Thandizani Woyang’anira Phunziro Lanu la Buku la Mpingo
1 Tonse timapindula kwambiri ndi Phunziro la Buku la Mpingo. Mwezi watha, tinakambirana njira zimene woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo amakwaniritsira ntchito yake. Koma kodi tingatani kuti tim’thandize ntchito imene amagwira kotero kuti ife ndi anthu ena tipindule?
2 Pezekanipo Mlungu Uliwonse: Chifukwa chakuti magulu a phunziro la buku amakhala ndi anthu ochepa, zimathandiza kwambiri mukapezekapo. Chikhale cholinga chanu kupezekapo mlungu uliwonse. Mungathandizenso mwa kufika nthaŵi yabwino, chifukwa zimenezi zimathandiza woyang’anira kuyamba msonkhanowo moyenera.—1 Akor. 14:40.
3 Mayankho Olimbikitsa: Njira ina imene mungathandizire ndiyo kukonzekera bwino ndi kukayankha zolimbikitsa. Kaŵirikaŵiri mayankho amene amakhala ndi mfundo imodzi amakhala abwino, ndipo izi zimalimbikitsanso ena kuyankha. Peŵani kuyankha ndime yonse. Ngati mfundo ina pa ndimeyo yakukhudzani mtima, pangitsani makambiranowo kukhala osangalatsa mwa kunena mfundo yanuyo.—1 Pet. 4:10.
4 Ngati muli ndi mwayi woŵerenga ndime pa phunzirolo kuti gulu lonse lipindule, yesetsani kukwaniritsa mbali yanuyo. Kuŵerenga bwino kumathandiza kuti phunzirolo likhale labwino kwambiri ndiponso losangalatsa.—1 Tim. 4:13.
5 Umboni wa Kagulu: Misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda imachitikira m’malo ambiri a phunziro la buku, ndipo kupezekapo kwanu pamisonkhano imeneyi kumathandiza woyang’anira potsogolera ntchito yolalikira. Onani misonkhano imeneyi kukhala mpata wodziŵana bwino ndi abale anu ndiponso wowalimbikitsa.
6 Malipoti a Utumiki Wakumunda: Kupereka malipoti anu a utumiki wakumunda mwamsanga kumapeto a mwezi uliwonse, ndi njira inanso imene mungathandizire woyang’anira. Mungam’patse pamanja malipoti anuwo kapena mungaike m’bokosi loikamo malipoti a utumiki wakumunda pa Nyumba ya Ufumu. Mlembi angatengenso m’bokosi limeneli malipoti a utumiki wakumunda amene oyang’anira maphunziro a buku anasonkhanitsa.
7 Anthu amayamikira ntchito imene mumagwira pothandiza woyang’anira Phunziro lanu la Buku la Mpingo. Koposa zonse, khalani ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ‘adzakhala ndi mzimu wanu.’—Afil. 4:23.