Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w18 November tsamba 32
  • Kodi Ndingapereke Chiyani kwa Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingapereke Chiyani kwa Yehova?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Nkhani Yofanana
  • “Muzipereka Mphatso kwa Yehova”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • ‘Timakobidi Tiwiri Tating’ono’ Tamtengo Wapatali
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Kodi Ndalama Zoyendetsera Ntchito ya a Mboni za Yehova Zimachokera Kuti?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
w18 November tsamba 32
donate.jw.org

Kodi Ndingapereke Chiyani Kwa Yehova?

PA NTHAWI ina Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pa nkhani ya ubwenzi wathu ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Yehova watipatsa mphatso zambirimbiri zomwe zimatithandiza kukhala osangalala. Koma tikhoza kusangalala kwambiri tikamapereka mphatso kwa Yehova. Kodi ndi mphatso ziti zimene tingapereke kwa Yehova? Lemba la Miyambo 3:9 limanena kuti: “Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.” Mawu oti ‘zinthu zamtengo wapatali’ angatanthauze zinthu monga nthawi, luso, mphamvu komanso chuma chathu. Tikamagwiritsa ntchito zinthu zimenezi kuti zithandizire pa kulambira Mulungu, timakhala tikupereka mphatso kwa Yehova ndipo timasangalala kwambiri.

Kodi tingatani kuti tisamaiwale kupereka chuma chathu kwa Yehova? Mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Korinto kuti “aziika kenakake pambali” koti adzapereke kwa Yehova. (1 Akor. 16:2) Ndiye kodi mungadziwe bwanji njira zimene mungaperekere? Onani bokosi lotsatirali.

Kupereka kudzera pa intaneti ndi kosatheka m’mayiko ena. Koma malangizo okhudza kupereka m’njira zina amapezeka pa jw.org. M’mayiko ena, amaikaponso mayankho a mafunso amene anthu amadzifunsa okhudza zopereka.

Njira Yosavuta Yoperekera Ndalama pa Intaneti

N’ZOSAVUTA KUPEZA

  • Pofufuzira pa intaneti

    Lembani donate.jw.org pofufuza pa intaneti

  • JW Library

    Patsamba loyamba la JW Library®, dinani palinki ya “Donations”

N’ZOSAVUTA KUPEREKA

Mukhoza kupereka kamodzi kokha kapena kukonza zoti muzipereka mobwerezabwereza:

  • Ntchito ya Padziko Lonse

  • Mpingo Wanu

  • Msonkhano Wachigawo

  • Msonkhano Wadera

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena