Chifukwa Chake Phunziro la Buku la Mpingo N’lofunika
1. Kodi Phunziro la Buku la Mpingo linayamba bwanji?
1 M’chaka cha 1895, magulu a maphunziro a Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova nthaŵi imeneyo, ankatchedwa Magulu a Dawn Ophunzirira Baibulo. Anali kugwiritsa ntchito mabuku a Millennial Dawn monga mabuku ophunzirira. Patapita nthaŵi, misonkhano imeneyi anali kuitcha Magulu a Abereya Ophunzira Baibulo. (Mac. 17:11) Nthaŵi zambiri gulu la anthu ocheperapo linkakumana m’nyumba madzulo patsiku limene linali labwino kwa anthu a m’gululo. Misonkhano imeneyi ndi pamene panayambira Phunziro la Buku la Mpingo.
2. Kodi ‘tingatonthozane’ bwanji paphunziro la buku?
2 Kulimbikitsana ndi Kuthandizana: Popeza magulu a maphunziro a buku amawakonza kuti azikhala ochepa, pamakhala mpata waukulu kwa anthu amene apezekapowo kufotokoza chikhulupiriro chawo. Zotsatira zake n’zoti pamakhala ‘kutonthozana pamodzi, mwa chikhulupiriro cha onse.’—Aroma 1:12.
3, 4. Kodi phunziro la buku limatithandiza bwanji kukwaniritsa utumiki wathu?
3 Kuonetsetsa mmene woyang’anira phunziro la buku amaphunzitsira kungatithandize ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Tim. 2:15) Onani mmene akutsindikira Malemba amene nkhaniyo yazikidwapo. Ngati n’koyenera malinga ndi buku limene mukuphunzira, angatsindike mfundo zazikulu mwa kubwereza pogwiritsa ntchito Baibulo lokha. Chitsanzo chake chabwino chingatithandize kupititsa patsogolo kaphunzitsidwe kathu mu utumiki wachikristu.—1 Akor. 11:1.
4 Kuwonjezera pa kuchititsa phunziro mlungu ndi mlungu, woyang’anira phunziro la buku amatsogolera pantchito yolalikira. Mogwirizana ndi woyang’anira utumiki, amakonza dongosolo labwino loloŵa mu utumiki wa kumunda. Amafuna kuthandiza anthu onse a m’gulu lake kukwaniritsa udindo wawo wachikristu wolalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa anthu.—Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 9:16.
5. Kodi munthu aliyense payekha amathandizidwa motani kudzera m’phunziro la buku?
5 Woyang’anira phunziro la buku amaganizira za moyo wauzimu wa munthu aliyense m’gululo. Amasonyeza kuganizira kumeneku pa misonkhano ya mpingo ndiponso pamene akugwira ntchito pamodzi ndi ena mu utumiki wa kumunda. Nthaŵi imene amachezera abale ku nyumba zawo amaigwiritsanso ntchito kuwapatsa mtulo wauzimu. Onse ayenera kuona kuti ndi omasuka kulankhula ndi woyang’anira phunziro la buku kuti awathandize mwauzimu nthaŵi iliyonse imene afuna thandizo.—Yes. 32:1, 2.
6. (a) Kodi abale athu m’mayiko ena alimbikitsidwa motani mwa kusonkhana m’magulu aang’ono? (b)Kodi inu panokha mwapindula bwanji ndi phunziro la buku?
6 Limbikitsanani: M’mayiko amene ntchito ya anthu a Mulungu imaponderezedwa, abale nthaŵi zambiri amakumana m’magulu ocheperapo. Mbale wina pokumbukira ananena kuti: “Ngakhale kuti ntchito yathu yachikristu inaletsedwa, timati tikapeza mpata tinkachita misonkhano ya mlungu ndi mlungu m’magulu a anthu okwana 10 kapena 15. Pamisonkhanoyo tinkapeza mphamvu mwauzimu chifukwa cha kuphunzira Baibuloko ndiponso kucheza kwathu tikamaliza phunziro. Tinkamva zimene aliyense anali kukumana nazo, ndipo zimenezi zinatithandiza kuzindikira kuti tonse tinali kukumana ndi mavuto ofanana.” (1 Pet. 5:9) Tiyeni nafenso tizilimbikitsana mwa kuchirikiza ndi mtima wonse Phunziro la Buku la Mpingo.—Aef. 4:16.