Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/11 tsamba 2
  • Bokosi La Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi La Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Tizigwiritsa Ntchito Mwanzeru Mabuku Ndiponso Magazini
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Mabuku Athu Ofotokoza Baibulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Makonzedwe Athu Opepukitsidwa a Kagaŵidwe ka Mabuku
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 12/11 tsamba 2

Bokosi La Mafunso

◼ Kodi tingadziwe bwanji munthu woyenera kumupatsa magazini kapena mabuku athu?

Chinthu chofunika kwambiri ndi chidwi cha munthuyo. Ngati munthu akuoneka kuti ali ndi chidwi chenicheni, tingamupatse magazini awiri, kabuku, buku kapena chofalitsa chilichonse chimene tikugawira pa nthawiyo. Tingamupatse zinthu zimenezi ngakhale titaona kuti ali ndi ndalama yochepa kapenanso alibiretu ndalama yoti apereke pa ntchito ya padziko lonse. (Yobu 34:19; Chiv. 22:17) Koma tisawononge magazini ndi mabuku athu amtengo wapatali popatsa anthu amene alibe nawo chidwi.—Mat. 7:6.

Kodi tingadziwe bwanji kuti munthu uyu ali ndi chidwi kapena ayi? Tingadziwe kuti munthu ali ndi chidwi ngati wavomera kuti tikambirane naye. Chimenechi ndi chizindikiro chachikulu. Munthu akamamvetsera pamene tikulankhula, kuyankha mafunso amene tamufunsa ndiponso kunena maganizo ake pa nkhani imene tikukambirana, zimasonyeza kuti nkhaniyo ikumukhudza. Akamatsatira m’Baibulo pamene tikuwerenga malemba, zimasonyeza kuti amalemekeza Mawu a Mulungu. Nthawi zambiri ndi bwino kufunsa munthuyo ngati awerenge magazini kapena mabuku amene tikufuna kum’patsa. Ofalitsa ayenera kuchita zinthu mosamala kuti adziwe ngati munthu ali ndi chidwi. Mwachitsanzo, tikamalalikira mumsewu, si bwino kumangopereka magazini, timabuku kapena mabuku kwa munthu aliyense amene akudutsa. Ngati tikulephera kudziwa kuti munthu uyu ali ndi chidwi kapena alibe, zingakhale bwino kumupatsa kapepala koitanira anthu ku misonkhano kapena kapepala kena kalikonse.

N’chimodzimodzi potenga magazini kapena mabuku ku Nyumba ya Ufumu. Wofalitsa ayenera kutenga mabuku malinga ndi mmene amalalikirira, osati malinga ndi m’thumba mwake. Zopereka zimene timapereka si zolipirira mabuku okha ayi. Zimathandizira pa ntchito zonse zokhudza kulalikira padziko lonse. Kaya timakhala ndi ndalama zambiri kapena ayi, mtima woyamikira ndi umene ungatilimbikitse kupereka zopereka mowolowa manja. Izi zikutanthauza kuti popereka ndalama zothandizira pa ntchito za Ufumu, tizipereka ndalama kuchokera pa ndalama zimene tikufuna kugwiritsa ntchito osati pa ndalama zimene zatsala ayi. (Maliko 12:41-44; 2 Akor. 9:7) Mtima woyamikira ungatithandizenso kuti tizitenga mabuku okhawo amene tikagwiritse ntchito, kuti tisawononge ndalama zopangira mabuku.

[Mawu Otsindika patsamba 2]

Ofalitsa ayenera kuchita zinthu mosamala kuti adziwe ngati munthu ali ndi chidwi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena