Phunziro Labuku Lampingo Limachirikiza Zochita Zophunzitsa
1 Phunziro Labuku Lampingo limachita mbali yofunika m’programu ya kuphunzitsa ya gulu la Yehova. Timagulu ta phunziro labuku timamwazikana m’gawo lonselo, kukuchititsa kukhala kosavuta kwa onse kufikapo. Pokhala ndi malo apakati a phunzirolo pafupi nawo, anthu okondwerera angavomere mosavuta chiitano cha kufikapo.
2 Kuyesayesa kuyenera kuchitidwa kuti kagulu kalikonse kakhale kakang’ono. Zimenezi zimalola wochititsa kupereka chithandizo chaumwini kwa mmodzi ndi mmodzi. Sionse amene amaphunzira pa mlingo wofanana. Ngati aliyense ali ndi vuto la kumvetsetsa mfundo inayake ngakhale pambuyo pophunzira phunzirolo pasadakhale, wochititsa angaifotokozenso pambuyo pa phunzirolo. Ndiponso, ndi kagulu kakang’ono, pamakhala mipata yochuluka ya kuyankhapo ndi kugaŵanamo m’kuŵerenga malemba. Kodi mumachirikiza makambitsiranowo mwa kuyankhapo nthaŵi zonse? Kodi mumayesa kuyankha m’mawu anuanu? Kukhala kwanu wokonzekera kutengamo mbali kungakhale kopindulitsa kwa inuyo ndi ena. Pamene mukukonzekera, gwiritsirani ntchito mphamvu zanu za kulingalira kudziŵa mmene mungagwiritsirire ntchito mfundo zakutizakuti za m’phunzirolo.—Aheb. 5:14.
3 Mwa kupenyetsetsa njira zophunzitsira za wochititsa phunziro labuku, mungaphunzire mmene mungachititsire maphunziro a Baibulo apanyumba mwa njira yokondweretsa ndi yophunzitsa. Ndime zitaŵerengedwa ndi mbale woyeneretsedwa, mafunso amafunsidwa. Wochititsa phunziro amalimbikitsa onse kulankhula momveka. Pamene nthaŵi ilola, amayesa kuitanitsa ndemanga pa malemba osonyezedwa kuti atithandize mmene amagwirira ntchito. (Yerekezerani ndi Nehemiya 8:8.) Nthaŵi zina angaphatikizepo ndemanga yakeyake yachidule kapena kugwiritsira ntchito mafunso othandiza kuti amveketse mfundo yaikulu. Chitsanzo kapena chithunzithunzi chingatithandize kuona mmene nkhaniyo imakhudzira miyoyo yathu.
4 Chiŵerengero cha opezeka pa Maphunziro Abuku Ampingo ena chimakhala chotsika. Kodi mumapezekapo mokhazikika? Ngati simumatero, mwakhala mukuphonya chogaŵiridwa chofunika kwambiri. Makonzedwe a phunziro labuku ali imodzi ya njira zimene Yehova amasonyezera chisamaliro chake kwa ife. (1 Pet. 5:7) Iye amafuna kuti tipite patsogolo m’chidziŵitso ndi nzeru kotero kuti tikhale olimba mwauzimu. Kumbali ina, Satana amafuna kubweza m’mbuyo kukula kwathu kwauzimu ndi kutifooketsa kuti tisakhale ogwiritsiridwa ntchito kwambiri ndi Yehova ndi gulu Lake. Musalole zimenezi kuchitika! Lolani kuti mkhalidwe wabwino ndi wachikondi umene uli m’gulu logwirizana limeneli ukhudze mtima wanu ndi kukusonkhezerani kupitiriza kutamanda Yehova.—Yerekezerani ndi Salmo 111:1.
5 Misonkhano yokonzekera utumiki yapafupi ndi ofalitsa imalinganizidwa pamalo ambiri a phunziro labuku. Imeneyi ingakhale pakati pa mlungu, kumapeto kwa mlungu, kapena ulaliki wa madzulo. Wochititsa phunziro labuku amatsimikizira kuti gawo lokwanira lilipo ndi kuti padzakhala munthu wina wotsogolera m’munda. Misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda iyenera kutenga mphindi 10-15. Wochititsayo angapende lemba latsiku mwachidule ngati likukhudza ntchito yathu yolalikira ndiyeno kupereka lingaliro lachindunji la utumiki wakumunda limodzi kapena aŵiri kapena kusonyeza chitsanzo chachidule cha chogaŵira cha panthaŵiyo.
6 Wochititsayo amayesayesa m’kupita kwa nthaŵi kugwira ntchito ndi aliyense wa m’kagulu kake, akumapereka chilimbikitso choyenera ndi chilangizo.—Yerekezerani ndi Marko 3:14; Luka 8:1.