Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/03 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Woyang’anira Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Mabuku Athu Ofotokoza Baibulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Bokosi La Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 7/03 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi woyang’anira utumiki angayang’anire bwanji ntchito ya atumiki otumikira amene amasamalira mabuku ndi magazini?

Ntchito ya woyang’anira utumiki sikungoyendera magulu a maphunziro a buku pamapeto pa mwezi uliwonse ndi kukonza misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda mokhazikika ayi. Mkulu wachangu ameneyu amakhala ndi chidwi ndi chilichonse chimene chingakhudze ntchito yolalikira m’gawo la mpingo. Iye amaonetsetsa kuti mwezi uliwonse pali mabuku ogwiritsa ntchito polalikira ndi magazini okwanira ndiponso kuti mabuku ameneŵa ndi osamalika bwino. Kuti achite zimenezi, amayang’anira ntchito zosiyanasiyana za atumiki otumikira amene amasamalira mabuku ndi magazini.

Woyang’anira utumiki amayang’anitsitsa zilengezo za mabuku odzagaŵira miyezi ya m’tsogolo zikatuluka mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Iye ndi mbale wosamalira mabuku amagwirira ntchito limodzi kuti aonetsetse kuti padzakhala mabuku okwanira ogwiritsa ntchito, koma ayenera kusamala kuti asaitanitse mabuku ochuluka kwambiri. Ngati buku lidzagwiritsidwa ntchito koyamba m’munda kapena ngati lidzaphunziridwa mu mpingo posachedwa, muyenera kukumbukira zimenezi mukamaitanitsa mabuku ku ofesi ya nthambi. Ngati bukulo linagaŵiridwapo kale, lipoti la utumiki wakumunda la mpingo la mwezi womaliza umene munagaŵira bukulo lidzasonyeza ngati mabuku amene muli nawo panopa ali okwanira. Inde, muyenera kuganizira chiŵerengero cha ofalitsa amene adzachite upainiya wothandiza mwezi umenewo komanso mmene ofalitsa ndi apainiya okhazikika awonjezekera kuchokera panthaŵi yomaliza imene munagaŵira bukulo. Anthu azitha kutenga mabuku musanayambe misonkhano komanso mukamaliza. Makatoni a mabuku ayenera kusungidwa bwino pa malo aukhondo ndiponso ouma ndipo muziwasanjikiza bwino kuti asaonongeke.

Woyang’anira utumiki azigwiranso ntchito pamodzi ndi mbale amene amasamalira magazini. Nthaŵi ndi nthaŵi, woyang’anira utumiki ndi mbale amene amasamalira magazini aziyerekezera chiŵerengero cha magazini amene amaitanitsa mwezi uliwonse ndi chiŵerengero cha magazini amene amagaŵiridwadi mu utumiki. Ofalitsa ena angafunike kuchepetsa magazini amene amaitanitsa ngati nthaŵi ndi nthaŵi magazini amangounjikana m’nyumba zawo. Magazini asamaonongedwe.

Potsatira mfundo zimenezi, woyang’anira utumiki aziona yekha chiŵerengero cha mabuku ofunika kugwiritsa ntchito amene mpingo ukuitanitsa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Akatero apereke fomuyo kwa mlembi wa mpingo, amene adzaifufuza mosamalitsa fomu yonseyo, n’kuonetsetsa chiŵerengero cha zinthu za oda yapadera zimene akufuna kuitanitsa.

Zoonadi, kuti tisamalire mabuku ndi magazini pamakhala zinthu zambiri zofunika kulemba. Ngati abale amene amasamalira zimenezi ali ndi mafunso okhudza mmene angagwiritsire ntchito mafomu ndiponso okhudza kusunga bwino zimene amalemba, mlembi adzakhala wosangalala kuwathandiza ntchito yawoyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena