Mmene Phunziro la Buku la Mpingo Limatithandizira
1. Kodi misonkhano isanu imene timakhala nayo mlungu ndi mlungu imatithandiza motani?
1 Msonkhano uliwonse umene timakhala nawo mlungu ndi mlungu, uli ndi cholinga chake ndipo umachitika mosiyana ndi unzake. Koma misonkhano yonseyi ndi yofunika potithandiza kuganizirana wina ndi mnzake, kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.’ (Aheb. 10:24, 25) Kodi Phunziro la Buku la Mpingo lili ndi mbali zotani zapadera ndiponso zothandiza?
2. Kodi kupezeka pa gulu la anthu ochepa paphunziro la buku n’kopindulitsa motani?
2 Limatithandiza Kupita Patsogolo Mwauzimu: Anthu amene amapezeka pa phunziro la buku ndi ochepa kwambiri powayerekezera ndi omwe amapezeka pa misonkhano ina ya mpingo. Chifukwa cha zimenezi, sizovuta kukhala ndi mabwenzi amene angatilimbikitse mwauzimu. (Miy. 18:24) Kodi mwayesapo kudziwa aliyense yemwe ali m’gulu la phunziro la buku lanu, mwina kuwapempha kuti muyendere nawo limodzi muutumiki? Phunziro la buku limathandizanso woyang’anira phunzirolo kuti adziwe moyo wa munthu aliyense yemwe ali m’gululo ndiponso kuti azilimbikitsa aliyense.—Miy. 27:23.
3. Kodi phunziro la buku limalimbikitsa motani anthu kuyankhapo ndiponso ophunzira Baibulo kuti azipezekapo?
3 Kodi anthu omwe mumaphunzira nawo Baibulo mwawapempha kuti adzapezeke nawo paphunziro la buku? Anthu achidwi omwe safuna kupezeka pa misonkhano yathu yaikulu sangachite mantha kwenikweni kupezeka pa msonkhano wa anthu ochepa, makamaka wochitikira m’nyumba ya munthu. Popeza aliyense amakhala womasuka zimenezi zimathandiza ana ndiponso atsopano kuti ayankhepo. Ndipo chifukwa choti pamapezeka anthu ochepa, timakhala ndi mwayi woyankhapo nthawi zambiri ndipo mwa kutero timatamanda Yehova.—Sal. 111:1.
4. Kodi phunziro la buku lingakhale labwino m’njira zotani?
4 Nthawi zambiri maphunziro a buku amachitika m’gawo lonse m’malo omwe ndi osavuta kwa anthu kufikapo. N’zoona kuti sizingatheke kuti aliyense auzidwe kuti azipezeka pa phunziro la buku limene lili kufupi ndi komwe akukhala, koma mtunda womwe timayenda popita ku phunziro lomwe tagawiridwa umakhala waufupi poyerekeza ndi umene timayenda popita ku misonkhano ina ya mpingo. Malo a phunziro la buku angakhalenso abwino kuchitirako misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda.
5. Kodi woyang’anira phunziro la buku lathu angatithandize motani muutumiki wa kumunda?
5 Limatithandiza Muutumiki: Woyang’anira phunziro la buku amafuna kwambiri kuthandiza aliyense kuti azichita utumiki mokhazikika, mosangalala ndiponso kuti akhale ndi zotsatirapo zabwino. Motero, amayesetsa kuyenda ndi aliyense m’gululo, ndi kuthandiza aliyense m’mbali zosiyanasiyana za utumiki. Ngati mukuona kuti simukuchita bwino mbali ina ya utumiki, monga kupanga maulendo obwereza, dziwitsani woyang’anira phunziro la buku lanu. Mwina angakonze zoti inuyo muziyendera limodzi ndi wofalitsa waluso wa m’gulu lanu. Luso lanu lophunzitsa anthu Baibulo lidzanoledwa ngati muchita chidwi kwambiri ndi njira zabwino zophunzitsira zimene woyang’anira phunziro la buku amagwiritsa ntchito akamachititsa phunziro la buku.—1 Akor. 4:17.
6. N’chifukwa chiyani tifunikira kuyesetsa kuti tizipindula mokwanira ndi dongosolo la phunziro la buku?
6 Phunziro la Buku la Mpingo ndi dongosolo lachikondi. Dongosolo la Yehova limeneli limatithandiza kuti tikhalebe olimba mwauzimu m’nthawi zovuta zino.—Sal. 26:12.