Ndandanda ya Mlungu wa October 29
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 29
Nyimbo Na. 125 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 14 ndime 6-10 ndi bokosi patsamba 110 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Hoseya 8-14 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: “Zimene Mungachite Kuti Muzipindula ndi Kagulu Kanu ka Utumiki.” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana bokosi la patsamba 6, funsani mwachidule munthu amene msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda umachitikira panyumba yake. Kodi amachita chiyani kuti pokonzekera msonkhano umenewu mlungu uliwonse? N’chifukwa chiyani amayamikira mwayi umene ali nawo, woti msonkhanowu umachitikira pakhomo lake?
Mph. 15: “Njira Zisanu Zopezera Phunziro la Baibulo.” Mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime 6, funsani abale ndi alongo amene anachititsapo phunziro la Baibulo lopita patsogolo kuti afotokoze mwachidule madalitso amene anapeza.
Nyimbo Na. 122 ndi Pemphero