Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 29, 2012. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.
1. Kodi guwa lansembe limene Ezekieli anaona m’masomphenya likuimira chiyani? (Ezek. 43:13-20) [Sept. 10, w07 8/1 tsa. 10 ndime 4]
2. Kodi madzi a mumtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya akuimira chiyani? (Ezek. 47:1-5) [Sept. 17, w07 8/1 tsa. 11 ndime 2]
3. Kodi mawu akuti “anatsimikiza mumtima mwake” akusonyeza chiyani za mmene Danieli anaphunzitsidwira ali wachinyamata? (Dan. 1:8) [Sept. 24, dp tsa. 33-34 ndime 7-9; tsa. 36 ndime 16]
4. Kodi mtengo waukulu womwe Nebukadinezara analota unkaimira chiyani? (Dan. 4:10, 11, 20-22) [Oct. 1, w07 9/1 tsa. 18 ndime 5]
5. Kodi lemba la Danieli 9:17-19 limatiphunzitsa chiyani pa nkhani ya pemphero? [Oct. 8, w07 9/1 tsa. 20 ndime 5-6]
6. Kodi ndi pangano liti limene ‘anasungira anthu ambiri’ mpaka kumapeto kwa mlungu wa 70 wa milungu ya zaka, kapena kuti mu 36 C.E.? (Dan. 9:27) [Oct. 8, w07 9/1 tsa. 20 ndime 4]
7. Kodi zimene mngelo anauza Danieli zakuti “kalonga wa ufumu wa Perisiya” anamutsekereza zikusonyeza chiyani? (Dan. 10:13) [Oct. 15, w11 9/1 tsa. 8 ndime 1-2]
8. Kodi ndi ulosi uti wa m’Baibulo wonena za Mesiya umene unakwaniritsidwa mogwirizana ndi zimene lemba la Danieli 11:20 limanena? [Oct. 15, dp tsa. 232 ndime 5-6]
9. Malinga ndi Hoseya 4:11, kodi pangakhale vuto lotani ngati munthu akumwa mowa mwauchidakwa? [Oct. 22, w10 1/1 mas. 4-5]
10. Kodi tingaphunzire mfundo yotani pa Hoseya 6:6? [Oct. 22, w07 9/15 tsa. 16 ndime 8; w05 11/15 tsa. 24 ndime 11-12]