MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzipereka Mphatso kwa Yehova”
Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ‘okonzeka kupereka mphatso kwa Yehova’? (1 Mbiri 29:5, 9, 14) M’munsimu muli njira zimene tingasankhe kuti tipereke ndalama zathu pothandiza ntchito ya Mboni za Yehova ya padziko lonse.
NDALAMA ZIMENE TIMAPEREKA PA INTANETI KAPENA M’MABOKOSI A ZOPEREKA ZIMATHANDIZA:
NTCHITO YA PADZIKO LONSE
kumanga komanso kuyendetsa ntchito za m’maofesi a nthambi ndi maofesi omasulira mabuku
sukulu zophunzitsa atumiki a Mulungu
atumiki apadera a nthawi zonse
kuthandiza anthu m’nthawi ya mavuto
kusindikiza mabuku, kukonza mavidiyo komanso za pa intaneti
KULIPILIRA ZINTHU ZOFUNIKA PAMPINGO
ndalama zolipirira madzi, magetsi komanso kukonza zimene zaonongeka pa Nyumba ya Ufumu
ndalama zimene mpingo wavomereza kupereka ku ofesi ya nthambi kuti zikathandize:
kumangira Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano padziko lonse
zopereka za padziko lonse zothandiza pakachitika tsoka
ntchito zina za padziko lonse
MISONKHANO YACHIGAWO KOMANSO YADERA
Zopereka za pa misonkhano yachigawo zimaperekedwa ku ntchito ya padziko lonse. Ndalama zimene zagwiritsidwa pa misonkhano yachigawo, yapadera komanso ya mayiko zimachokera ku thumba la ntchito ya padziko lonse.
Zopereka zothandiza misonkhano yadera zimagwiritsidwa ntchito polipirira lendi, kugula zinthu zofunika komanso kukonza zowonongeka kapenanso kulipirira zinthu zina zofunika m’dera. Dera lingathenso kusankha kuti ndalama zina ziperekedwe ku thumba la ntchito ya padziko lonse ya Mboni za Yehova.