Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/00 tsamba 3-4
  • Makonzedwe Athu Opepukitsidwa a Kagaŵidwe ka Mabuku

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makonzedwe Athu Opepukitsidwa a Kagaŵidwe ka Mabuku
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Timapezera Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • “Muzipereka Mphatso kwa Yehova”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Bokosi La Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 5/00 tsamba 3-4

Makonzedwe Athu Opepukitsidwa a Kagaŵidwe ka Mabuku

1 Makonzedwe opepukitsidwa a kagaŵidwe ka mabuku popanda mtengo weniweni tsopano akhala akugwira ntchito kwa miyezi inayi. Kodi makonzedwe ameneŵa akuyenda bwino? Malipoti autumiki wakumunda akusonyeza kuwonjezeka kwa zogaŵira za mitundu yonse. M’lingaliro lenileni anthu ambiri zedi akupatsidwa mwayi wakuti “adze . . . atenge madzi a moyo kwaulere.”—Chiv. 22:17.

2 Komabe, tilibe ulamuliro, komanso si cholinga chathu, kupereka mabuku mwachisawawa kwa munthu aliyense amene angalandire. Monga mmene timagwiritsira ntchito mwanzeru zinthu zathu zakuthupi, wofalitsa aliyense ali ndi udindo kuonetsetsa kuti akugwiritsa ntchito mwanzeru mabuku amene Sosaite ikumupatsa kudzera ku mpingo wake popanda kumulipiritsa. Pamene kuli kwakuti Sosaite ikupereka mabuku kwa ofalitsa mosalipiritsa, mwachionekere sizikutanthauza kuti, siiwononga ndalama popanga ndi potumiza mabukuwo. Onse ayenera kuzindikira makamaka kufunika kwa mabuku athu pothandiza anthu oona mtima ofuna chidziŵitso cholongosoka cha Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Kristu.—Yoh. 17:3.

3 Kodi Sosaite imatha bwanji kumapereka mabuku kwa onse popanda kulipiritsa? Zowonongedwa zosapeŵeka zochitika popanga ndiponso potumiza mabuku zimalipiridwa ndi zopereka zaufulu. Atumiki odzipatulira a Yehova ndiwo gwero lalikulu la chichirikizo chimenechi. Mboni za Yehova sizinapemphepo thandizo kwa anthu kaamba ka ntchito yofunika kwambiri imeneyi yolengeza Ufumu. Sitinapemphetsepo m’mbuyomu, ngakhalenso pakali pano sitipeza ndalama mopempha anthu. Komabe, zopereka zochepa chabe zochokera kwa anthu achidwi ndiponso oyamikira amene timakumana nawo m’munda timaziyamikira.

4 Ntchito ya Zopereka Zathu: Chotero, n’koyenera kuti tikhale okonzeka kufotokoza mwachidule ndiponso momveka bwino mmene zopereka zaufulu zimachirikizira ntchito yathu yophunzitsa Baibulo ya padziko lonse. Ndalama zonse zimene timalandira zimagwira ntchito yolipirira zinthu zambiri zimene zawonongedwa mu ntchito yolalikira Ufumu m’nthaŵi yamakono ino. Kuphatikiza pa kusindikiza mabuku ogaŵira padziko lonse, Sosaite imakonzetsa maofesi anthambi, nyumba za Beteli, sukulu za amishonale ndi zophunzitsa utumiki, kusamalira amishonale, oyang’anira oyendayenda, malo otumizira mabuku, ndi ntchito zina zofunika pokwaniritsa ntchito imene Yesu anapatsa atumwi ake.—Mat. 24:14; 28:19, 20.

5 Kuwonjezeka kwakukulu kumene kukuchitika pa anthu a Yehova kwapangitsa ena kufunsa zimene angachite kuti athandize. Ambiri sangathe kuthandiza kwenikweni mwa kumanga nawo nthambi zatsopano ndiponso Nyumba za Ufumu kapena kupita ku mayiko akutali kukathandiza kulalikira kumeneko. Koma ndi cholinga chothandiza nawo m’zochitika zosangalatsa zimenezi kumlingo umene angathe, ofalitsa ambiri ndi mabanja awo ali ndi chizoloŵezi chopatula kangachepe nthaŵi zonse kothandiza ntchito ya padziko lonse. (Yerekezani ndi 1 Akorinto 16:1, 2.) Mwa njira imeneyi, ntchito zonse za Sosaite zimachirikizidwa, kuphatikizapo kugaŵira mabuku. Aliyense sayenera kuona zopereka zaufulu za ntchito yapadziko lonse monga zolipilira mtengo wa mabuku wokha.

6 Tikamapita kwa mwininyumba kapena kwa anthu ena n’cholinga chowalalikira, tiyenera kukhala okonzeka kukambirana nawo nkhani za Baibulo. Mayambidwe osangalatsa osiyanasiyana ambiri zedi, ndiponso mitu ya Baibulo yabwino yambiri zaikidwa mu Kukambitsirana za m’Malemba. Malinga ndi mmene munthuyo akuchitira ndi uthenga wa Ufumu, wofalitsa angaone mmene angachitire ponena za kupereka mabuku. Ngati sakuoneka kukhala ndi chidwi chokwanira chakuti n’kum’patsa buku kapena zofalitsa zina, mungaone mmene mungathetsere kukambiranako mwanzeru ndi kupita ku nyumba zina. Kapena mungafune kusiya thirakiti ngati munthuyo alonjeza kuti aliŵerenga. Onetsetsani chidwi chawo kuti mudzapite paulendo wobwereza. Zimenezi mungazichitenso pamene mulibe nthaŵi yokwanira yoti n’kukambirana mwachifatse chifukwa chakuti munthuyo watanganidwa kapena simunam’fikire nthaŵi yabwino.

7 Makonzedwe opepukitsidwa a kagaŵidwe ka mabuku akuthandiza aliyense kuona kuti ntchito yathu yophunzitsa Baibulo ya padziko lonse si malonda mwanjira iliyonse. Akutithandizanso kuika patsogolo cholinga chathu cholalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndiponso kupanga ophunzira a Yesu Kristu. Mosiyaniranatu ndi magulu “opemphetsa ndalama,” Mboni za Yehova zimasangalala kuona kuti mabuku akuperekedwa kwa anthu onse mosalipiritsa. Sitipempha m’pang’ono pomwe zopereka zochirikizira ntchito yapadziko lonse kwa anthu amene alibe chidwi ndi uthenga wathu. (Onani Nsanja ya Olonda ya December 1, 1990, tsamba 22 ndi 23.) Zopereka zonse zimagwiritsidwa ntchito kuchirikizira ntchito yophunzitsa Baibulo ya padziko lonse imeneyi, popeza ogwira ntchito onse m’gulu limeneli ndi odzifunira ndipo salandira malipiro kapena chiwongola dzanja. Nkhani ya zopereka zothandizira ntchito yapadziko lonse timakamba ndi anthu okhawo amene amafunsa kapena amasonyeza chidwi mu ntchito yathu.

8 Pofutukula utumiki wathu mwachangu, tikumagwiritsa ntchito mwanzeru mabuku a Sosaite amtengo wapataliwa, Yehova adzapitiriza kuwonjezera. Anthu amitima yabwino kulikonse amayamikira kalongosoledwe kathu komveka ka utumiki wathu ndipo amasangalala kusonyeza kuchirikiza kwawo mwa zopereka zaufulu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena