Kuthandiza Ena pa Phunziro la Buku la Mpingo
1 Polambira Yehova Akristu oyambirira ankakumana m’nyumba. (Aroma 16:3, 5; Filem. 1, 2) Lerolino m’madera ambiri, makamaka kumene abale athu amagwira ntchito mopanikizika, misonkhano imachitikira m’nyumba za abale. Lerolinonso, Maphunziro ambiri a Buku a Mpingo amachitikira m’nyumba za abale ndipo Yehova akupitiriza kudalitsa makonzedwe ameneŵa.
2 Mwa Phunziro la Buku la Mpingo, akulu angasamalire kwambiri munthu aliyense payekha malinga ndi mmene akupitira patsogolo mwauzimu—chinthu chimene chingakhale chovuta kuchita pamisonkhano ikuluikulu. Wochititsa phunziro amachita khama kudziŵana bwino ndi onse a m’gulu lake, chachikulu koposa ndicho kuŵeta ndiponso kusamalira zosoŵa zawo zauzimu. (Miy. 27:23) Amayesetsa kugwirira nawo ntchito pamodzi mu utumiki wakumunda ndiponso nthaŵi zina kuwayendera m’makomo mwawo.
3 Nthaŵi zambiri phunziro limaikidwa kufupi ndi kumene kumakhala anthu amene amapita kuphunziro limenelo. Pachifukwa chimenechi kaŵirikaŵiri amakhala malo okonzekerera utumiki wakumunda. Izi zimakupatsani mpata wogwira ntchito ndi anthu osiyanasiyana a m’gulu lanu ndipo mumapindula mwakuona mmene iwo akuchitira akafika pakhomo la munthu. Mukatha phunziro la buku ndi nthaŵi yabwino yokonzekera kugwira ntchito pamodzi.
4 Sonyezani Chidwi: Kodi paphunziro lanu la buku mumaona kuti pali mzimu wonga wabanja? Onse akasonyeza chidwi mwa ena m’gululo zimathandiza kukhala okondana. (Agal. 6:10) Mwachitsanzo, kodi mumazindikira ngati ena sanabwere pamsonkhano ndiyeno n’kuwauza kuti munawasoŵa? Ngati wina m’banja panalibe panthaŵi ya chakudya ndithudi ena m’banjamo amazindikira. Ndipo onse amada nkhaŵa. Mkhalidwe umenewu paphunziro la buku umagwirizanitsa abale pamodzi ndipo umawalimbikitsa kusaphonya “chakudya.” Pamene musonyeza chidwi mwa aliyense wa m’gululo mudzathandiza kukulitsa mkhalidwe wa “banja” umenewu.
5 Kodi mungakhale ndi njira zina zimene mungasonyezere chidwi mwa ena? Njira ina imene mungachitire zimenezi ndiyo kuchita khama kulankhula ndi ena pamisonkhano, osati kungopereka moni kokha basi. Ena amakhala amanyazi koma amakhala akufuna wina woti alankhule naye ndipo amalankhula ngati wina awalankhula. Pali zinthu zambiri zimene tingazichite. Wochititsa phunziro lanu la buku angakhale ndi malingaliro ena. Bwanji osam’funsa?
6 Kodi mungachite chiyani ngati wina wa m’gulu lanu la phunziro la buku akuoneka kufooka kapena kuti ali ndi vuto? Uphungu wakuti “limbikitsani amantha mtima” udzakhala woyenera kwabasi. (1 Ates. 5:14) Ngati wina akudwala, kumakhala kotonthoza anzake akabwera kudzamuona ndi kum’thandiza! Nthaŵi zambiri zimene zimafunika n’kungodziŵa kuti ena akudziŵa ndiponso amada nkhaŵa. Wochititsa phunziro la buku, monga kholo, ayenera kukhala tcheru kuona zizindikiro za kufooka ndipo ayenera kupereka thandizo loyenera.
7 Kodi ndi Motani Mmene Mungathandizire?: Pali njira zina zimene mungathandizire makonzedwe a phunziro la buku. Njira imodzi ndiyo chitsanzo chanu chabwino. Mwachitsanzo, kuvala mmene mungavalire popita ku msonkhano ku Nyumba ya Ufumu mumasonyeza ulemu. Mupereka chitsanzo chabwino kwa awo amene ali ndi chizoloŵezi chovala motayirira. Kodi n’chizoloŵezi chanu kufika pamsokhano nthaŵi yabwino kuti musadodometse msonkhano?
8 N’zodziŵikiratu kuti phunziro limakhala losangalatsa ngati onse akonzekera bwino, mwina kudula mizera mayankho ndiyeno n’kumayankha m’mawu awoawo. Kuŵerengeraku malemba operekedwa ndiyeno n’kukagogomezera kungathandize kwambiri msonkhanowo. Enanso amapeza nthaŵi kuŵerenga nkhani yogwirizana ndi mfundo zina zofunika n’kukagaŵana zimenezi ndi gululo. Izi n’zabwino kwambiri. Zinthu zonsezi zimathandiza Phunziro la Buku la Mpingo kukhala lotsitsimula ndi lomangirira mwauzimu kwa onse opezekapo.
9 Awo amene amapezeka pa phunziro la buku nthaŵi zonse amakhulupirira kuti Yehova amalidalitsa. Ndi malo amene munthu angathandizidwe ndiponso angathandizire ena kutsitsimulidwa mwauzimu. Ngati simupezeka pamsonkhano umenewu nthaŵi zonse, bwanji osasintha ndandanda yanu kuti muzisangalala ndi msonkhano wabwino umenewu womwe Yehova ndi gulu lake akukonzerani.