Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/05 tsamba 8
  • Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Mabuku Athu Ofotokoza Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Mabuku Athu Ofotokoza Baibulo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Tizigwiritsa Ntchito Mwanzeru Mabuku Ndiponso Magazini
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Bokosi La Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 12/05 tsamba 8

Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Mabuku Athu Ofotokoza Baibulo

1, 2. Kodi anthu ambiri amawaona motani mabuku athu, ndipo kodi zimenezi zikubutsa funso lotani?

1 “Ndakhala ndikuwerenga mabuku anu kuyambira chaka cha 1965. N’kamawerenga, ndimaona mavesi a m’Baibulo, ndipo nkhani zonse za m’mabuku mwanu zimagwirizana ndi zimene zili m’Baibulo. Ndakhala ndikufuna kudziwa choonadi chenicheni ponena za Mulungu ndi Yesu, ndipo ndinganene moona mtima kuti ndikupeza mayankho olondola kudzera m’mabuku amenewa ndi m’Baibulo.” Zimenezo n’zimene mwamuna wina analembera likulu la Mboni za Yehova. M’kalata yomweyo, anapempha phunziro la Baibulo.

2 Monga mwamuna ameneyo, mamiliyoni a anthu padziko lonse amayamikira mabuku othandiza kuphunzira Baibulo amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatipatsa. (Mat. 24:45) Chaka chilichonse, mabuku ambiri akupangidwa kuti athandize anthu oona mtima ‘kufika pozindikira choonadi.’ (1 Tim. 2:4) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mwanzeru mabuku athu ofotokoza Baibulo?

3. Kodi tingapewe bwanji kuwononga mabuku?

3 Pewani Kuwononga: Patapita nthawi, tingakhale ndi mabuku ambiri amene sitingathe kugwiritsa ntchito. Kodi tingatani kuti tipewe kuwononga zofalitsa zathu zamtengo wapatali zimenezi? Tifunika kukhala ozindikira tikamatenga mabuku olowa nawo mu utumiki. M’malo motenga mabuku ambiri kuti tikagawire, tingangotenga limodzi kapena awiri ndipo tingakatengenso owonjezera ngati tagawira amene tinatenga aja. Zimenezi zidzatithandiza kupewa kuunjikana kwa mabuku ambiri m’nyumba mwathu. Mofananamo, ngati tili ndi magazini ambiri amene sitinagawire, ndi bwino kuchepetsa chiwerengero cha magazini amene timaoda.

4. Kodi tingatani ngati mpingo uli ndi zofalitsa zambiri zomwe sungathe kugwiritsa ntchito?

4 Mabuku Amene Aunjikana: Ngati mpingo uli ndi zofalitsa zina zambiri kuposa zimene angagwiritse ntchito, mlembi angafunse mipingo yoyandikana nayo m’deralo kuti adziwe ngati mipingo inayo ingawafune mabuku otsalawo. Ofalitsa angagawire mabuku akale kwa apabanja lawo amene si Mboni, ophunzira Baibulo, ndi enanso. Atsopano amene angoyamba kugwirizana ndi mpingo angakonde kukhala ndi mabuku akale pa laibulale yawo.

5. Kodi tingasonyeze motani kuti timayamikira mabuku athu?

5 Timafuna kuti mabuku athu azikwaniritsa cholinga chake chofuna kuthandiza anthu oona mtima kuti aphunzire zambiri zokhudza zolinga za Yehova. Monga Yesu yemwe sanataye chakudya chotsala atadyetsa khamu la anthu mozizwitsa, cholinga chathu chikhale kugwiritsa ntchito bwino mabuku athu amtengo wapatali ofotokoza Baibulo amene timalandira. (Yoh. 6:11-13) Uthenga wopatsa moyo umene umapezeka m’zofalitsa zathu, sungafike pa mtima wa anthu ofuna chilungamo ngati timangounjika mabukuwo pa mashelefu kapena m’zikwama mwathu. Choncho, tiyenera kukhala oganiza bwino potenga mabuku opita nawo mu utumiki ndi kuwagwiritsa ntchito mwanzeru kuti tipindulitse anthu ena.—Afil. 4:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena