Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tizipereka pemphero pochititsa phunziro la Baibulo lachidule limene timachita titaimirira pakhomo la munthu?
Timapeza madalitso ambiri tikamatsegula ndiponso kutseka phunziro la Baibulo ndi pemphero. Tikamapemphera, timakhala tikupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake woyera kuti utitsogolere pa zokambirana zathu. (Luka 11:13) Pemphero limathandizanso wophunzirayo kuona kufunikira kwa zimene akuphunzira m’Baibulo ndiponso limamuphunzitsa mmene angamapempherere. (Luka 6:40) Choncho, mukangoyamba kuphunzira Baibulo ndi winawake, ndibwino kuyamba kupemphera musanayambe kuphunzira. Komabe, chifukwa chakuti zochitika zimasiyanasiyana, wochititsa phunziroyo ayenera kuchita zinthu mozindikira posankha kuti apemphere kapena ayi pamene akuchititsa phunziro ataimirira pakhomo la munthu.
Mfundo imodzi yofunika kuiganizira ndi malo amene mumaphunzirira. Ngati ndi pamalo amene sipadutsadutsa anthu, mungapereke pemphero lachidule kuti muyambe ndiponso kutseka phunziro limene lakhala likuchitika nthawi zonse mutaima pakhomo. Koma ngati kuchita zimenezi kungakope chidwi chosafunikira kapenanso kuchititsa wophunzirayo kukhala womangika, zingakhale bwino kudikira kaye kufikira mutayamba kuchitira phunzirolo pamalo amene sipadutsadutsa anthu. Ndiye kaya tikuchita phunziro pamalo otani, tiyenera kuona bwino mmene zinthu zilili kuti tidziwe malo amene tingatsegule phunziro ndi pemphero. Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2005 tsamba 8.