Kodi Ndinu Nokha M’banja Mwanu Amene Muli M’choonadi?
1 Si dalitso lake kuona banja lonse likutumikira Yehova pamodzi! Komabe, si onse amene ali mu mkhalidwe wosangalatsa umenewu. Abale ndi alongo athu ambiri ndi iwo okha amene akutumikira Yehova m’mabanja awo. Ndithudi tiyenera kuwayamikira chifukwa amasonyeza chitsanzo chabwino cha kukhulupirika ndiponso kupirira.—2 Ates. 1:4.
2 Makolo: Mu mpingo wanu kodi muli ndi alongo a ana amene amuna awo sali m’choonadi, kapena amuna awo anawasiya? Mayi wina analemba kuti: “Ndinayenera kudyetsa banja langa—ndinafunika kugula zinthu, kuyeretsa zinthu, kuphika, kusoka, ndiponso kumvetsera mavuto a ana anga,” komanso kupita ndi banja lonse kumisonkhano ndi ku utumiki. Inde, zitsanzo zabwino ngati zimenezi n’zofunika chiyamikiro chathu ndi thandizo lathu.
3 Kodi n’chiyani chimene tingachite kuti tiwathandize? Ofalitsa ena achinyamata akhala mabwenzi kwambiri a ana a m’mabanja ogawanika ameneŵa n’cholinga choti akhale ndi mabwenzi abwino. Ofalitsa ozoloŵera athandiza mwa kuchita maphunziro a Baibulo ndi anawo ndiponso mwa kuwathandiza kupita mu utumiki mokhazikika. Banja lina linadzipereka kuthandiza mlongo amene mwamuna wake sanali m’choonadi. Kenako, banja limeneli mokoma mtima linaitana mwamuna wa mlongo uja kudzakhala nawo pazochitika zina za teokalase. Mapeto ake mwamuna uja anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anadzakhala wofalitsa wodzipatulira ndi wobatizidwa.
4 Ofalitsa Achinyamata: Ambiri a ana kapena ofalitsa achinyamata athu ndi iwo okha amene ali m’choonadi m’banja mwawo. Mnyamata wina wa Kum’maŵa anachitabe cholinga chake cha upainiya, ngakhale anali ndi miyambo ya banja yovuta ndiponso anam’panikiza kwambiri kuti apeze maphunziro apamwamba. Mwa chitsanzo chake chabwino, mlongo wake wamng’ono anaphunzira choonadi ndipo onse tsopano akuchita upainiya.
5 Nthaŵi zambiri ofalitsa achinyamata amene makolo awo sali m’choonadi amafuna thandizo ndi chitsogozo, ponse paŵiri mwauzimu ndi mwakuthupi. Achikulire ambiri athandiza mokoma mtima achinyamata ameneŵa mwa kuchita nawo chidwi, ndipo akhala atate ndi amayi awo mwauzimu, titero kunena kwake. Banja lina ponena za wophunzira Baibulo wina wachinyamata linati: “Analimbikitsidwa kupemphera, kugwiritsa ntchito mfundo za Baibulo zachikhalidwe m’moyo wake ndiponso kukhala waulemu ndi woleza mtima ndi makolo ake.” Banjalo linamuthandiza kupezeka pamsonkhano wa mayiko ndipo tsopano akupita patsogolo kuti abatizidwe.
6 Okalamba Kapena Opunduka: Awo amene ali okalamba kapena opunduka amayamikiridwa kwambiri mu mpingo ngakhale kuti amachita zochepa mu ntchito yawo yolalikira. Ngati ndinu m’modzi wa anthu otereŵa, tikufuna tikutsimikizireni kuti kudzipereka kwanu ndiponso utumiki wanu wopatulika zimalimbitsa chikhulupiriro chathu.—Miy. 16:31.
7 Anthu ambiri okalamba kapena opunduka agwiritsa ntchito unyamata wawo ndiponso mphamvu zawo mu utumiki wa Yehova, ndipo tsopano angakhale ali okha. Ndithudi sitikufuna kuti tsopano tiwanyalanyaze. Kungocheza nawo nthaŵi pang’ono kungakhale kothandiza kwambiri. Komanso, titha kuwathandiza kukawagulira zinthu ndiponso kuwagwirira ntchito za panyumba, kapena kupita nawo ku misonkhano ndi mu utumiki wa m’munda. Banja lina linathandiza mkazi wina wokalamba amene anali wamasiye, yemwe mwana wake m’modzi yekhayo anamwalira. Akum’tonthoza, anam’thandizanso mwakuthupi kusamalira nkhani zamalamulo.
8 Ngati ndinu nokha m’banja mwanu amene muli m’choonadi, ndithudi timafunitsitsa kuti mukhale olimba mwauzimu. Kugwira nanu ntchito ndiponso kuyanjana nanu kumatilimbikitsa, ndipo tikuthokoza Yehova kaamba ka ntchito yabwino imene mukuchita.—1 Ates. 1:2, 3.