba ndi kumaliza phunziro la Baibulo ndi pemphero? (b) Kodi tingatani kuti tiyambe kumapemphera pa phunziro la Baibulo?
1 Kuti ophunzira Baibulo apite patsogolo mwauzimu, m’pofunika dalitso la Yehova. (1 Akor. 3:6) Choncho, ndi bwino kuyamba ndi kumaliza phunziro ndi pemphero. Tikhoza kumachita zimenezi pa phunziro loyambirira lenileni ngati tikuyamba kuphunzira ndi anthu amene ndi okonda zopembedza. Koma kwa ena, tingafunike kuona nthawi yabwino imene tingayenere kuyamba kumapemphera pa phunziro. Mungathe kugwiritsa ntchito Salmo 25:4, 5 ndi 1 Yohane 5:14 kuti muthandize wophunzira kuona chifukwa chake payenera kuperekedwa pemphero ndiponso mungagwiritse ntchito Yohane 15:16 kufotokoza kufunika kopemphera kwa Yehova kudzera mwa Yesu Kristu.
2. Ngati mlongo apita ndi mbale wobatizidwa kapena mwamuna wofalitsa wosabatizidwa ku phunziro la Baibulo, kodi ndani amene adzapereka pemphero?
2 Kodi ndani amene ayenera kupereka pemphero pa phunziro la Baibulo? Ngati mbale wobatizidwa apita ndi mlongo kuphunziro, mbaleyo ayenera kupereka pemphero, ngakhale kuti mlongoyo angachititse phunzirolo atavala chophimba kumutu. (1 Akor. 11:5, 10) Koma ngati mwamuna wofalitsa Ufumu wosabatizidwa apita ndi mlongo ku phunziro, mlongoyo ayenera kupereka pemphero. Ngati zili choncho, mlongoyo ayenera kuvala chophimba kumutu popemphera ndiponso pochititsa phunzirolo.
3. Kodi ndi zinthu zofunika ziti zimene tingaziphatikize m’mapemphero operekedwa pa phunziro la Baibulo?
3 Zimene Mungaziphatikize M’pemphero: Mapemphero a pa phunziro la Baibulo sayenera kukhala aatali, koma ayenera kukhala olunjika. Kuwonjezera pa kupempha dalitso la Mulungu pa phunzirolo ndiponso kuthokoza chifukwa cha choonadi chimene mukuphunzira, n’koyenera kupereka ulemerero kwa Yehova monga Gwero la malangizo. (Yes. 54:13) Tingaphatikizemonso mawu osonyeza kuti tikukondwera naye wophunzirayo ndiponso kuyamikira gulu limene Yehova akugwiritsa ntchito. (1 Ates. 1:2, 3; 2:7, 8) Kupempha Yehova kuti adalitse khama la wophunzirayo pamene akuyesetsa kugwiritsa ntchito zimene akuphunzira, kungamuthandize kuona kufunika kokhala ‘wakuchita mawu.’—Yak. 1:22.
4. Kodi kuyamba ndi kumaliza phunziro la Baibulo ndi pemphero, kumabweretsa phindu liti?
4 Pemphero lili ndi phindu lalikulu. Limabweretsa dalitso la Mulungu. (Luka 11:13) Limasonyeza kuti kuphunzira Mawu a Mulungu ndi nkhani yaikulu. Pamene wophunzira akumvetsera mapemphero athu, amaphunzira mmene angapempherere. (Luka 6:40) Ndiponso, mapemphero ochokera mu mtima wokonda Mulungu ndiponso osonyeza kuti timayamikira makhalidwe ake osayerekezeka akhoza kuthandiza wophunzira kukhala paubwenzi ndi Yehova.