Njira Zimene Oyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo Amasonyezera Kuganizira Ena
1 Phunziro la Buku la Mpingo linapangidwa kuti ‘kuzikhala kotheka kupereka chisamaliro chachikulu pa munthu mmodzi ndi mmodzi. . . . Zimenezi zimaonetsa kukoma mtima kwapadera kwa Yehova ndi chisamaliro chake chachikondi kwa anthu ake.’ (om-CN tsa. 75; Yes. 40:11) Woyang’anira phunziro la buku amagwira ntchito yofunika kwambiri yosamalira anthu imeneyi.
2 Pa Phunziro la Buku: Popeza magulu onse a phunziro la buku amaikako dala anthu ochepa, woyang’anira phunzirolo amatha kuwadziŵa bwino anthu a m’gulu lake. (Miy. 27:23) Nthaŵi zambiri mlungu uliwonse pamapezeka mpata wocheza phunziro lisanayambe kapena likatha. Mwezi ukamatha, zingatheke kuti acheze pafupifupi ndi anthu onse a m’gulu lakelo. Izi zimathandiza anthu a ku phunziro la bukulo kukhala omasuka kulankhula naye akapeza mavuto kapena akafuna kulimbikitsidwa.—Yes. 32:2.
3 Woyang’anira phunziro la buku amayesetsa kulimbikitsa anthu onse a m’gulu lake kuti aziyankha pa phunzirolo. Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndiyo mwa kuchititsa phunziro mokoma mtima ndiponso mwachifatse. (1 Ates. 2:7, 8) Amafufuza njira zimene angaphatikizire onse ndi ana omwe, pokambiranapo. Ngati ena amachita manyazi kuyankha, angawathandize paokha mwa kuwakonzekeretsa kuti adzaŵerenge lemba kapena adzayankhe pandime ina yake. Kapena angawasonyeze momwe angamayankhire m’mawu awoawo.
4 Ngati wothandiza wa woyang’anira phunziro la buku ndi mtumiki wotumikira, woyang’anirayo azikonza zoti mtumikiyo azichititsa phunzirolo kamodzi pakatha miyezi iŵiri iliyonse. Izi zizipangitsa woyang’anirayo kuona mmene wothandiza wakeyo akuchitira ndi kum’thandiza mbali zina. Imeneyitu ndi njira yabwino kwambiri yothandizira abale kuwonjezera luso lawo la kuphunzitsa!—Tito 1:9.
5 Mu Utumiki Wakumunda: Ntchito ina yaikulu ya woyang’anira phunziro la buku ndiyo kutsogolera ntchito yolalikira. (Num. 27:16, 17) Amakonza dongosolo labwino lakuti azichita umboni wa kagulu ndipo amayesetsa kuthandiza onse m’kaguluko kusangalala ndi utumiki wawo. (Aef. 4:11, 12) Kuti zimenezi zitheke, chimakhala cholinga chake kuyenda mu utumiki ndi aliyense wa m’kagulu kake. Amathandizananso ndi woyang’anira utumiki kuona kuti amene akufuna kumachita bwino m’mbali zina za utumiki wawo athandizidwe ndi ofalitsa odziŵa kwambiri.
6 Monga Abusa Achikondi: Woyang’anira phunziro la buku amaganizira anthu amene amachita zochepa mu ntchito yolalikira chifukwa cha mavuto ena. Amaonetsetsa kuti anthu amene amatero chifukwa cha ukalamba kapena amangokhala pakhomo chifukwa cha matenda komanso amene asiya kuchita zochuluka kwa kanthaŵi chabe chifukwa chodwala kwambiri kapena kuvulala, akudziŵa za dongosolo lakuti akhoza kumapereka mphindi 15 zilizonse za mu utumiki wakumunda ngati sangathe kukwanitsa ola limodzi pamwezi. (Komiti ya Utumiki ya Mpingo ndi imene imaona kuti ndi ndani akuyenera zimenezi.) Amaganiziranso anthu a m’gulu lake amene anasiya kuloŵa m’munda, amayesetsa kuwathandiza kuti ayambirenso kugwira ntchito ndi mpingo.—Luka 15:4-7.
7 Tikuyamikira kwambiri chikondi chimene oyang’anira maphunziro a buku amasonyeza. Kuganizira kwawo anthu kumathandiza kuti ‘ife tonse tifikire ku umodzi wa chikhulupiriro . . . , ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu.’—Aef. 4:13.